Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzikhulupirira Yehova Kuti Muzisankha Zochita Mwanzeru

Muzikhulupirira Yehova Kuti Muzisankha Zochita Mwanzeru

Azipempha ndi chikhulupiriro, osakayikira m’pang’ono pomwe.”—YAK. 1:6.

NYIMBO: 81, 70

1. N’chiyani chinalepheretsa Kaini kuti asankhe zochita mwanzeru, nanga zotsatira zake zinali zotani?

PA NTHAWI ina Kaini ankafunika kusankha zochita. Ankafunika kusankha kugonjetsa mkwiyo wake kapena kuulekerera. Zilizonse zimene akanasankha zikanakhudza moyo wake wonse. Koma tonse tikudziwa kuti Kaini sanasankhe bwino. Zimene anasankha zinaphetsa mng’ono wake Abele komanso zinachititsa kuti ubwenzi wake ndi Yehova usokonekere.—Gen. 4:3-16.

2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tizisankha zochita mwanzeru?

2 Ifenso timafunika kusankha zochita. N’zoona kuti zosankha zina sizikhala zazikulu. Koma zosankha zambiri zimakhudza kwambiri moyo wathu. Tikasankha zochita mwanzeru zinthu zimatiyendera bwino. Koma tikapanda kusankha bwino timakumana ndi mavuto.—Miy. 14:8.

3. (a) Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisankha zochita mwanzeru? (b) Kodi m’nkhaniyi tikambirana mafunso ati?

3 Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisankha zochita mwanzeru? Tiyenera kukhulupirira Mulungu ndipo tisamakayikire ngakhale pang’ono kuti angatithandize kuti  tisankhe zoyenera. Tizikhulupiriranso Mawu ake komanso tizidziwa kuti malangizo ake ndi odalirika. (Werengani Yakobo 1:5-8.) Ubwenzi wathu ndi Yehova ukamalimba komanso tikamakonda kwambiri Mawu ake timayamba kumudalira kwambiri podziwa kuti amatifunira zabwino. Zikatere, nthawi zonse timafufuza kaye m’Mawu ake tisanasankhe zochita. Koma kodi tingatani kuti tikulitse luso lathu lotha kusankha zochita mwanzeru? Nanga kodi tikasankha zochita sitiyenera kusintha zivute zitani?

TONSEFE TIMAFUNIKA KUSANKHA ZOCHITA

4. Kodi Adamu anafunika kusankha zochita pa nkhani iti, nanga zotsatira za zimene anasankha zinali zotani?

4 Kuyambira kale, anthu amafunika kusankha zochita. Mwachitsanzo, Adamu ankafunika kusankha kumvera Mulungu kapena Hava. Koma Adamu sanasankhe bwino chifukwa anamvera mkazi wake. Izi zinachititsa kuti athamangitsidwe m’munda wa Edeni ndipo pamapeto pake anamwalira. Koma si zokhazi. Mpaka pano anthufe timavutikabe chifukwa choti Adamu sanasankhe mwanzeru.

5. Kodi inuyo mumaona kuti Mulungu anachita bwino kutipatsa ufulu wosankha zochita?

5 Anthu ena angaganize kuti zikanakhala bwino anthufe tikanati tisamasankhe zochita. Kodi inunso mumaona choncho? Tizikumbukira kuti Yehova sanatilenge ngati maloboti koma anatilenga kuti tizitha kuganiza ndiponso kusankha zochita. Komanso watipatsa Mawu ake kuti azitithandiza kusankha zochita mwanzeru. Yehova amafuna kuti tizisankha zochita ndipo izi zili ndi ubwino wake. Tiyeni tikambirane umboni wa zimenezi.

6, 7. Kodi Aisiraeli anafunika kusankha zochita pa nkhani iti, nanga n’chifukwa chiyani ankavutika kusankha mwanzeru? (Onani chithunzi patsamba 13.)

6 Aisiraeli ali m’Dziko Lolonjezedwa ankafunika kusankha kulambira Yehova kapena milungu ina. (Werengani Yoswa 24:15.) Zimene akanasankha pa nkhaniyi zikanachititsa kuti akhale ndi moyo kapena afe. Mwina mungaganize kuti nkhani imeneyi inali yosavuta kusankha. Komabe n’zodabwitsa kuti m’nthawi ya oweruza, Aisiraeli mobwerezabwereza sankasankha zochita mwanzeru. Iwo ankasiya kutumikira Yehova n’kumatumikira milungu ina. (Ower. 2:3, 11-23) Kenako m’nthawi ya Eliya, Aisiraeli ankafunika kusankha kutumikira Mulungu kapena Baala. (1 Maf. 18:21) Ena angaganize kuti zinalinso zosavuta kusankha pa nkhaniyi chifukwa woyenera kumulambira ndi Yehova. Munthu woganiza bwino sangasankhe kulambira mulungu wopanda moyo. Koma Aisiraeliwo analephera kusankha ndipo ‘ankangokayikakayika.’ Choncho Eliya anawalimbikitsa kuti ayenera kusankha kulambira Yehova chifukwa ndi Mulungu woona.

7 N’chifukwa chiyani Aisiraeliwa zinkawavuta kusankha mwanzeru pa nkhaniyi? Choyamba, anali atasiya kukhulupirira Yehova ndipo sankamumveranso. Iwo sankadziwa zolondola, sankadalira Mulungu komanso sankatsogoleredwa ndi nzeru zake. Akanakhala kuti ankadziwa zolondola za Mulungu ndipo ankachita zinthu mogwirizana ndi zomwe ankadziwazo, akanatha kusankha mwanzeru pa nkhaniyi. (Sal. 25:12) Chachiwiri, ankalola kuti azingoyendera maganizo a anthu osalambira Yehova, mwinanso mpaka kumawalola kuti aziwasankhira zochita. Aisiraeli anasokonezeka kwambiri ndi anthu  amenewa moti mpaka anayamba kulambira mafano. Ndipotu Yehova anali ataneneratu kuti zoterezi zidzachitika.—Eks. 23:2.

KODI TIZILOLA KUTI ANTHU ENA AZITISANKHIRA ZOCHITA?

8. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Aisiraeli pa nkhani yosankha zochita?

8 Tingaphunzire zambiri pa zitsanzo za Aisiraeli zimene takambiranazi. Aliyense ali ndi udindo wosankha zochita ndipo kuti tizisankha zochita mwanzeru tiyenera kudziwa bwino mfundo za m’Malemba. Lemba la Agalatiya 6:5 limati: “Aliyense ayenera kunyamula katundu wake.” Choncho sitiyenera kupatsa munthu wina udindo wathu wosankha zochita. M’malomwake tiyenera kufufuza kuti tidziwe zimene Mulungu angasangalale nazo, n’kusankha zimenezo.

9. Kodi kulola kuti ena azitisankhira zochita n’koopsa bwanji?

9 Ngati talola kuyendera maganizo a anthu ena n’kusankha zolakwika, ndiye kuti anthuwo atisankhira zochita. (Miy. 1:10, 15) Koma ndi udindo wathu kusankha zochita mogwirizana ndi chikumbumtima chathu chabwino ngakhale zitakhala kuti ena akutikakamiza kuti tisankhe zinazake. Tikalola kuti ena atisankhire zochita zimakhala ngati tasankha ‘kuyenda nawo limodzi panjira’ yawo. Koma zimenezi zikhoza kutibweretsera mavuto.

10. Kodi mtumwi Paulo anachenjeza Agalatiya za chiyani?

10 Mtumwi Paulo anachenjeza Agalatiya za kuipa kolola kuti ena aziwasankhira zochita. (Werengani Agalatiya 4:17.) Anthu ena mumpingo ankafuna kuti azisankhira anzawo zochita n’cholinga choti anthuwo azitsatira iwowo osati atumwi. Anthuwa anali odzikonda komanso ankafuna udindo. Anthu amenewa ankachita zinthu mopitirira malire ndipo sankalemekeza ufulu wa ena wosankha zochita.

11. Kodi tingathandize bwanji ena akafuna kusankha zochita?

11 Tingaphunzire zambiri pa chitsanzo cha mtumwi Paulo. Iye ankadziwa kuti abale ake ali ndi ufulu wosankha okha zochita ndipo ankalemekeza ufulu wawowo. (Werengani 2 Akorinto 1:24.) Masiku anonso akulu akamapereka malangizo pa nkhani  imene munthu ayenera kusankha yekha, ayenera kutengera chitsanzo cha Paulo. Iwo angakambirane ndi munthuyo mfundo za m’Malemba. Komabe amalola kuti munthuyo asankhe yekha zochita. Zimenezi n’zomveka chifukwa munthuyo ndi amene adzakumane ndi zotsatira za zimene angasankhezo. Choncho mfundo yoti tonse tiziikumbukira ndi yakuti: Tikhoza kuthandiza anthu kumvetsa malangizo a M’Baibulo amene angawathandize, koma tisamaiwale kuti udindo wosankha ndi wawo. Akasankha zochita mwanzeru, zinthu zingawayendere bwino. Ndipotu tiyenera kupewa chizolowezi choganiza kuti tili ndi mphamvu zosankhira abale ndi alongo athu zochita.

Akulu achikondi amathandiza ena kuti azitha kusankha okha zochita (Onani ndime 11)

TISAMANGOTSATIRA MTIMA WATHU

12, 13. N’chifukwa chiyani n’zoopsa kusankha zochita titakwiya kapena titakhumudwa?

12 Anthu ambiri akafuna kusankha zochita amangotsatira zimene mtima wawo ukufuna. Komatu kuchita zimenezi n’koopsa kwambiri ndiponso n’kosemphana ndi mfundo za m’Malemba. Baibulo limatichenjeza kuti tikafuna kusankha zochita tisamangotsatira zofuna za mtima wathu. (Miy. 28:26) Limafotokozanso kuti pamakhala zotsatira zomvetsa chisoni tikamangotsatira zofuna za mtima wathu. Sitingadalire mtima wathu chifukwa “ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa.” (Yer. 3:17; 13:10; 17:9; 1 Maf. 11:9) Ndiye kodi mukuganiza kuti zinthu zingakuthereni bwanji mutati muzingotsatira mtima wanu posankha zochita?

13 N’zoona kuti mtima ndi wofunika kwambiri ndipo Yehova amatilamula kuti tizimukonda ndi mtima wathu wonse komanso tizikonda anzathu mmene timadzikondera. (Mat. 22:37-39) Koma tiyenera kukhala osamala. Malemba amene ali m’ndime yapitayi akusonyeza kuopsa kotsatira mtima posankha zochita. Mwachitsanzo, kodi chingachitike n’chiyani ngati tingasankhe zochita titakwiya? Yankho la funsoli n’lodziwikiratu. (Miy. 14:17; 29:22) Komanso ngati tikusankha zochita titakhumudwa, kodi tingasankhe mwanzeru? (Num. 32:6-12; Miy. 24:10) Tiyenera kulola kuti “chilamulo cha Mulungu” chizititsogolera. (Aroma 7:25) Choncho n’zoonekeratu kuti sitiyenera kusankha zochita titakwiya kapena titakhumudwa.

NTHAWI ZINA TINGAFUNIKE KUSINTHA ZOMWE TINASANKHA

14. N’chiyani chikusonyeza kuti sikulakwa kusintha zimene tinasankha?

14 Anthufe tiyenera kusankha zinthu mwanzeru. Koma izi sizikutanthauza kuti tikasankha zochita ndiye kuti basi tasankha. Nthawi zina timafunika kuganiziranso zimene tinasankha mwinanso n’kuzisintha. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene Yehova anachita ndi anthu a ku Nineve m’nthawi ya Yona. Baibulo limati: “Mulungu woona anaona ntchito zawo. Anaona kuti alapa ndi kusiya njira zawo zoipa. Choncho, Mulungu woona anasintha maganizo ake pa tsoka limene ananena kuti awabweretsera, moti sanawabweretsere.” (Yona 3:10) Yehova ataona kuti anthu a ku Nineve alapa, anasintha zimene ankafuna kuchita. Apatu anasonyeza kuti ndi wodzichepetsa, wachifundo komanso amamvetsa zinthu. Iye sali ngati anthu amene amasankha zochita mopupuluma chifukwa choti akwiya kapena akhumudwa.

15. N’chiyani chingatichititse kusintha zimene tinasankha?

 15 Nafenso nthawi zina tingafunike kuganiziranso zimene tinasankha. Ngati zinthu zina zasintha, ifenso tikhoza kusintha. Nayenso Yehova amasintha maganizo zinthu zikasintha. (1 Maf. 21:20, 21, 27-29; 2 Maf. 20:1-5) Mwachitsanzo, tikadziwa mfundo ina yatsopano tikhoza kusintha zimene tinasankha. Izi n’zimene zinachitikira Mfumu Davide. Poyamba anauzidwa zinthu zabodza zokhudza mdzukulu wa Sauli dzina lake Mefiboseti. Koma atamva zoona zake anasintha zimene anasankha poyamba. (2 Sam. 16: 3, 4; 19:24-29) Choncho nthawi zina ifenso tiyenera kuchita chimodzimodzi.

16. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani tikafuna kusankha zochita? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kuonanso zimene tinasankha?

16 Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti tisamasankhe zochita mopupuluma pa nkhani zikuluzikulu. (Miy. 21:5) Tikaganizira mfundo zosiyanasiyana tisanasankhe zochita, tikhoza kusankha zinthu mwanzeru. (1 Ates. 5:21) Amuna asanasankhe zochita pa nkhani yokhudza banja lonse ayenera kufufuza m’Malemba, m’mabuku athu komanso kumva maganizo a anthu ena m’banjamo. Kumbukirani kuti Yehova anauza Abulahamu kuti amvere maganizo a mkazi wake. (Gen. 21:9-12) Nawonso akulu ayenera kufufuza asanasankhe zochita. Iwo ayenera kukhala ololera komanso odzichepetsa. Makhalidwe amenewa angawathandize kuti akadziwa mfundo zatsopano, asamaope kusintha zimene anasankha poganiza kuti anyozeka. Iwo ayenera kukhala okonzeka kusintha ngati pakufunika kutero, ndipo ifenso tiyenera kutengera chitsanzo chawo. Izi zingathandize kuti mumpingo mukhale bata ndi mtendere.—Mac. 6:1-4.

TIZIYESETSA KUCHITA ZIMENE TASANKHA

17. Kodi tingatani kuti tizisankha zochita mwanzeru?

17 Nkhani zina zimakhala zazikulu ndipo pamafunika kuziganizira kwa nthawi yaitali komanso kuzipempherera. Mwachitsanzo, Mkhristu angafunike kusankha nthawi yolowa m’banja komanso munthu woti akwatirane naye. Ena amafunika kusankha utumiki wa nthawi zonse umene angachite komanso nthawi yoyamba utumikiwo. Pa nkhani ngati zimenezi, tiyenera kudalira Yehova ndipo tisamakayikire kuti iye amapereka malangizo othandiza. (Miy. 1:5) Choncho ndi bwino kufufuza m’Baibulo komanso kupempha Yehova kuti atitsogolere. Yehova angatithandize kukhala ndi makhalidwe ofunika kuti tisankhe bwino mogwirizana ndi chifuniro chake. Nthawi zonse tikamasankha zochita tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi zimene ndikusankhazi zisonyeza kuti ndimakonda kwambiri Yehova? Kodi zithandiza kuti aliyense m’banjali azisangalala? Nanga zisonyeza kuti ndine woleza mtima komanso wokoma mtima?’

18. N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizisankha tokha zochita?

18 Yehova sachita kutikakamiza kuti tizimukonda komanso kumutumikira. Amafuna kuti tizisankha tokha kuchita zimenezi. Iye anatipatsa ufulu wosankha ndipo amatisiya kuti tizisankha tokha ngati tikufuna kumutumikira kapena ayi. (Yos. 24:15; Mlal. 5:4) Koma amafunanso kuti tiziyesetsa kuchita zimene tasankha mogwirizana ndi malangizo ake. Tikamakhulupirira Yehova komanso mfundo zake, tingamasankhe zochita mwanzeru komanso sitingakhale okayikakayika pochita zinthu.—Yak. 1:5-8; 4:8.