Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ezekieli anagwira modzipereka ntchito yokhudza mzinda wa Yerusalemu imene Mulungu anamupatsa

Muzitsanzira Aneneri

Muzitsanzira Aneneri

KODI Akhristufe timafanana bwanji ndi aneneri a Mulungu akale? Mbali yakuti, “Matanthauzo a Mawu Ena” imene ili mu Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi lomwe linatuluka mu 2013, imati mneneri ndi “munthu amene Mulungu amamugwiritsa ntchito pouza ena zimene akufuna kuchita. Aneneri ankauza anthu ulosi wochokera kwa Mulungu, malamulo ake, chiweruzo chake komanso zimene Mulungu amafuna.” Ngakhale kuti ifeyo sitilosera zam’tsogolo, timalankhula ndi anthu m’malo mwa Mulungu ndipo timawauza zimene zili m’Mawu ake.—Mat. 24:14.

Ndi mwayi waukulu kuuza anthu za Mulungu wathu komanso kuwaphunzitsa zimene watilonjeza zokhudza anthu. Timagwira ntchitoyi limodzi ndi ‘mngelo amene akuuluka chapafupi m’mlengalenga.’ (Chiv. 14:6) Koma mwina tingakumane ndi mavuto amene angapangitse kuti tisiye kuganizira za mwayi umene tili nawowu. Mavutowa ndi monga kutopa, zinthu zofooketsa komanso maganizo odziona kuti ndife osafunika. Aneneri akale ankakumananso ndi mavuto, koma sanasiye kutumikira Mulungu. Ndipotu Mulungu anawathandiza kuti akwanitse kugwira ntchito yawo. Tiyeni tikambirane zimene tingachite powatsanzira.

ANKAGWIRA NTCHITO YAWO MWAKHAMA

Nthawi zina tingatope chifukwa cha zimene timachita tsiku lililonse ndipo tingaone kuti sitingathe kupita kolalikira. N’zoona kuti timafunika kupumula, ndipo Yesu ndi ophunzira ake nawonso ankapuma akatopa. (Maliko 6:31) Koma taganizirani zimene zinachitikira Ezekieli ali ku Babulo. Iye ankagwira ntchito yake pakati pa Aisiraeli omwe anali akapolo m’dzikoli. Koma Mulungu anamuuza kuti atenge njerwa n’kujambulapo mzinda wa Yerusalemu. Kenako anamuuza kuti kwa masiku 390 agonere mbali yakumanzere ndipo kwa masiku 40 agonere mbali yakumanja. Kuchita zimenezi kunali ngati kumenyana ndi mzindawo atamanga mpanda womenyera nkhondo kuzungulira mzinda wonsewo. Yehova anauza Ezekieli kuti: “Ine ndidzakumanga ndi zingwe kuti usatembenukire kumbali ina, mpaka utamaliza masiku  ako ozungulira mzindawo.” (Ezek. 4:1-8) Aisiraeli omwe anali ku ukapolowo ayenera kuti ankadabwa ndi zimenezi. Ndipotu Ezekieli anayenera kuchita zimene Yehova anamuuzazi kwa nthawi yoposa chaka. Koma kodi mneneriyu akanakwanitsa bwanji kugwira ntchito yakeyi?

Ezekieli ankadziwa chifukwa chimene Yehova anamutumizira monga mneneri. Tikutero chifukwa pamene ankamutumiza anamuuza kuti: “Kaya [Aisiraeli] akamvetsera kapena ayi,  . . . adzadziwabe kuti pakati pawo panali mneneri.” (Ezek. 2:5) Ezekieli sanaiwale cholinga cha ntchito yake, choncho ankaigwira modzipereka kwambiri. Ndiyeno zimene zinachitika zinasonyeza kuti Ezekieli anali mneneri woona. Iye ndi Aisiraeli amene anali ku ukapolowo analandira uthenga wakuti: “Mzinda uja wawonongedwa!” Apa Aisiraeliwo anadziwa kuti pakati pawo panali mneneri.—Ezek. 33:21, 33.

Masiku ano, nafenso timalalikira kuti posachedwapa dziko la Satanali liwonongedwa. Ngakhale kuti nthawi zina timatopa, timayesetsa kuuza anthu uthenga wa m’Baibulo, kupanga maulendo obwereza komanso kuchititsa maphunziro a Baibulo. Maulosi okhudza mapeto a dzikoli akamakwaniritsidwa, timasangalala podziwa kuti ‘Mulungu akutigwiritsa ntchito pouza ena zimene akufuna kuchita.’

ANKAGWIRABE NTCHITO YAWO NGAKHALE KUTI ENA SANKAMVETSERA

Mzimu wa Yehova umatithandiza kuti tizigwira ntchito yolalikira mwakhama. Komabe nthawi zina tingakhumudwe chifukwa za zimene ena amachita akamva uthenga wathu. Zikatere tizikumbukira chitsanzo cha mneneri Yeremiya. Iye ankauza Aisiraeli uthenga wochokera kwa Mulungu, koma ena ankamunyoza kwambiri. Moti nthawi ina Yeremiya ananena kuti: “Sindidzanenanso za iye ndipo sindidzalankhulanso m’dzina lake.” Izitu zikusonyeza kuti Yeremiya anali munthu ngati ife tomwe. Koma iye anapitirizabe kuuza Aisiraeli uthenga wochokera kwa Mulungu. Pofotokoza chifukwa chake, ananena kuti: “Mumtima mwangamu, mawu ake anali ngati moto woyaka. Anali ngati moto woyaka umene autsekera m’mafupa anga. Choncho ndinatopa ndi kudziletsa kuti ndisalankhule moti sindinathenso kupirira.”—Yer. 20:7-9.

Ifenso tikakhumudwa ndi zimene anthu omwe timawalalikira achita, tiziganizira kufunika kwa uthenga wathu. Tikatero uthengawu udzakhala ngati ‘moto woyaka umene autsekera m’mafupa athu.’ Kuwerenga Baibulo tsiku lililonse kungatithandize kuti tizionabe kuti uthenga wathu ndi wofunika kwambiri.

SANKANGOGANIZIRA ZINTHU ZOFOOKETSA

Akhristu ena akapatsidwa utumiki watsopano amada nkhawa kuti aukwanitsa bwanji komanso sadziwa chifukwa chake apatsidwa utumikiwo. Mwina zoterezi n’zimenenso zinachitikira mneneri Hoseya. Yehova anamuuza kuti: “Pita ukakwatire mkazi amene adzachita dama. Pamenepo udzakhala ndi ana chifukwa cha dama la mkazi wakoyo.” (Hos. 1:2) Kodi inuyo mungatani Mulungu atakuuzani kuti mkazi amene mukufuna kukwatira azidzachita uhule? Kodi mungamukwatirebe? Komatu Hoseya anachita zimene Mulungu anamuuza. Anakwatira Gomeri ndipo patapita nthawi Gomeriyo anabereka mwana wamwamuna. Ndiyeno anaberekanso mwana wamkazi ndipo kenako anabereka winanso wamwamuna. Koma zikuoneka kuti mwana wachiwiri ndi wachitatuyo sanali a Hoseya. Yehova anali atauziratu Hoseya kuti mkazi wakeyo ‘adzathamangira amuna omukonda kwambiri.’ Izi zikusonyeza kuti Gomeri sankachita chigololo ndi mwamuna mmodzi yekha. Koma Yehova ananenanso kuti kenako mkaziyo adzabwerera kwa Hoseya. Kodi mukanakhala Hoseya, mukanalola kuti mubwereranenso ndi mkazi wotereyu? Komatu Yehova anauza mneneriyu kuti abwererane ndi mkazi wakeyo. Hoseya anachitadi zimenezi ndipo kuti zitheke, anachita kumugula mkazi wakeyo modula.—Hos. 2:7; 3:1-5.

Hoseya anachita mokhulupirika zonse zimene Yehova anamuuza, ngakhale kuti mwina ankadabwa kuti n’chifukwa chiyani akumuuza kuti achite zimenezo. Nkhani ya Hoseya imatithandiza kumvetsa mmene Yehova anamvera pamene Aisiraeli anakhala osakhulupirika kwa iye. Komabe Aisiraeli ena analapa n’kubwereranso kwa Yehova.

Masiku ano Yehova sauza aliyense kuti akwatire ‘mkazi wadama.’ Koma tingaphunzire zambiri pa zimene Hoseya anachita. Mfundo imodzi ndi yakuti, tizigwira mokhulupirika ntchito yolalikira Ufumu  “poyera komanso kunyumba ndi nyumba.” (Mac. 20:20) Tiyenera kuchita zimenezi ngakhale zitakhala kuti ifeyo timaona kuti n’zovuta. Mwina pali njira zina zolalikirira zimene zimakuvutani. Mwachitsanzo, pali anthu ena amene ankasangalala kuphunzira Baibulo ndi a Mboni komabe ankati sangapite kukalalikira kunyumba ndi nyumba. Koma patapita nthawi, ambiri a anthuwa anayamba kulalikira. Izi zikusonyeza kuti, ngati ndife odzipereka kwa Yehova tikhoza kuchita utumiki umene poyamba tinkaona kuti sitingaukwanitse.

Pali zinanso zimene tingaphunzire kwa Hoseya. Iye akanatha kuyamba kupereka zifukwa n’cholinga choti asachite zimene Yehova anamuuza. Komanso Hoseya akanapanda kulemba nkhani yakeyi sitikanadziwa zimene zinachitika. Ifenso nthawi zina tingakhale ndi mwayi woti tiuze ena za Yehova ndipo palibe amene angadziwe za mwayi umenewo. Izi n’zimene zinachitikira mtsikana wina wa ku United States dzina lake Anna. Ali kusekondale, aphunzitsi ake anauza ana onse a m’kalasi mwawo kuti alembe nkhani. Anati aliyense alembe nkhani imene amakhulupirira ndipo afotokoze mfundo zosonyeza kuti nkhaniyo ndi yoonadi. Anna anaona kuti apa Mulungu wamupatsa mpata woti alalikire. Komabe anadziwa kuti ana ena a m’kalasimo akhoza kutsutsa zimene angalembe. Choncho anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize kuchita zinthu molimba mtima. Kenako analemba nkhani yonena kuti zamoyo sizinasinthe kuchokera ku zinthu zina koma zinachita kulengedwa.

Achinyamata a Mboni amatsanzira aneneri ndipo amauza ena za Mlengi wathu molimba mtima

Pamene Anna ankawerenga nkhani yakeyi, mtsikana wina amene ankakhulupirira kwambiri kuti zamoyo sizinachite kulengedwa anamufunsa mafunso ambirimbiri. Koma Anna anayankha bwinobwino mafunso onsewo. Aphunzitsi ake anachita chidwi kwambiri ndipo anamupatsa mphoto chifukwa anaona kuti mfundo zake zinali zoona. Kuchokera nthawi imeneyo, Anna ankakambirana ndi mtsikana wotsutsa uja nkhani yokhudza chilengedwe. Anna anati: “Panopa ndimalalikira uthenga wabwino molimba mtima.” Izi zinatheka chifukwa choti analimba mtima n’kugwira ntchito imene Yehova anamupatsa.

N’zoona kuti si ife aneneri, koma tikamatsanzira mtima wodzipereka wa aneneri monga Ezekieli, Yeremiya komanso Hoseya tidzatha kugwira bwino ntchito iliyonse imene Yehova angatipatse. Mukhoza kuwerenga nkhani za aneneri ena pa kulambira kwanu kwa pabanja kapena pophunzira Baibulo panokha. Kenako mungaganizire zimene mungachite potengera chitsanzo chawo.