NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) May 2016

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira June 27 mpaka pa July 31, 2016.

Kodi Mumathetsa Nkhani Mwachikondi Mukasemphana Maganizo?

Kodi cholinga pokambirana chizikhala kuwina mkangano, kuchititsa munthu kuvomereza kuti walakwa kapena chiyani?

“Pitani Mukaphunzitse Anthu a Mitundu Yonse”

Mayankho a mafunso 4 akusonyeza amene akukwaniritsa ulosi wa Yesu masiku ano.

Kodi Mumasankha Bwanji Zochita?

Kodi mungasankhe bwanji zochita pa nkhani zimene m’Baibulo mulibe malamulo ake?

Kodi Baibulo Likusinthabe Moyo Wanu?

Munthu wina anasiya kutchova juga, kusuta, kuledzera komanso kumwa mankhwala osokoneza ubongo ndipo anabatizidwa, koma zinkamuvutabe kusintha timakhalidwe tina.

Kodi Zinthu Zonse Zimene Yehova Amatipatsa Zimakuthandizani?

Kodi n’chiyani chingatilepheretse kuti tizipindula kwambiri ndi zinthu zonse zimene Yehova watipatsa?

KALE LATHU

“Kwa Amene Apatsidwa Ntchitoyi”

Msonkhano womwe unachitika mu 1919 unali chiyambi cha ntchito yolalikira imene zotsatira zake zinafalikira padziko lonse.

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Mkhristu angadziwe bwanji ngati n’zoyenera kupereka ndalama kwa ogwira ntchito m’boma? Kodi tingasonyeze bwanji kusangalala tikamva chilengezo choti munthu wina wabwezeretsedwa? Kodi n’chiyani chinkachititsa kuti madzi apadziwe la Betesida ‘aziwinduka’?