NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) March 2017

Magaziniyi ili ndi nkhani zophunzira kuyambira May 1 mpaka 28, 2017.

MBIRI YA MOYO WANGA

Kuyenda Ndi Anthu Anzeru Kwandithandiza Kwambiri

Pa zaka zimene a William Samuelson akhala akuchita utumiki wa nthawi zonse, akumana ndi zinthu zovuta komanso zosangalatsa.

Tizipereka Ulemu kwa Oyenera Kulemekezedwa

Kodi tiyenera kupereka ulemu kwa ndani ndipo n’chifukwa chiyani? Kodi ubwino wopereka ulemu woyenera ndi wotani?

Muzikhulupirira Yehova Kuti Muzisankha Zochita Mwanzeru

Zinthu zina zimene timasankha, zimakhudza kwambiri moyo wathu. Ndiye tingatani kuti tizisankha zochita mwanzeru?

Tizitumikira Yehova ndi Mtima Wathunthu

Asa, Yehosafati, Hezekiya komanso Yosiya onsewa anali mafumu a Yuda ndipo analakwitsapo zinazake. Komabe Mulungu anawaona kuti ankamutumikira ndi mtima wathunthu. N’chifukwa chiyani zili choncho?

Kodi Mumatsatira ndi Mtima Wonse Zimene Zinalembedwa?

Tingaphunzire zambiri kuchokera pa zimene ena analakwitsa, ngakhalenso anthu otchulidwa m’Baibulo

Kodi Mumakhalabe Bwenzi Labwino Zinthu Zikavuta?

Nthawi zina mungafunike kuthandiza mnzanu amene walakwitsa zinazake. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

Dzina la M’Baibulo Linapezeka Pamtsuko Wakale

Mu 2012 anthu ofukula zinthu zakale anasangalala atapeza mapale a mtsuko winawake womwe unaumbidwa zaka 3,000 zapitazo. Kodi chinali chapadera n’chiyani ndi zimene anapezazi?