Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizipereka Ulemu kwa Oyenera Kulemekezedwa

Tizipereka Ulemu kwa Oyenera Kulemekezedwa

“Iye wokhala pampando wachifumu, ndi Mwanawankhosa, atamandidwe ndiponso alandire ulemu, ulemerero, ndi mphamvu, kwamuyaya.”CHIV. 5:13.

NYIMBO: 9, 108

1. N’chifukwa chiyani anthu ena amafunika kulemekezedwa, nanga tikambirana funso liti?

KUPEREKA ulemu kwa munthu kumatanthauza kuchita zinthu zosonyeza kuti timamulemekeza. Nthawi zambiri munthu woyenera kulemekezedwayo amakhala kuti wachita zinazake kapena ali ndi udindo winawake. Ndiye tingafunse kuti, kodi tiyenera kupereka ulemu kwa ndani, ndipo n’chifukwa chiyani?

2, 3. (a) N’chifukwa chiyani Yehova ndi woyenera kupatsidwa ulemu? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) Kodi Mwanawankhosa wotchulidwa pa Chivumbulutso 5:13 ndi ndani, ndipo n’chifukwa chiyani ali woyenera kupatsidwa ulemu?

2 Lemba la Chivumbulutso 5:13 limasonyeza kuti ‘wokhala pampando wachifumu ndiponso Mwanawankhosa’ ayenera kulemekezedwa. Chaputala 4 cha buku lomweli chimafotokoza chifukwa chake Yehova ali woyenera kupatsidwa ulemu. Angelo amatamanda mokweza Yehova “amene adzakhalabe ndi moyo kwamuyaya.” Iwo amati: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga  zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.”Chiv. 4:9, 11.

3 Mwanawankhosa ndi Yesu Khristu ndipo iye ndi “amene akuchotsa uchimo wa dziko.” (Yoh. 1:29) Baibulo limasonyeza kuti Yesu ndi wapamwamba kuposa mafumu onse. Limati iye ndi “Mfumu ya olamulira monga mafumu ndi Mbuye wa olamulira monga ambuye, adzaonekera pa nthawi zake zoikidwiratu. Iye yekha ndiye amene ali ndi moyo wosakhoza kufa, amene amakhala m’kuwala kosafikirika. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene anamuonapo kapena amene angamuone.” (1 Tim. 6:14-16) Angelo amalengeza kuti: “Mwanawankhosa amene anaphedwa ndiye woyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero, ndi madalitso.” (Chiv. 5:12) Kodi pali mfumu iliyonse imene inalolera kufa chifukwa chofuna kupulumutsa anthu ake? Kuganizira zimene Yesu anachitazi kungatilimbikitse kuti nafenso tizimulemekeza.

4. N’chifukwa chiyani kulemekeza Yehova ndi Yesu si nkhani yochita kusankha?

4 Kulemekeza Yehova ndi Khristu si nkhani yochita kusankha. Kuti tidzapeze moyo wosatha tiyenera kuchita zimenezi basi. Mawu a Yesu a pa Yohane 5:22, 23 amatithandiza kumvetsa bwino mfundo imeneyi. Iye anati: “Atate saweruza munthu aliyense, koma wapereka udindo wonse woweruza kwa Mwana, kuti onse alemekeze Mwana monga mmene amalemekezera Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamutuma.”Werengani Salimo 2:11, 12.

5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu amafunika kupatsidwa ulemu?

5 Anthufe tinalengedwa “m’chifaniziro cha Mulungu.” (Gen. 1:27) N’chifukwa chake anthu ambiri amasonyeza makhalidwe a Mulungu. Mwachitsanzo, anthu amatha kusonyezana chikondi, kukoma mtima komanso chifundo. Popeza anthu analengedwa ndi chikumbumtima, amatha kusiyanitsa zoyenera ndi zosayenera, zachilungamo ndi zachinyengo ndiponso zabwino ndi zoipa. (Aroma 2:14, 15) Komanso anthu ambiri amasangalala ndi zinthu zaukhondo ndiponso zokongola. Anthufe timafunanso kukhala mwamtendere ndi ena. Choncho, kaya modziwa kapena mosadziwa, anthu amasonyeza ulemerero wa Mulungu mwa njira inayake. Chifukwa cha zimenezi anthu ayenera kupatsidwa ulemu ngakhale kuti sungafanane ndi umene timapatsa Yehova kapena Yesu.Sal. 8:5.

TIZIDZIWA MALIRE PA NKHANI YOLEMEKEZA ENA

6, 7. Pa nkhani ya kulemekeza anthu, kodi a Mboni za Yehova amasiyana bwanji ndi anthu ena?

6 Koma pa nkhani yopereka ulemu kwa anthuyi tiyenera kudziwa zoyenera ndi zosayenera kuchita. N’zosavuta kwa anthu ochimwafe kuti tiyambe kutengera mzimu wa dziko la Satanali. N’chifukwa chake anthu ambiri, m’malo mopereka ulemu woyenera kwa munthu, amayamba kum’patsa ulemu wofanana ndi kumulambira. Amalemekeza kwambiri atsogoleri achipembedzo ndi andale, akatswiri amasewera ndi azisudzo komanso anthu ena otchuka ndipo amawaona kuti ndi apamwamba kwambiri kuposa ena. Choncho amafuna atakhala ngati iwowo ndipo amatsanzira khalidwe lawo, kavalidwe kawo komanso zochita zawo.

7 Koma Akhristu oona amapewa kupereka ulemu wosayenera kwa anthu. Khristu yekha ndi yemwe anali munthu wangwiro ndipo ndi amene tiyenera kumutsanzira. (1 Pet. 2:21)  Mulungu sangasangalale tikamapereka ulemu wonyanyira kwa anthu. Tiyenera kukumbukira mfundo yakuti: “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Choncho palibe munthu amene ayenera kupatsidwa ulemu wofanana ndi kumulambira.

8, 9. (a) Kodi a Mboni za Yehova amawaona bwanji akuluakulu a boma? (b) Kodi timamvera akuluakulu a boma pa zinthu ziti?

8 Pali anthu ena amene ali ndi maudindo m’dzikoli. Mwachitsanzo, akuluakulu a boma amasamalira nzika za dziko lawo komanso amathandiza kuti anthu azitsatira malamulo. Akamachita zimenezi anthu onse m’dzikolo amapindula. N’chifukwa chake mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti aziwaona kuti ndi “olamulira akuluakulu” ndipo aziwamvera. Analangizanso Akhristu kuti: “Perekani kwa onse zimene amafuna. Amene amafuna msonkho, m’patseni msonkho. . . . Amene amafuna kupatsidwa ulemu, m’patseni ulemu wake.”—Aroma 13:1, 7.

9 Choncho a Mboni za Yehova amatsatira malangizo amenewa ndipo amalemekeza akuluakulu a boma mogwirizana ndi chikhalidwe cha m’dziko limene akukhala. Timayesetsanso kuwamvera kuti azigwira bwino ntchito yawo. Komabe sikuti timawamvera kapena kuwalemekeza pa chilichonse. Mwachitsanzo, sitingawamvere ngati atiuza kuti tichite zinthu zosemphana ndi zimene Mulungu amafuna kapena zimene zingasonyeze kuti tikulowerera ndale.Werengani 1 Petulo 2:13-17.

10. Kodi atumiki a Yehova akale anasonyeza bwanji kuti ankalemekeza akuluakulu a boma?

10 Tingaphunzire zambiri pa zimene atumiki a Yehova ena akale anachita pa nkhani ya kumvera olamulira kapena akuluakulu a boma. Mwachitsanzo, boma la Roma litanena kuti anthu ake ayenera kulembetsa m’kaundula, Yosefe ndi Mariya anapita ku Betelehemu kukalembetsa. Iwo anachita zimenezi ngakhale kuti Mariya anali wotopa. (Luka 2:1-5) Nayenso Paulo akuimbidwa mlandu, anayankha mwaulemu ndipo ankalemekeza Mfumu Herode Agiripa ndi bwanamkubwa wa ku Yudeya dzina lake Fesito.Mac. 25:1-12; 26:1-3.

11, 12. (a) N’chifukwa chiyani timasiyanitsa ulemu umene timapereka kwa akuluakulu a boma ndi umene timapereka kwa atsogoleri achipembedzo? (b) Fotokozani zinthu zabwino zimene zinachitika m’bale wa ku Austria atasonyeza ulemu kwa munthu wina wandale.

11 Koma a Mboni za Yehova sapereka ulemu wapadera kwa atsogoleri achipembedzo ngakhale kuti atsogoleriwo amafuna ulemu. Zipembedzo zonyenga zimaphunzitsa mabodza okhudza Mulungu komanso zimapotoza Malemba. Choncho atsogoleri ake si ofunika kuwapatsa ulemu wapadera koma kungowalemekeza mmene timalemekezera anthu ena onse. Yesu ananena kuti atsogoleri achipembedzo a nthawi yake anali achinyengo komanso akhungu. (Mat. 23:23, 24) Koma kupereka ulemu woyenera kwa akuluakulu a boma n’kothandiza moti tikhoza kudabwa ndi zotsatira zake.

12 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina wa ku Austria. Iye anamangidwa ndi asilikali a Nazi n’kumutumiza pa sitima kundende ina. Musitimayo munalinso munthu wina wandale wotchuka amene anamangidwa chifukwa choti chipani cha Nazi chinayamba kudana naye. Pa ulendowu, m’baleyu anafotokozera wandaleyo mwaulemu mfundo zimene amakhulupirira. Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha, wandaleyu anagwiritsa ntchito udindo wake pothandiza a Mboni ku Austria. Mwina  inunso mukukumbukira zinthu zabwino zimene zinachitika chifukwa choti a Mboni anatsatira mfundo ya m’Baibulo yoti Akhristu azilemekeza akuluakulu a boma.

ANTHU ENA AMENE TIYENERA KUWALEMEKEZA

13. Kodi ndi anthu enanso ati amene tiyenera kuwalemekeza, ndipo n’chifukwa chiyani?

13 Anthu enanso oyenera kuwalemekeza ndi Akhristu anzathu. Ndipo tiyenera kulemekeza makamaka akulu amene amatitsogolera. (Werengani 1 Timoteyo 5:17.) Timawalemekeza mosatengera mtundu wawo, maphunziro awo, chuma chawo kapenanso kuti ndi otchuka kapena ayi. Baibulo limanena kuti akulu ndi “mphatso za amuna,” ndipo amagwira ntchito yaikulu posamalira anthu a Mulungu. (Aef. 4:8) Taganizirani ntchito imene akulu, oyang’anira dera, abale a m’Komiti ya Nthambi komanso a m’Bungwe Lolamulira amagwira. Abale ndi alongo a m’nthawi ya atumwi ankalemekeza kwambiri anthu amene Mulungu anawasankha kuti aziwatsogolera. Ifenso masiku ano timachita chimodzimodzi. Sikuti timawalemekeza mpaka kufika pokhala ngati tikuwalambira ndipo tikakumana nawo sitimakhala ngati takumana ndi angelo. Komabe timalemekeza abalewa chifukwa cha ntchito imene amagwira komanso kudzichepetsa kwawo.Werengani 2 Akorinto 1:24; Chivumbulutso 19:10.

14, 15. Kodi abusa achikhristu enieni amasiyana bwanji ndi atsogoleri azipembedzo?

14 Akulu amenewa amasonyeza kuti ndi abusa odzichepetsa. Umboni wa zimenezi ndi woti amakana kuti anthu aziwachitira zinthu ngati anthu otchuka. Choncho amasiyana ndi atsogoleri ambiri achipembedzo a masiku ano komanso a m’nthawi ya Yesu. Ponena za atsogoleri amenewo Yesu anati: “Amakonda malo olemekezeka kwambiri pa chakudya chamadzulo ndi mipando yakutsogolo m’masunagoge. Amakondanso kupatsidwa moni m’misika.”Mat. 23:6, 7.

15 Koma abusa achikhristu enieni amakhala odzichepetsa ndipo amamvera mawu a Yesu akuti: “Musamatchulidwe kuti Rabi, chifukwa mphunzitsi wanu ndi mmodzi yekha, ndipo nonsenu ndinu abale. Komanso musamatchule aliyense kuti atate wanu padziko lapansi pano, pakuti Atate wanu ndi mmodzi, wakumwamba Yekhayo. Musamatchedwe ‘atsogoleri,’ pakuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu. Koma wamkulu kwambiri pakati panu akhale mtumiki wanu. Aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, koma aliyense wodzichepetsa adzakwezedwa.” (Mat. 23:8-12) Popeza akulu amatsatira malangizo amenewa, n’chifukwa chake abale ndi alongo amawakonda komanso kuwalemekeza kwambiri.

Akulu akakhala odzichepetsa, abale ndi alongo amawakonda komanso kuwalemekeza kwambiri (Onani ndime 13 mpaka 15)

16. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tizitsatira zimene Baibulo limanena pa nkhani yolemekeza ena?

 16 N’zoona kuti zingatitengere nthawi kuti tidziwe bwinobwino zoyenera ndi zosayenera kuchita pa nkhani yolemekeza ena. Zoterezi zinkachitikanso m’nthawi ya atumwi. (Mac. 10:22-26; 3 Yoh. 9, 10) Komabe tiyenera kuyesetsa kuti tizitsatira zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi. Chifukwa tikamachita zinthu mosapitirira malire pa nkhani yolemekeza ena, pamakhala zotsatira zabwino.

KUPEREKA ULEMU WOYENERA N’KOTHANDIZA

17. Fotokozani zabwino zimene zinachitika chifukwa cholemekeza anthu audindo.

17 Tikamalemekeza anthu amene ali ndi udindo m’dzikoli, amatithandiza kuti tikhale ndi ufulu wogwira bwinobwino ntchito yathu yolalikira. Izi zimathandiza kuti anthu ambiri asamadane ndi ntchito yathu. Zaka zingapo zapitazo, mpainiya wina wa ku Germany dzina lake Birgit anapita kusukulu kwa mwana wake kukakhala nawo pamwambo wotsekera sukulu. Aphunzitsi anauza mlongoyu kuti amasangalala kukhala ndi ana a Mboni pasukuluyo. Iwo ananena kuti pasukulupo pakanakhala kuti panalibe ana a Mboni sizikanakhala bwino. Mlongoyu anawafotokozera kuti: “Timaphunzitsa ana athu kuti azitsatira mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. Ndipo mfundo ina ndi yoti ayenera kumalemekeza aphunzitsi awo.” Mphunzitsi wina anati: “Ana onse akanakhala ngati a Mboni, bwenzi ntchito yophunzitsa ikusangalatsa kwambiri.” Patadutsa milungu ingapo, mmodzi mwa aphunzitsiwo anapezeka pamsonkhano wachigawo womwe unachitikira mumzinda wina.

18, 19. N’chifukwa chiyani nkhani yopereka ulemu woyenera kwa akulu tiyenera kuiganizira bwinobwino?

18 Mfundo za m’Mawu a Mulungu zingatithandize kuti tizipereka ulemu woyenera kwa akulu. (Werengani Aheberi 13:7, 17.) Tiyenera kumawayamikira chifukwa cha ntchito yaikulu imene amagwira komanso tizitsatira malangizo omwe amatipatsa. Izi zingathandize kuti akuluwa azigwira ntchito yawo mosangalala. Koma kulemekeza akulu sikukutanthauza kuti tizitsanzira ndendende mmene amavalira, amametera, amakambira nkhani komanso mmene amalankhulira. Ngati tingachite zimenezi zingaoneke ngati timatsatira munthu. Tizikumbukira kuti munthu aliyense ndi wochimwa ndipo woyenera kumutsanzira ndi Khristu.

19 Komanso tikamapereka ulemu woyenera kwa akulu n’kumapewa kuwachitira zinthu ngati anthu otchuka, timawathandiza kwambiri. Izi zimawathandiza kuti asagwere mu msampha wonyada komanso wodziona ngati apamwamba ndiponso olungama.

20. Kodi kupereka ulemu woyenera kumatithandiza bwanji?

20 Kupereka ulemu kwa anthu oyenera kulemekezedwa kumatithandizanso ifeyo. Kumatithandiza kuti tisamadzikweze anthu ena akatilemekeza. Komanso kumatithandiza kuti tizigwirizana ndi gulu la Yehova limene limatilangiza kuti tisamalemekeze anthu monyanyira, kaya ndi a Mboni anzathu kapena ayi. Kupereka ulemu woyenera kwa anthu kumathandizanso kuti tisadzakhumudwe kwambiri munthu amene timam’patsa ulemuyo akadzachita zolakwika.

21. Tchulani phindu lalikulu limene timapeza tikamapereka ulemu woyenera?

21 Chofunika kwambiri n’chakuti tikamapereka ulemu woyenera, timalemekeza Mulungu. Timakhala kuti tikuchita zimene iye amafuna komanso timasonyeza kuti ndife okhulupirika. Zimenezi zimathandiza kuti ayankhe Satana, amene amamutonza. (Miy. 27:11) Ambiri m’dzikoli amapereka ulemu wonyanyira kwa anthu. Koma ifeyo tikuthokoza Yehova chifukwa amatiphunzitsa zoyenera kuchita pa nkhaniyi.