Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amatsogolera Anthu Ake Kuti Adzapeze Moyo

Yehova Amatsogolera Anthu Ake Kuti Adzapeze Moyo

“Njira ndi iyi. Yendani mmenemu.”—YES. 30:21.

NYIMBO: 65, 48

1, 2. (a) Kodi n’chiyani chinathandiza kuti anthu ambiri apulumuke? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) Kodi n’chiyani chimathandiza kwambiri anthu a Mulungu?

ZAKA zoposa 100 zapitazo, ku North America kunali malo ena pamene msewu wina unkadutsana ndi njanji. Pamalowa panali zikwangwani zikuluzikulu zokhala ndi mawu amene ankathandiza kwambiri madalaivala a galimoto. Mawuwa ankauza dalaivala kuti aime kaye, ayang’ane mbali zonse ndipo amvetsere ngati kukubwera sitima. Izi zinkathandiza kuti madalaivala asawombedwe ndi sitima zomwe zinkadutsa mothamanga kwambiri. Kutsatira malangizowa kunapulumutsa anthu ambiri chifukwa kunathandiza kuti pamalowa pasamachitike ngozi.

2 Nayenso Yehova amapereka malangizo othandiza kwa anthu ake. Amawauza zimene angachite kuti apewe zinthu zimene zingaike moyo wawo pa ngozi komanso zomwe angachite kuti adzapeze moyo wosatha. Yehova ali ngati m’busa amene amateteza ndiponso kuchenjeza nkhosa zake kuti zisalowere kolakwika.—Werengani Yesaya 30:20, 21.

 YEHOVA WAKHALA AKUTSOGOLERA ANTHU AKE

3. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti anthufe tizivutika komanso kufa?

3 Kuyambira kale kwambiri, Yehova wakhala akupatsa anthu ake malangizo. Mwachitsanzo, m’munda wa Edeni anapereka malangizo omveka bwino omwe akanathandiza kuti anthu onse azikhala mosangalala komanso mpaka kalekale. (Gen. 2:15-17) Koma Adamu ndi Hava sanamvere malangizo a Mulungu. Hava anamvera zimene njoka inamuuza ndipo Adamu anamvera mkazi wake. Zotsatira zake n’zakuti onse anafa ndipo sadzakhalanso ndi moyo. Komanso kusamvera kwawoko kunachititsa kuti anthu onse azivutika ndiponso kufa.

4. (a) Chigumula chitatha, n’chifukwa chiyani Mulungu anafunika kupereka malangizo atsopano? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa lamulo limene anapereka?

4 M’nthawi ya Nowa, Yehova anaperekanso malangizo omwe anathandiza kuti Nowa ndi banja lake apulumuke. Chigumula chitatha, Yehova analamula anthu kuti asamadye magazi. Kodi n’chifukwa chiyani anapereka lamuloli? N’chifukwa cha mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Yehova analola kuti anthu azidya nyama, choncho anafunika kuwapatsa malangizo ogwirizana ndi zimenezi. Iye anawauza kuti: “Musadye nyama pamodzi ndi magazi ake, amene ndiwo moyo wake.” (Gen. 9:1-4) Lamuloli likutithandiza kudziwa mmene Mulungu amaonera moyo. Iye ndi Mlengi komanso ndi amene anatipatsa moyo, choncho ali ndi ufulu wotipatsa malamulo okhudza moyo. Mwachitsanzo, anapereka lamulo lakuti pasamapezeke aliyense wopha munthu. Mulungu amaona kuti moyo komanso magazi ndi zinthu zopatulika ndipo adzaimba mlandu aliyense wopha munthu kapena wogwiritsa ntchito magazi molakwika.—Gen. 9:5, 6.

5. Kodi tsopano tikambirana chiyani ndipo zimenezi zitithandiza bwanji?

5 Tsopano tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo zosonyeza kuti Mulungu anapitirizabe kutsogolera anthu ake. Zimene tikambiranezo zitithandiza kuti nafenso tizitsatira malangizo a Yehova amene angatithandize kuti tidzapulumuke.

MTUNDU WATSOPANO UNALANDIRA MALANGIZO ATSOPANO

6. N’chifukwa chiyani Aisiraeli ankayenera kumvera malamulo a Mulungu kudzera mwa Mose, ndipo ankayenera kuwaona bwanji?

6 M’nthawi ya Mose, Yehova anapatsa anthu ake malangizo omveka bwino oti aziwatsatira pa moyo wawo komanso pomulambira. Apanso anachita zimenezi chifukwa cha mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Aisiraeli anali atakhala akapolo ku Iguputo zaka zoposa 200. Anthu a kumeneko ankalambira mafano, anthu akufa komanso ankachita zinthu zosalemekeza Yehova. Choncho Yehova atapulumutsa Aisiraeli ku Iguputo, iwo ankafunika malangizo atsopano. Anthu a Mulunguwa anayenera kuyamba kutsatira Chilamulo cha Yehova. Mabuku ena amati mawu achiheberi akuti “lamulo,” ndi ofanana ndi mawu amene amatanthauza, “kutsogolera” kapena “kulangiza.” Chilamulo chinkateteza Aisiraeli kuti asatengere makhalidwe oipa komanso kulambira konyenga kwa anthu a mitundu ina. Aisiraeli akamamvera, Mulungu ankawadalitsa koma akasiya kumumvera ankakumana ndi mavuto aakulu.—Werengani Deuteronomo 28:1, 2, 15.

7. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anapereka malangizo kwa anthu ake? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Chilamulo chinali mtsogoleri wa Aisiraeli?

7 Koma palinso chifukwa china chimene Mulungu anaperekera malangizo atsopano kwa Aisiraeli kudzera m’Chilamulo. Chilamulo  chinawathandiza kuti akonzekere kubwera kwa Mesiya ndipo kubwera kwa Mesiyako kunali kogwirizana kwambiri ndi cholinga cha Yehova. Komanso Chilamulochi chinkathandiza Aisiraeli kukumbukira kuti ndi ochimwa. Chinawathandizanso kudziwa kuti ankafunika nsembe ya dipo imene ingachotseretu machimo awo. (Agal. 3:19; Aheb. 10:1-10) Kuwonjezera pamenepa, Chilamulo chinathandizanso kuti mzere wobadwira Mesiya usasokonekere komanso kuti Aisiraeliwo adzathe kumuzindikira. Choncho Chilamulochi chinali ‘mtsogoleri wowafikitsa kwa Khristu.’—Agal. 3:23, 24.

8. Kodi mfundo za m’Chilamulo cha Mose zingatithandize bwanji?

8 Malangizo amene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli ndi othandizanso kwa ife. Tikutero chifukwa chakuti ngakhale kuti sititsatira Chilamulo, mfundo zake zingatithandize pa moyo wathu komanso polambira Yehova. Yehova analola kuti Chilamulo chilembedwe m’Baibulo n’cholinga choti tiphunzirepo kanthu komanso mfundo zake zizititsogolera. Anafunanso kuti chizitithandiza kuzindikira kuti zimene Yesu anatiphunzitsa ndi zofunika kwambiri. Mwachitsanzo, Yesu ananena kuti: “Inu munamva kuti anati, ‘Usachite chigololo.’ Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.” Choncho, sikuti tiyenera kungopewa chigololo, koma tiyeneranso kupewa maganizo amene angatipangitse kuti tichite chigololocho.—Mat. 5:27, 28.

9. Kodi n’chifukwa chiyani anthu a Mulungu anafunika kupatsidwa malangizo atsopano?

9 Mesiya atafika, Yehova anaperekanso malangizo atsopano kwa anthu ake komanso anawaululira zinthu zina zokhudza cholinga chake. Iye anachita izi chifukwa cha mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Mu 33 C.E. Yehova anakana mtundu wa Isiraeli ndipo anayamba kugwiritsa ntchito mpingo wachikhristu. Choncho anthu ake anafunika kupatsidwa malangizo atsopano.

YEHOVA ANAPEREKA MALANGIZO KWA AKHRISTU

10. N’chifukwa chiyani Mulungu anapatsa Akhristu malamulo atsopano, ndipo malamulowa ankasiyana bwanji ndi amene Aisiraeli anapatsidwa?

10 M’nthawi ya atumwi, anthu a Mulungu analandira malangizo atsopano oti azitsatira pa moyo wawo komanso polambira Yehova. Anthuwa, omwe anali mumpingo wachikhristu, ankadziwikanso kuti Isiraeli wauzimu ndipo anali mu pangano latsopano. Paja Chilamulo chinaperekedwa kwa mtundu wa Aisiraeli wokha. Koma Akhristuwa anali ochokera m’mitundu komanso zikhalidwe zosiyanasiyana. Izi zikusonyeza kuti “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Mac. 10:34, 35) Chilamulo cha Mose chinalembedwa pamiyala ndipo chinatsogolera Aisiraeli M’dziko Lolonjezedwa. Koma Isiraeli wauzimu anapatsidwa “chilamulo cha Khristu” chomwe mfundo zake zinalembedwa m’mitima.—Agal. 6:2.

11. Kodi ndi malamulo ati amene akugwirizana kwambiri ndi “chilamulo cha Khristu”?

11 Malangizo amene Mulungu anapatsa Akhristu kudzera mwa Mwana wake, anawathandiza kwambiri. Yesu asananene za pangano latsopano, anapereka malamulo awiri. Lamulo loyamba linali lokhudza ntchito yolalikira. Lachiwiri linali loti otsatira ake ayenera kumakondana. Malamulowa anali opita kwa Akhristu onse. Choncho akugwiranso ntchito kwa ifeyo, kaya tikuyembekezera kudzapita kumwamba kapena kudzakhala padzikoli.

12. Kodi panali zinthu zatsopano ziti zokhudza ntchito yolalikira?

 12 Taganizirani za lamulo lokhudza kulalikira uthenga wabwino limene Yesu anapatsa otsatira ake. Kale, anthu a mitundu ina ankafunika kupita ku Isiraeli kuti akalambire Yehova. (1 Maf. 8:41-43) Koma tsopano Yesu anapereka lamulo lopezeka pa Mateyu 28:19, 20. (Werengani.) Iye anauza ophunzira ake kuti ‘apite’ kukalalikira kwa anthu onse. Ndiyeno zimene zinachitika pamwambo wa Pentekosite mu 33 C.E. zinasonyeza kuti Yehova akufuna kuti uthenga wabwino ulalikidwe padziko lonse lapansi. Pa nthawiyi, mzimu woyera unathandiza ophunzira 120 kuti alankhule m’zilankhulo zosiyanasiyana kwa Ayuda komanso kwa anthu amene analowa Chiyuda. (Mac. 2:4-11) Patapita nthawi, ophunzirawo ankafunikanso kuti azilalikira kwa Asamariya. Komanso m’chaka cha 36 C.E., tingati gawo linakula chifukwa ankayenera kulalikiranso kwa anthu a mitundu ina, osadulidwa. Apa ndiye kuti Akhristu anayenera kulalikira padziko lonse.

13, 14. (a) Kodi tingatsatire bwanji “lamulo latsopano”? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yesu?

13 Tsopano tiyeni tikambirane za lamulo lachiwiri lija limene Yesu anapereka. Iye anayambitsa “lamulo latsopano” lokhudza mmene tingachitire zinthu ndi abale komanso alongo athu. (Werengani Yohane 13:34, 35.) Potsatira lamuloli, sikuti tiyenera kungokonda abale athu, koma tiyeneranso kuwafera ngati pakufunika kutero. Izi n’zosiyana ndi Chilamulo cha Mose, chomwe sichinkanena kuti tiyenera kufera abale athu.—Mat. 22:39; 1 Yoh. 3:16.

14 Yesu ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi. Iye ankakonda kwambiri ophunzira ake moti mpaka anawafera. Yesu ankafuna kuti ophunzira akewo azichitanso zomwezo. Nafenso tizilolera kuvutika chifukwa cha Akhristu anzathu ndipo tizikhala okonzeka kuwafera.—1 Ates. 2:8.

MALANGIZO AMENE TAPATSIDWA MASIKU ANO KOMANSO A M’TSOGOLO

15, 16. (a) Kodi Yehova amatipatsa bwanji malangizo masiku ano? (b) N’chifukwa chiyani malangizo amene amatipatsa ndi ofunika kwambiri?

15 Yesu wasankha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azipereka chakudya chauzimu kwa otsatira ake “pa nthawi yoyenera.” (Mat. 24:45-47) Chakudyachi chikuphatikizapo malangizo ofunika kwambiri amene timalandira ogwirizana ndi mmene zinthu zilili panopa.

16 Tikukhala ‘m’masiku otsiriza, ndipo posachedwapa kuchitika chisautso chachikulu choti sichinachitikepo. (2 Tim. 3:1; Maliko 13:19) Komanso, Satana ndi ziwanda zake anaponyedwa padzikoli ndipo izi zikuchititsa kuti anthufe tizivutika. (Chiv. 12:9, 12) Kuwonjezera pamenepa, tikugwira ntchito imene Yesu anatilamula yoti tizilalikira kwa anthu a mitundu yonse komanso a zilankhulo zonse.

17, 18. Kodi tizitani Mulungu akatipatsa malangizo?

17 Gulu la Yehova latipatsa zinthu zambiri zimene zingatithandize pa ntchito yolalikira. Kodi mumagwiritsa ntchito zinthu zimenezi? Pamisonkhano yathu yampingo timalandira malangizo okhudza mmene tingagwiritsire ntchito zinthuzi. Kodi inuyo mumaona kuti malangizowa ndi ochokera kwa Yehova?

18 Kuti Mulungu apitirize kutidalitsa, tiyenera kutsatira kwambiri malangizo amene timalandira kudzera mumpingo wachikhristu. Tikamachita zimenezi timafanana ndi madalaivala amene ankatsatira malangizo omwe anali pazikwangwani zija. Tikamamvera malangizo amene Mulungu akutipatsa panopa, zidzakhalanso zosavuta kuti tidzamvere malangizo pa nthawi ya “chisautso chachikulu,” chomwe chidzawononge dziko la Satanali. (Mat. 24:21) Chisautso chachikulu chikadzatha, tidzakhala  m’dziko latsopano ndipo Satana sadzasocheretsanso anthu. Choncho tidzafunikanso malangizo atsopano.

M’Paradaiso, Yehova adzatipatsa malangizo atsopano kudzera m’mipukutu (Onani ndime 19 ndi 20)

19, 20. Kodi ndi mipukutu iti yomwe idzakhalepo m’dziko latsopano, ndipo idzatithandiza bwanji?

19 M’nthawi ya Mose, Yehova anapereka malangizo atsopano kwa Aisiraeli. Kenako anaperekanso malangizo atsopano kumpingo wachikhristu kudzera ‘m’chilamulo cha Khristu.’ Mofanana ndi zimenezi, Baibulo limati m’dziko latsopano Yehova adzatipatsa malangizo kudzera m’mipukutu. (Werengani Chivumbulutso 20:12.) M’mipukutuyi muyenera kuti mudzakhala zimene Yehova adzafune kuti anthu onse, kuphatikizapo oukitsidwa, azidzachita pa nthawiyo. Mipukutu imeneyi idzatithandizanso kuti tidzamudziwe bwino Yehova. Komanso tidzamvetsa bwino zimene Mawu a Mulungu amanena ndipo zimenezi zidzathandiza kuti tizidzakondana komanso kulemekezana kwambiri m’Paradaiso. (Yes. 26:9) Nthawi imeneyo tidzaphunzira zinthu zambiri motsogoleredwa ndi Mfumu yathu, Yesu Khristu.

20 Tikadzamvera ‘zolembedwa m’mipukutu’ n’kukhalabe okhulupirika pa mayesero omaliza, Yehova adzalemba mayina athu ‘mumpukutu wa moyo’ ndipo sadzachotsedwamonso. Zimenezi zikusonyeza kuti adzatipatsa moyo wosatha. Choncho tiyenera kumawerenga Baibulo, kuganizira zimene tawerengazo kuti tizimvetse kenako n’kutsatira zimene taphunzirazo. Tikatero tidzapulumuka pa chisautso chachikulu n’kupitiriza kuphunzira za Yehova Mulungu wathu wanzeru komanso wachikondi mpaka kalekale.—Mlal. 3:11; Aroma 11:33.