Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizikonda ndi Mtima Wonse Chuma Chimene Mulungu Watipatsa

Tizikonda ndi Mtima Wonse Chuma Chimene Mulungu Watipatsa

“Pakuti kumene kuli chuma chanu, mitima yanunso idzakhala komweko.”—LUKA 12:34.

NYIMBO: 153, 104

1, 2. (a) Tchulani zinthu zitatu zamtengo wapatali zimene Yehova watipatsa. (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

YEHOVA ndi wachuma kwambiri kuposa wina aliyense. (1 Mbiri 29:11, 12) Koma popeza ali ndi mtima wopatsa, amagawira anthu ake mowolowa manja chuma chauzimu. Timayamikira kwambiri kuti Yehova watipatsa (1) Ufumu wa Mulungu, (2) utumiki umene umapulumutsa anthu komanso (3) mfundo zamtengo wapatali zomwe zimapezeka m’Mawu ake. Koma kupanda kusamala, tikhoza kusiya kuyamikira chuma chamtengo wapatalichi ndipo zingakhale ngati tachitaya. Choncho tiyenera kuteteza zinthu zamtengo wapatalizi pozigwiritsa ntchito bwino komanso kupitiriza kuzikonda kwambiri. Paja Yesu anati: “Kumene kuli chuma chanu, mitima yanunso idzakhala komweko.”Luka 12:34.

2 Tiyeni tione zimene tingachite kuti tiziyamikira komanso kukonda kwambiri Ufumu, utumiki wathu komanso choonadi. Tikamakambirana zimenezi, muziganizira zimene inuyo mungachite kuti muzikonda kwambiri zinthuzi.

 UFUMU WA MULUNGU ULI NGATI NGALE YAMTENGO WAPATALI

3. Kodi wamalonda wa mufanizo la Yesu analolera kuchita chiyani kuti agule ngale yapamwamba kwambiri? (Onani chithunzi choyambirira.)

3 Werengani Mateyu 13:45, 46. Yesu anafotokoza fanizo la wamalonda amene ankafunafuna ngale. Munthuyo ayenera kuti ankagula ndiponso kugulitsa ngale zambiri. Koma mufanizoli anapeza ngale yamtengo wapatali kwambiri moti atangoiona anasangalala. Ndipo kuti agule ngaleyo analolera kugulitsa zonse zimene anali nazo. Apa n’zoonekeratu kuti munthuyo ankaona kuti ngaleyo inali yamtengo wapatali kwambiri.

4. Tikamakonda Ufumu wa Mulungu ngati mmene wamalonda uja ankakondera ngale ija, kodi tidzachita chiyani?

4 Kodi tikuphunzira chiyani mufanizoli? Ufumu wa Mulungu uli ngati ngale yamtengo wapatali. Tikamaukonda ngati mmene wamalonda uja ankakondera ngale ija, tidzalolera kusiya zonse zimene tili nazo n’cholinga choti tikhale nzika ya Ufumuwo. (Werengani Maliko 10:28-30.) Tiyeni tsopano tikambirane za anthu awiri amene anachita zimenezi.

5. Kodi Zakeyu anasonyeza bwanji kuti ankakonda kwambiri Ufumu wa Mulungu?

5 Zakeyu anali mkulu wa okhometsa misonkho ndipo anapeza chuma chambiri chifukwa chobera anthu. (Luka 19:1-9) Komabe atamva Yesu akulalikira za Ufumu, anazindikira kufunika kwa zimene anamvazo ndipo nthawi yomweyo anasintha. Iye ananena kuti: “Ambuye, ine ndipereka ndithu hafu ya chuma changa kwa osauka. Ndipo chilichonse chimene ndinalanda munthu aliyense pomunamizira mlandu ndibweza kuwirikiza kanayi.” Zakeyu anagawadi chuma chimene anachipeza mwachinyengo ndipo anasiya mtima wadyera.

6. Kodi mlongo wina anasintha zinthu ziti ataphunzira Baibulo, ndipo n’chifukwa chiyani anasintha?

6 Chitsanzo chachiwiri ndi cha mlongo wina amene tangomupatsa dzina loti Rose. Zaka zingapo zapitazo anamva uthenga wa Ufumu koma pa nthawiyo anali pa chibwenzi ndi mkazi mnzake. Iye analinso pulezidenti wa bungwe lomenyera ufulu wa anthu ofuna kuti amuna okhaokha kapena akazi okhaokha azikwatirana. Koma atayamba kuphunzira Baibulo anazindikira kuti mfundo zokhudza Ufumu wa Mulungu ndi zofunika kwambiri. Kenako anaona kuti afunika kusintha kwambiri moyo wake. (1 Akor. 6:9, 10) Iye anatula pansi udindo wake uja komanso anathetsa chibwenzi chake. Rose anabatizidwa mu 2009 ndipo chaka chotsatira anayamba upainiya wokhazikika. Iye amakonda kwambiri Yehova ndi Ufumu wake kuposa zinthu zina zonse zimene ankakonda poyamba.Maliko 12:29, 30.

7. Kodi tingatani kuti tisasiye kukonda Ufumu wa Mulungu?

7 Ambirife tasinthanso zinthu zambiri pa moyo wathu kuti tikhale nzika za Ufumu wa Mulungu. (Aroma 12:2) Komatu ntchito idakalipo. Tiyenera kukhala tcheru nthawi zonse kuti mtima wathu usayambe kukonda zinthu zina monga chuma kapena chiwerewere. (Miy. 4:23; Mat. 5:27-29) Tiyeni tikambirane mphatso ina yamtengo wapatali imene Yehova watipatsa yomwe ingatithandize kuti tizikondabe Ufumu wa Mulungu.

UTUMIKI WATHU UMENE UMAPULUMUTSA ANTHU

8. (a) N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti utumiki wathu uli ngati ‘chuma chimene chili m’zonyamulira zoumbidwa ndi dothi’? (b) Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti ankakonda utumiki?

8 Yesu watipatsa ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mat. 28:19, 20) Mtumwi Paulo ankaona kuti utumiki wokhudza pangano latsopano ndi wofunika kwambiri. Iye ananena kuti uli ngati ‘chuma chimene chili m’zonyamulira  zoumbidwa ndi dothi.’ (2 Akor. 4:7; 1 Tim. 1:12) Anthufe tili ngati zonyamulira zoumbidwa ndi dothi chifukwa si ife angwiro, koma uthenga umene timalalikira ukhoza kuthandiza ifeyo komanso anthu ena kuti adzapeze moyo wosatha. Paulo ankazindikira mfundo imeneyi ndipo ananena kuti: “Koma ndikuchita zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndiugawirenso kwa ena.” (1 Akor. 9:23) Paulo ankachita khama kwambiri pa ntchito yophunzitsa anthu chifukwa choti ankakonda utumiki. (Werengani Aroma 1:14, 15; 2 Timoteyo 4:2.) Zimenezi zinamuthandizanso kuti apirire pa nthawi imene ankatsutsidwa kwambiri. (1 Ates. 2:2) Kodi ifenso tingasonyeze bwanji kuti timakonda utumiki?

9. Tchulani njira zina zimene tingasonyezere kuti timakonda utumiki.

9 Paulo ankakhala tcheru nthawi zonse kuti aone mpata woti alalikire ndipo iyi ndi njira ina imene anasonyezera kuti ankakonda utumiki. Mofanana ndi atumwi komanso Akhristu ena oyambirira, timalalikira mwamwayi, m’malo opezeka anthu ambiri komanso kunyumba ndi nyumba. (Mac. 5:42; 20:20) Ngati n’zotheka, tingawonjezere utumiki wathu, mwina pochita upainiya wothandiza kapena wokhazikika. Tikhozanso kuphunzira chilankhulo china, kusamukira kudera lina kapenanso kudziko lina.Mac. 16:9, 10.

10. Kodi Irene wadalitsidwa bwanji chifukwa cholalikira uthenga wabwino mwakhama?

10 Chitsanzo china pa nkhaniyi ndi cha mlongo wina wa ku United States dzina lake Irene, yemwe sali pa banja. Mlongoyu ankafunitsitsa kulalikira kwa anthu olankhula Chirasha amene anasamukira m’dzikolo. Iye anayamba kulalikira anthu amenewa mu 1993 ndipo pa nthawiyo mumzinda wa New York munali kagulu kachirasha ka ofalitsa 20 okha. Panopa, patha zaka pafupifupi 20 Irene akutumikira mwakhama m’gawoli. Komabe iye anati: “Mpaka pano pali mawu ambiri achirasha amene sindikuwadziwa.” Ngakhale zili choncho, Yehova wadalitsa kwambiri khama lake komanso la anthu ena amene adzipereka kwambiri. Panopa, mumzinda wa New York muli mipingo 6 yachirasha. Pa anthu amene Irene anaphunzira nawo, 15 anabatizidwa ndipo ena panopa akutumikira pa Beteli, ena ndi apainiya ndipo ena ndi akulu. Irene ananena kuti: “Ndikaganizira zinthu zina zimene ndikanachita pa moyo wanga ndimaona kuti sizikanandithandiza kukhala wosangalala ngati mmene zilili panopa.” Kunena zoona, mlongoyu amakonda kwambiri utumiki.

Kodi mumaona kuti utumiki ndi wofunika kwambiri? Nanga zimene mumachita mlungu uliwonse zimasonyeza zimenezi? (Onani ndime 11 ndi 12)

11. Kodi chimachitika n’chiyani tikamalalikirabe ngakhale kuti anthu akutizunza?

11 Ngati timakonda kwambiri utumiki wathu, tidzatsanzira Paulo n’kumalalikira ngakhale pamene tikutsutsidwa. (Mac. 14:19-22) Cha m’ma 1930 ndi m’ma 1940, abale  athu ku United States ankatsutsidwa kwambiri. Koma mofanana ndi Paulo, sanasiye kulalikira ndipo anayesetsa kumenyera ufulu wochitira zimenezi m’makhoti. Mu 1943, M’bale Nathan H. Knorr anafotokoza za mlandu wina umene tinawina kukhoti lalikulu kwambiri la ku United States kuti: “Timawina milandu chifukwa cha khama lanu. Abale akanasiya kulalikira si bwenzi kukhoti lalikululi kuli milandu. Koma chifukwa choti abale ndi alongo inu mukulalikirabe mwakhama padziko lonse ndipo simungasiye, tikutha kugonjetsa anthu amene akutizunza. Kusagonja kwa anthu a Mulungu kumeneku n’komwe kwathandiza kuti mlanduwu tiuwine.” Zinthu ngati zimenezi zachitikanso m’mayiko osiyanasiyana. Apa zikuonekeratu kuti kukonda utumiki kumathandiza kuti tigonjetse anthu amene amatizunza.

12. Kodi inuyo mukufunitsitsa kuchita chiyani pa nkhani ya utumiki?

12 Ngati timaona kuti utumiki ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Yehova, sitilalikira n’cholinga choti tingopeza maola. M’malomwake, timachita chilichonse chimene tingathe kuti ‘tichitire umboni mokwanira za uthenga wabwino.’ (Mac. 20:24; 2 Tim. 4:5) Koma kodi ndi mfundo ziti zimene timaphunzitsa anthu? Funso limeneli likutifikitsa pa chuma china chimene Mulungu watipatsa.

MFUNDO ZA M’BAIBULO ZAMTENGO WAPATALI

13, 14. Kodi “chuma” chimene Yesu anatchula pa Mateyu 13:52 n’chiyani, ndipo tingachiwonjezere bwanji?

13 Chinthu china chamtengo wapatali chimene Mulungu watipatsa ndi mfundo za m’Baibulo. Yehova ndi Mulungu wachoonadi. (2 Sam. 7:28; Sal. 31:5) Iye ndi Atate wowolowa manja ndipo amathandiza anthu amene amamuopa kuti adziwe mfundo za m’Baibulo. Kuyambira nthawi imene tinayamba kuphunzira choonadi takhala tikuphunzira mfundo zofunika kwambiri kuchokera m’Baibulo, mabuku athu, misonkhano yampingo komanso ikuluikulu. Choncho mogwirizana ndi zimene Yesu ananena, tili ndi mfundo zachoonadi zakale ndiponso zatsopano zomwe takhala tikuika ‘mosungiramo chuma chathu.’ (Werengani Mateyu 13:52.) Tikamafunafuna mfundozi ngati chuma chobisika, Yehova amatithandiza kupeza mfundo zamtengo wapatali zatsopano zomwe tingaikenso ‘mosungiramo chuma chathu.’ (Werengani Miyambo 2:4-7.) Koma kodi tingachite chiyani kuti tiwonjezere mfundozi?

14 Tiyenera kukhala ndi ndandanda yabwino yophunzira komanso kufufuza zinthu m’Baibulo ndi m’mabuku athu. Izi zingatithandize kuphunzira mfundo “zatsopano” zomwe sitinkazidziwa. (Yos. 1:8, 9; Sal. 1:2, 3) Nsanja ya Olonda yoyambirira imene inasindikizidwa mu July 1879 inanena kuti: “Choonadi chili ngati duwa lomwe lazunguliridwa ndi udzu wambiri umene ukhoza kulipha. Kuti munthu apeze duwalo ayenera kufufuza kwambiri . . . ndipo kuti likhale lake ayenera kuwerama n’kulitenga. Koma tisamangokhutira ndi mfundo imodzi yokha yachoonadi. . . . Nthawi zonse tizifufuza mfundo zina.” Malinga ndi zimene magaziniyi inanena, tiyenera kuyesetsa kuwonjezera mfundo zina ‘mosungiramo chuma chathu.’

15. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mfundo zina ndi “zakale,” nanga ndi mfundo ziti zimene zimakusangalatsani kwambiri?

15 Titangoyamba kuphunzira Mawu a Mulungu tinapeza mfundo zina zamtengo wapatali. Tinganene kuti mfundozi ndi “zakale” chifukwa takhala tikuzidziwa kuchokera pamene tinayamba choonadi. Kodi mfundo zina zimene tinaphunzira ndi ziti? Tinaphunzira kuti Yehova ndi amene anatilenga ndipo ali nafe cholinga. Tinaphunziranso kuti Mulungu amatikonda kwambiri moti anapereka nsembe ya dipo ya Mwana wake n’cholinga choti timasuke ku uchimo ndi imfa. Komanso tinaphunzira kuti  Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto athu onse ndipo tidzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha m’dziko lamtendere.Yoh. 3:16; Chiv. 4:11; 21:3, 4.

16. Kodi tiyenera kuchita chiyani kafotokozedwe ka mfundo zina kakasintha?

16 Nthawi zina kafotokozedwe ka mfundo zina za m’Baibulo kakhoza kusintha. Izi zikachitika tiyenera kuphunzira mfundozi mosamala komanso kuziganizira kwambiri. (Mac. 17:11; 1 Tim. 4:15) Zimenezi zingatithandize kumvetsa bwino mfundo zikuluzikulu komanso zing’onozing’ono zimene zasintha. Tikamatero timakhala kuti tikusunga bwinobwino mfundozi mosungiramo chuma chathu. Koma kodi ubwino wochita zimenezi ndi wotani?

17, 18. Kodi mzimu woyera ungatithandize bwanji?

17 Yesu ananena kuti mzimu wa Mulungu ukhoza kutikumbutsa mfundo zimene tinaphunzira. (Yoh. 14:25, 26) Kodi zimenezi zingatithandize bwanji tikamaphunzitsa anthu uthenga wabwino? Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira M’bale Peter. Mu 1970, anali atangoyamba kumene kutumikira pa Beteli ku Britain ndipo n’kuti ali ndi zaka 19. Tsiku lina akulalikira kunyumba ndi nyumba anakumana ndi bambo winawake wandevu zake. Peter anafunsa bamboyo ngati akufuna kudziwa bwino Baibulo. Popeza bamboyo ankadziona kuti amadziwa Baibulo, anadabwa n’kunena kuti onse m’nyumbayo ndi arabi achiyuda. Pofuna kumuyesa, bamboyo anafunsa kuti: “Mnyamata iwe, kodi buku la Danieli linalembedwa m’chilankhulo chanji?” Peter anayankha kuti: “Mbali ina inalembedwa m’Chiaramu.” Iye atafotokoza zimenezi, rabiyo anadabwa kuti Peter akudziwa yankho la funsolo. Nayenso Peter anadabwa kwambiri kuti wadziwa bwanji yankholo. Atafika kunyumba anafufuza m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amene anawerenga ndipo anapeza nkhani yofotokoza kuti mbali ina ya buku la Danieli inalembedwa m’Chiaramu. (Dan. 2:4) Izi zikusonyezeratu kuti mzimu woyera ungatithandize kukumbukira zinthu zimene tinawerenga kale n’kuziika mosungiramo chuma chathu.Luka 12:11, 12; 21:13-15.

18 Ngati timakonda kwambiri nzeru zochokera kwa Yehova, tingafunitsitse kuwonjezera mfundo zatsopano ndi zakale mosungiramo chuma chathu. Tikapitiriza kukonda ndiponso kuyamikira nzeru za Yehova tidzakhala aphunzitsi abwino a Mawu a Mulungu.

MUZITETEZA CHUMA CHANU

19. N’chifukwa chiyani tiyenera kuteteza kwambiri chuma chimene Mulungu watipatsa?

19 Kupanda kusamala, Satana ndi dziko loipali akhoza kutichititsa kuti tisiye kuyamikira chuma chimene takambirana munkhaniyi. N’zosavuta kutengeka chifukwa chofuna ntchito yabwino, moyo wawofuwofu komanso kudzionetsera ndi zinthu zimene tili nazo. Koma mtumwi Yohane anatichenjeza kuti dzikoli likupita limodzi ndi chilakolako chake. (1 Yoh. 2:15-17) Choncho tiyenera kusamala kwambiri kuti tisayambe kukonda zinthu za m’dzikoli. M’malomwake, tiyeni tipitirize kukonda komanso kuyamikira chuma chimene Mulungu watipatsa.

20. Kodi inuyo mudzatani kuti muteteze chuma chimene Mulungu wakupatsani?

20 Tiyeni tizipewa chilichonse chimene chingatilepheretse kukonda kwambiri Ufumu wa Mulungu. Tizilalikira modzipereka ndiponso tisasiye kuona kuti utumiki wathu ndi wofunika kwambiri. Tiyeneranso kupitiriza kufufuza mwakhama mfundo za m’Baibulo. Tikamachita zimenezi ndiye kuti tikusunga ‘chuma chosatha kumwamba, kumene mbala singafikeko, ndipo njenjete singawononge. Pakuti kumene kuli chuma chathu, mitima yathunso idzakhala komweko.’Luka 12:33, 34.