Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MBIRI YA MOYO WANGA

Kuyenda Ndi Anthu Anzeru Kwandithandiza Kwambiri

Kuyenda Ndi Anthu Anzeru Kwandithandiza Kwambiri

NDIMAKUMBUKIRABE zimene zinachitika m’mawa wa tsiku linalake zaka zambiri zapitazo tili mumzinda wa Brookings ku South Dakota m’dziko la United States. Zinkachita kuonekeratu kuti kunja kuyamba kuzizira kwambiri. Pa nthawiyi ine ndi anthu ena atatu tinali m’chibalani chinachake ndipo tinkanjenjemera. Tinaima pafupi ndi chibeseni chachikulu chomwe munali madzi ozizira ndipo tinkadikira kubatizidwa. Mwina ndifotokoze kaye zokhudza mbiri ya moyo wanga.

BANJA LIMENE NDINAKULIRA

A Alfred ali ndi abambo anga

Ndinabadwa pa 7 March 1936. M’banja lathu tinalipo ana 4 ndipo ine ndine wamng’ono. Tinkakhala pafamu yaing’ono kum’mawa kwa South Dakota. Banja lathu linkakonda ulimi koma sikuti tinkaona kuti ndi wofunika kuposa chilichonse. Makolo anga anabatizidwa mu 1934. Popeza anadzipereka kwa Yehova, ankaona kuti kuchita chifuniro chake n’kofunika kwambiri kuposa chilichonse. Bambo anga a Clarence komanso bambo anga aakulu a Alfred anatumikirapo mumpingo wina wa ku Conde ku South Dakota ngati wogwirizanitsa ntchito za akulu. Pa nthawiyo ankati mtumiki wa mpingo.

Banja lathu linkakonda kusonkhana komanso kulalikira n’kumauza anthu za madalitso am’tsogolo. Zimene makolo athu ankatiphunzitsa komanso chitsanzo chawo zinatithandiza kwambiri. Mchemwali wanga Dorothy anakhala wofalitsa ali ndi zaka 6 ndipo inenso nditakwanitsa zaka 6 ndinakhala wofalitsa. Mu 1943 ndinalembetsa m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu yomwe inali itangoyamba kumene.

Ndikuchita upainiya mu 1952

Banja lathu linkakonda kwambiri misonkhano yadera komanso yachigawo moti sitinkaphonya misonkhanoyi. Ndimakumbukirabe msonkhano wachigawo wina womwe unachitikira ku Sioux  Falls ku South Dakota mu 1949. M’bale Grant Suiter anali mlendo pamsonkhanowu ndipo anakamba nkhani ya mutu wakuti: “Mapeto Ali Pafupi Kuposa Mmene Mukuganizira.” M’baleyu anatsindika mfundo yoti Mkhristu aliyense ayenera kudzipereka ndi mtima wonse pa ntchito yolalikira. Izi zinandithandiza kuti ndidzipereke kwa Yehova. Choncho pamsonkhano wadera wotsatira womwe unachitikira ku Brookings ndinabatizidwa. Apa panali pa November 12, 1949 ndipo zimene zinachitika ndi zomwe ndafotokoza poyamba paja.

Ndinali ndi cholinga chodzakhala mpainiya ndipo ndili ndi zaka 15 ndinayambadi utumikiwu pa 1 January 1952. Baibulo limati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru.” (Miy. 13:20) Ndipo ndingati m’banja lathu munali anthu ambiri anzeru amene anandithandiza kuti ndikwaniritse utumiki wanga. Mwachitsanzo, nditayamba upainiya ndinkayenda ndi abambo anga aakulu omwe anali ndi zaka 60 dzina lawo a Julius. Ngakhale kuti tinkasiyana kwambiri zaka, anali anzanga ndipo tinkasangalala kwambiri. Ndinaphunzira zambiri kwa abambo angawa. Pasanapite nthawi yaitali Dorothy nayenso anayamba upainiya.

OYANG’ANIRA MADERA ANANDITHANDIZA KWAMBIRI

Ndili wamng’ono, makolo anga ankakonda kuitana woyang’anira dera ndi mkazi wake kuti adzafikire kwathu. Banja lina limene linandithandiza kwambiri linali la a Jesse ndi a Lynn Cantwell. Banjali ndi limene linandilimbikitsa kuti ndiyambe upainiya. Iwo ankandikonda kwambiri moti zinandithandiza kuti ndikhale ndi zolinga zochita utumiki. Nthawi zina akamachezera mpingo wapafupi ankandiitana kuti ndikalalikire nawo. Zimenezi zinkandisangalatsa komanso kundilimbikitsa kwambiri.

Kenako M’bale Bud Miller anakhala woyang’anira dera wathu ndipo mkazi wake anali Joan. Pa nthawiyo ndinali ndi zaka 18 ndipo munthu akafika zaka zimenezi ankaitanidwa ku usilikali. Komiti yoona zolemba asilikali inandipatsa ntchito yomwe inkasemphana ndi lamulo la Yesu loti tisamalowerere ndale. Chomwe ine ndinkafuna ndi kulalikira uthenga wa Ufumu basi. (Yoh. 15:19) Choncho ndinaganiza zokapempha komitiyo kuti ivomereze kuti ndine mtumiki wa Mulungu ndipo sindikuyenera kukhala msilikali.

 Ndinasangalala kwambiri M’bale Miller atanena kuti andiperekeza pokaonana ndi komitiyo ndipo ndinalimba mtima. M’baleyo ankadziwa bwino Malemba ndipo mwachibadwa anali wopanda manyazi kapena mantha. Zotsatira zake zinali zakuti mu 1954 komitiyo inavomereza kuti ndine mtumiki wa Mulungu. Izi zinandithandiza kuti ndikhale ndi mwayi wochita utumiki wina.

Nditangoyamba kumene utumiki wa pa Beteli

Pasanapite nthawi yaitali, ndinaitanidwa kuti ndikatumikire ku Beteli pa Famu ya Watchtower yomwe inali pachilumba cha Staten ku New York. Ndinatumikira kumeneku kwa zaka zitatu ndipo ndinasangalala kwabasi chifukwa ndinkagwira ntchito ndi abale ndi alongo anzeru kwambiri.

UTUMIKI WA PA BETELI

Tili ndi M’bale Franz pachikwangwani cha WBBR

Pafamupa panalinso siteshoni ya wailesi ya WBBR. A Mboni za Yehova anagwiritsa ntchito wailesiyi kuyambira mu 1924 mpaka mu 1957. Pafamuyi tinalipo anthu okwana 15 kapena 20. Ambirife tinali achinyamata komanso sitinkadziwa zambiri. Koma tinkagwira ntchito limodzi ndi m’bale wina wodzozedwa dzina lake Eldon Woodworth. M’baleyu ankatikonda ngati ana ake ndipo anatiphunzitsa zinthu zambiri. Nthawi zina tikasemphana maganizo, M’bale Woodworth ankatiuza kuti: “Yehova akuchita zazikulu ngakhale kuti akugwiritsa ntchito anthu omwe si angwiro.”

M’bale Peterson ankalalikira mwakhama kwambiri

Tinalinso ndi M’bale Frederick W. Franz ndipo ankatithandiza kwambiri. Iye anali munthu wanzeru komanso wodziwa kwambiri Malemba ndipo ankatikonda tonsefe. Amene ankatiphikira chakudya anali M’bale Papargyropoulos Peterson. Tinkakonda kumuitanira dzina lomaliza chifukwa dzina lake loyamba linkativuta kutchula. Nayenso anali wodzozedwa ndipo ankakonda kwambiri kulalikira. M’bale Peterson ankalimbikira kwambiri ntchito ya pa Beteli koma sankanyalanyaza kulalikira. Nthawi zina ankagawira magazini oposa 100 pa mwezi. M’baleyu ankalidziwanso bwino Baibulo ndipo ankatiyankha mafunso ambiri.

ALONGO ANZERU ANANDITHANDIZANSO

Pa chaka tinkakolola masamba ndi zipatso zambiri ndipo tikazikonza zinkakwana zitini 45,000. Zinthu zimenezi zinkagwiritsidwa ntchito pa Beteli. Ndinali ndi mwayi wotumikira limodzi ndi  mlongo wina dzina lake Etta Huth. Mlongoyu ndi amene ankaona zonse zokhudzana ndi kukonza zinthu zimene tinkakolola kuti zisungidwe bwino. Alongo ena akuderali ankaitanidwa kuti adzathandize pa ntchitoyi ndipo a Etta ndi amene ankakonza ntchito yoti agwire. Ngakhale kuti a Etta ankathandiza kwambiri pa ntchitoyi, ankalemekeza abale oyang’anira. Ndinkaona kuti iwo ankasonyeza chitsanzo chabwino pa nkhani ya kugonjera.

Ndili ndi Angela komanso Mlongo Etta Huth

Koma pafamupa ndinakumananso ndi mlongo wina dzina lake Angela Romano. Iye anali mmodzi mwa alongo amene ankabwera kudzathandiza aja. A Etta ndi amene anamuthandiza kwambiri mtsikanayu pamene ankaphunzira choonadi. Ine ndi Angela tinakwatirana mu April 1958. Takhala m’banja kwa zaka 58 ndipo tachitira limodzi utumiki wosiyanasiyana. Angela ndi mlongo wokhulupirika kwa Yehova ndipo zimenezi zathandiza kwambiri banja lathu. Ndi munthu woti ndimamudalira pa vuto lililonse.

UTUMIKI WAUMISHONALE KOMANSO WOYENDAYENDA

Wailesi ya WBBR itagulitsidwa m’chaka cha 1957, ndinapita kukatumikira pa Beteli ya ku Brooklyn kwa nthawi yochepa. Nditakwatirana ndi Angela, ndinachoka pa Beteli ndipo tinachita upainiya pachilumba cha Staten kwa zaka zitatu. Ndinagwiraponso ntchito kwa anthu amene anagula siteshoni ya wailesi yathu ija ndipo pa nthawiyi inkatchedwa WPOW.

Ine ndi Angela tinkakhala moyo wosalira zambiri kuti tizitha kukatumikira kulikonse. Choncho chakumayambiriro kwa chaka cha 1961 tinatumizidwa ku Falls City ku Nebraska, kuti tizikachita upainiya wapadera. Koma titangofika kumeneko, tinalandiranso kalata yotiuza kuti tikalowe Sukulu ya Utumiki wa Ufumu. Sukuluyi inali ya mwezi umodzi ndipo inachitikira ku South Lansing ku New York. Tinasangalala kwambiri ndi sukuluyi ndipo tinkafunitsitsa kukagwiritsa ntchito zimene tinaphunzira tikabwerera ku Nebraska. Koma titamaliza, anatiuza kuti tipite kukachita umishonale ku Cambodia. Dzikoli ndi lokongola kwambiri ndipo lili ku Southeast Asia. Kumeneko tinaona, kumva komanso kulawa zinthu zambiri zomwe zinali zatsopano kwa ife. Tinkafunitsitsa kulalikira uthenga wabwino kwa anthu a m’dzikoli.

Koma zinthu zitasintha pa nkhani zandale, tinachoka m’dzikoli n’kupita ku South Vietnam. N’zomvetsa chisoni kuti patangopita zaka ziwiri ndinapezeka ndi matenda aakulu. Choncho tinafunika kubwerera kwathu. Tinakhala kumeneko mpaka pamene ndinapeza bwino. Nditangochira, ndinayambiranso kuchita utumiki wa nthawi zonse.

Ndili ndi Angela mu 1975 tikudikira kuti atifunse mafunso pa TV

Mu March 1965 tinayamba utumiki woyang’anira dera. Kwa zaka 33, ine ndi Angela takhala tikugwira ntchito yoyang’anira dera komanso chigawo. Tinkathandizanso abale pokonzekera misonkhano yachigawo. Ndinkasangalala kwambiri ndi ntchitoyi chifukwa ndimakonda misonkhano yachigawo. Kwa zaka zambiri tinkayendera mipingo ya mu New York City ndi madera ozungulira ndipo misonkhano yambiri yachigawo tinkachitira ku Yankee Stadium.

TINABWERERA KU BETELI NDIPO NDINAKAKHALA MLANGIZI

Ine ndi Angela tachita utumiki wosiyanasiyana kwa zaka zambiri ndipo wina unali wovuta. Mwachitsanzo, mu 1995 ndinapemphedwa kuti ndikakhale  mlangizi wa Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Patapita zaka zitatu, tinaitanidwa ku Beteli. Ndinasangalala kupitanso kumalo amene ndinayambira utumiki wa nthawi zonse wapadera zaka 40 m’mbuyomo. Kwa kanthawi ndinkagwira ntchito ku Dipatimenti ya Utumiki ndipo ndinakhalapo mlangizi wa makalasi angapo. Mu 2007, Bungwe Lolamulira linakhazikitsa Dipatimenti Yoyang’anira Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu kuti iziyang’anira masukulu onse. Ineyo ndinali ndi mwayi wokhala woyang’anira dipatimentiyi kwa zaka zingapo.

Posachedwapa, zinthu zasintha kwambiri pa masukulu amenewa. Mwachitsanzo, mu 2008 Sukulu ya Akulu inakhazikitsidwa. Pa zaka ziwiri zotsatira, akulu oposa 12,000 anaphunzitsidwa m’sukuluyi ku Patterson komanso ku Brooklyn. Sukulu imeneyi ikuchitikabe m’madera osiyanasiyana ndipo pali alangizi amene amaphunzitsa. Mu 2010, Sukulu Yophunzitsa Utumiki inasinthidwa kukhala Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira. Kenako panakhazikitsidwanso Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja.

Mu 2015 masukulu awiriwa anaphatikizidwa n’kupanga Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Panopa Akhristu apabanja komanso amene sali pabanja akhoza kulowa sukuluyi. Abale ndi alongo padziko lonse anasangalala kumva kuti sukuluyi izichitikanso m’mayiko ambiri. N’zosangalatsa kwambiri kuti mwayi watseguka woti anthu ambiri aphunzitsidwe. Ndimasangalala kuona anthu akusintha zina ndi zina pa moyo wawo n’cholinga choti alowe sukuluyi.

Ndikaganizira za moyo wanga kuyambira ndisanabatizidwe m’chibeseni chija kufika pano, ndimathokoza kwambiri anthu anzeru ndipo ndaphunzira zambiri kwa iwo. Ambiri sanali a msinkhu wanga ndipo ena tinkasiyana chikhalidwe. Koma zochita zawo komanso khalidwe lawo zimasonyeza kuti amakonda kwambiri Yehova. Choncho m’gulu la Yehova muli anthu ambiri anzeru ndipo tingaphunzire zambiri kwa iwo.

Ndimasangalala kukumana ndi ophunzira ochokera m’mayiko osiyanasiyana