NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) June 2017

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa July 31 mpaka August 27, 2017.

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa.

Yehova Amatitonthoza M’masautso Athu Onse

Kodi ndi mavuto ati amene Akhristu amakumana nawo m’banja masiku ano? Ngati mukukumana ndi mavuto amenewa kodi Mulungu angakulimbikitseni bwanji?

Tizikonda ndi Mtima Wonse Chuma Chimene Mulungu Watipatsa

Kodi ndi chuma chiti chimene tiyenera kuchikonda ndi mtima wonse ndipo tingachite bwanji zimenezi?

Tisamaweruze Anthu Chifukwa cha Maonekedwe Awo

Kodi chinachitika n’chiyani wa Mboni za Yehova wina atalalikira kwa munthu amene ankangoyendayenda mumsewu

Kodi Mumathetsa Kusamvana N’kukhazikitsa Mtendere?

Anthu amalakalaka kukhala mwamtendere. Koma akaona kuti anthu ena sakuwalemekeza kapena kulemekeza udindo wawo, amayamba kuchita zinthu zosokoneza mtendere. Kodi inuyo mungapewe bwanji zimenezi?

“Udalitsike Chifukwa cha Kulingalira Bwino Kwako!”

Davide ndi amene analankhula mawu amenewa pamene ankayamikira Abigayeli. N’chifukwa chiyani anayamikira Abigayeli nanga ife tikuphunzira chiyani pa zimene Abigayeli anachita?

Musamaiwale Nkhani Yofunika Kwambiri

Kodi nkhani yofunika kwambiri ndi iti? Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuikumbukira nthawi zonse?

Muzikhala Kumbali ya Ulamuliro wa Yehova

Kodi chimachitika n’chiyani munthu akazindikira mfundo yoti Yehova yekha ndi amene ali woyenera kulamulira chilengedwe chonse?

Kodi Mukudziwa?

Kodi amalonda amene ankagulitsa nyama kukachisi mu Yerusalemu analidi ngati “achifwamba”?