Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Yehova Mulungu Wathu Ndi Yehova Mmodzi”

“Yehova Mulungu Wathu Ndi Yehova Mmodzi”

“Tamverani, Aisiraeli inu: Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.”—DEUT. 6:4.

NYIMBO: 138, 112

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mawu a pa Deuteronomo 6:4 ndi odziwika kwambiri? (b) N’chifukwa chiyani Mose analankhula mawu amenewa?

KWA zaka zambiri, Ayuda akhala akugwiritsa ntchito mawu a pa Deuteronomo 6:4 popemphera tsiku lililonse, m’mawa ndi madzulo. M’Chiheberi, vesili limayamba ndi mawu oti Shema ndipo pempheroli limangodziwikanso kuti Shema. Akamanena pempheroli, Ayuda amasonyeza kuti ndi odzipereka kwa Mulungu yekha basi.

2 Mawu a vesi limeneli ananena ndi Mose m’chaka cha 1473 B.C.E. potsanzikana ndi Aisiraeli m’chigwa cha Mowabu. Aisiraeli anali atatsala pang’ono kuwoloka mtsinje wa Yorodano kuti akalandire Dziko Lolonjezedwa. (Deut. 6:1) Mose anali atawatsogolera kwa zaka 40, ndipo ankafuna kuti iwo akhale olimba mtima. Aisiraeli ankafunika kukhulupirira Yehova Mulungu wawo ndiponso kumumvera. Mawu a Mosewa ayenera kuti anawalimbikitsa kwambiri. Mose atatchula Malamulo Khumi komanso  malamulo ena, ananena mawu a pa Deuteronomo 6:4, 5. (Werengani.)

3. Kodi tikambirana mafunso ati m’nkhaniyi?

3 Pa nthawiyo Aisiraeli ankadziwa kale kuti Mulungu amene amamulambira ndi “Yehova ndi mmodzi” ndipo ndi Mulungu wa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo. Nanga n’chifukwa chiyani Mose anawauza kuti Yehova Mulungu wawo ndi “Yehova mmodzi”? Kodi mfundo yoti Yehova ndi mmodzi ikugwirizana bwanji ndi mfundo ya vesi 5 yoti tizimukonda ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse ndi mphamvu zathu zonse? Nanga ifeyo tikuphunzira chiyani pa mawu a pa Deuteronomo 6:4, 5?

KODI MAWU OTI YEHOVA NDI MMODZI AMATANTHAUZA CHIYANI?

4, 5. (a) Kodi mawu oti “Yehova mmodzi” amatanthauza chiyani? (b) Kodi Yehova ndi wosiyana bwanji ndi milungu ina?

4 Ndi wapadera. Mawu oti “Yehova mmodzi” amatanthauza kuti iye ndi wapadera ndipo palibenso wofanana naye. Zikuoneka kuti Mose sananene mawuwa potsutsa chiphunzitso cha Utatu. Iye ankakumbutsa Aisiraeli kuti ayenera kulambira Yehova yekha chifukwa ndi amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi ndipo ndi Mfumu ya chilengedwe chonse. Iye yekha ndi Mulungu woona ndipo palibenso mulungu wina amene angafanane naye. (2 Sam. 7:22) Iwo sankayenera kutsanzira anthu a mitundu ina amene ankalambira milungu yosiyanasiyana. Anthuwa ankakhulupirira kuti milungu yawoyo imayang’anira zinthu zosiyanasiyana.

5 Mwachitsanzo, Aiguputo ankalambira mulungu wadzuwa wotchedwa Ra komanso mulungu wa mitambo wotchedwa Nut. Analinso ndi mulungu wadziko dzina lake Geb komanso wa mtsinje wa Nailo wotchedwa Hapi. Iwo ankalambiranso nyama zosiyanasiyana. Yambiri mwa milunguyi, Yehova anaiwononga pamene anagwetsera Aiguputo miliri 10. Mulungu wotchuka wa Akanani anali Baala. Ameneyu anali mulungu wobereketsa yemwenso nthawi zina ankamuona kuti ndi mulungu wa mitambo, wa mvula komanso wa mphepo. M’madera enanso anthu ankakhulupirira kuti Baala amawateteza. (Num. 25:3) Koma Aisiraeli anayenera kukumbukira kuti Mulungu wawo ndi “Yehova mmodzi.”—Deut. 4:35, 39.

6, 7. Kodi mawu oti “Yehova mmodzi” angatanthauzenso chiyani?

6 Ndi wokhulupirika ndipo sasintha. Mawu oti “Yehova mmodzi” amatanthauzanso kuti zolinga ndi zochita zake sizisintha. Iye sasinthasintha kapena kulonjeza zina n’kuchita zina. Nthawi zonse ndi wokhulupirika ndipo amanena zoona. Mwachitsanzo, iye anauza Abulahamu kuti ana ake adzakhala m’Dziko Lolonjezedwa ndipo anachita zozizwitsa kuti akwaniritse lonjezoli. Ngakhale kuti panadutsa zaka 430, iye anakwaniritsabe zimene analonjezazo.—Gen. 12:1, 2, 7; Eks. 12:40, 41.

7 Patapita zaka mahandiredi angapo, Yehova anauza Aisiraeli kuti iwo ndi mboni zake ndipo ananena kuti: “Ine sindinasinthe. Ine ndisanakhaleko kunalibe Mulungu amene anapangidwa.” Ananenanso kuti: “Nthawi zonse ine sindisintha.” (Yes. 43:10, 13; 44:6; 48:12) Kunena zoona, Aisiraeli komanso ifeyo tili ndi mwayi wolambira Mulungu amene sasintha ndipo ndi wodalirika nthawi zonse.—Mal. 3:6; Yak. 1:17.

8, 9. (a) Kodi Yehova amafuna kuti anthu amene amamulambira azichita chiyani? (b) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti mawu amene Mose ananena ndi ofunika kwambiri?

8 Mose anakumbutsa Aisiraeli kuti Yehova  sasintha ndipo nthawi zonse ankawakonda komanso kuwasamalira. Choncho, iwonso anafunika kulambira iye yekha komanso kum’konda ndi mtima wawo wonse, moyo wawo wonse komanso mphamvu zawo zonse. Ananso ankafunika kuchita chimodzimodzi chifukwa makolo awo ankayenera kuwaphunzitsa kuti azikonda Yehova.—Deut. 6:6-9.

9 Popeza Yehova sasintha, n’zodziwikiratu kuti zimene ankafuna kuti Aisiraeli azichita pa nkhani yolambira n’zimene amafunanso kuti ife tizichita. Kuti Mulungu azivomereza kulambira kwathu, tiyenera kulambira iye yekha komanso kumukonda ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse ndi mphamvu zathu zonse. Ndipotu Yesu Khristu anatchulanso mfundo yomweyi. (Werengani Maliko 12:28-31.) Tsopano tiyeni tione zimene tingachite posonyeza kuti timakhulupirira zoti “Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.”

TIZIDZIPEREKA KWA YEHOVA YEKHA

10, 11. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalambira Yehova yekha? (b) Kodi anyamata achiheberi anasonyeza bwanji kuti ankalambira Yehova yekha pamene anali ku Babulo?

10 Kuti Yehova akhale Mulungu wathu mmodzi yekha, m’pofunika kumalambira iye yekha basi. Anthu amene amalambira Yehova sayenera kukhulupiriranso maganizo kapena miyambo yabodza. Tizikumbukira kuti iye yekha ndiye Mulungu woona komanso wamphamvu amene tiyenera kumulambira.—Werengani Chivumbulutso 4:11.

11 M’buku la Danieli muli nkhani ya Danieli, Hananiya, Misayeli ndi Azariya, omwe anali anyamata achiheberi. Iwo anakana kudya zakudya zodetsedwa komanso kulambira fano la Nebukadinezara. Apa anasonyeza kuti ankalambira Yehova yekha. Anyamatawa ankaona kuti Yehova ndi wofunika kuposa chilichonse ndipo anakhalabe okhulupirika kwa iye.—Dan. 1:1–3:30.

12. Pa nkhani yolambira Yehova yekha, kodi tiyenera kusamala ndi chiyani?

12 Kuti tizilambira Yehova yekha, tiyenera kusamala kuti tisalole chilichonse kulowa m’malo mwa iye. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatilepheretse kulambira Yehova yekha? Pa Malamulo Khumi aja, panali lamulo loti Aisiraeli asamalambire mafano kapena milungu ina. (Deut. 5:6-10) Masiku ano, kulambira mafano kungachitike m’njira zosiyanasiyana ndipo njira zina n’zovuta kuzizindikira. Koma zimene Yehova amafuna sizinasinthe ndipo iye adakali “Yehova mmodzi.” Tiyeni tsopano tikambirane zimene tingachite kuti tisamalambire mafano.

13. Kodi tingayambe kukonda zinthu ziti koposa Yehova?

13 Pa Akolose 3:5 (werengani), pali malangizo otithandiza kupewa zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Lembali likunena kuti kusirira kwa nsanje kuli ngati kulambira mafano. Izi zili choncho chifukwa munthu akamasirira chuma kapena zinthu zina n’kumazilakalaka, amayamba kuona kuti zinthuzo n’zofunika kwambiri kuposa Mulungu. Ndiponso zinthu zonse zimene zatchulidwa palembali n’zogwirizana ndi kusirira kwa nsanje. Munthu amene amachita zinthu zimenezi amakhala kuti akulambira mafano chifukwa zimamulepheretsa kuti azikonda Yehova ndi mtima wonse. Choncho tisalole chilichonse kutilepheretsa kukhala odzipereka kwa “Yehova mmodzi.”

14. Kodi mtumwi Yohane anapereka chenjezo lotani?

14 Mtumwi Yohane anafotokozanso bwino  mfundoyi pamene ananena kuti ngati munthu akukonda zinthu za m’dziko “ndiye kuti sakonda Atate.” Zina mwa zinthu za m’dzikozi ndi monga “chilakolako cha thupi, chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake.” (1 Yoh. 2:15, 16) Choncho tiyenera kudzifufuza nthawi zonse kuti tione ngati tayamba kukonda zinthu za m’dziko pa nkhani ya zosangalatsa, anthu ocheza nawo ndiponso mafashoni. Komanso kukonda zinthu za m’dziko kungachititse munthu kufuna “zinthu zazikulu,” mwina kudzera m’maphunziro apamwamba. (Yer. 45:4, 5) Panopa, tatsala pang’ono kulowa m’dziko latsopano. Choncho ndi bwino kuti tizikumbukira mawu a Mose aja. Ngati timakhulupirira ndi mtima wonse kuti “Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi,” tidzayesetsa kuchita zonse zomwe tingathe kuti tizimutumikira m’njira imene amavomereza.—Aheb. 12:28, 29.

TIZIGWIRIZANA NDI AKHRISTU ANZATHU

15. N’chifukwa chiyani Paulo anakumbutsa Akhristu kuti Mulungu wathu ndi “Yehova mmodzi”?

15 Mawu oti Yehova mmodzi amatithandizanso kudziwa kuti iye amafuna kuti atumiki ake azigwirizana ndiponso azimutumikira ndi cholinga chimodzi. Mumpingo wachikhristu woyambirira munali Ayuda, Agiriki, Aroma komanso anthu a mitundu ina. Poyamba anthuwa anali osiyana zikhulupiriro, miyambo komanso zokonda. Zimenezi zinachititsa kuti anthu ena azivutika kulambira Mulungu m’njira yovomerezeka. Ankavutikanso kuti asiye zinthu zina zimene ankachita poyamba.  Choncho mtumwi Paulo anawakumbutsa kuti Akhristu onse ali ndi Mulungu mmodzi, Yehova.—Werengani 1 Akorinto 8:5, 6.

16, 17. (a) Kodi ndi ulosi uti umene ukukwaniritsidwa masiku ano ndipo zotsatira zake ndi zotani? (b) Kodi n’chiyani chimene chingasokoneze mgwirizano wathu?

16 Nanga kodi zinthu zili bwanji mumpingo wachikhristu masiku ano? Mneneri Yesaya ananeneratu kuti “m’masiku otsiriza,” anthu ochokera m’mitundu yonse adzayamba kulambira Yehova. Iwo adzanena kuti: ‘[Yehova] adzatiphunzitsa njira zake, ndipo ife tidzayenda m’njira zakezo.’ (Yes. 2:2, 3) Ndi zosangalatsa kuona kuti ulosiwu ukukwaniritsidwa masiku ano. M’mipingo mumapezeka abale ndi alongo a mitundu, zilankhulo komanso zikhalidwe zosiyanasiyana. Koma tonse timalambira Yehova mogwirizana. Komabe kupanda kusamala, kusiyana kumeneku kungabweretse mavuto ena.

Kodi inuyo mumathandiza kuti mpingo wanu uzigwirizana? (Onani ndime 16 mpaka 19)

17 Mwachitsanzo, kodi mumawaona bwanji abale ndi alongo achikhalidwe chosiyana kwambiri ndi chanu? Mwina mumasiyana nawo kwambiri chilankhulo, zovala, makhalidwe komanso chakudya chimene mumakonda. Kodi mumawapewa n’kumangocheza ndi anthu achikhalidwe chofanana ndi chanu? Nanga mumatani ngati abale amene akukuyang’anirani ndi aang’ono kapena ndi a mtundu wosiyana ndi wanu? Kodi mumalola kuti kusiyana kumeneku kusokoneze mgwirizano wathu?

18, 19. (a) Kodi palemba la Aefeso 4:1-3 pali malangizo otani? (b) Kodi tingatani kuti mpingo wathu ukhalabe wogwirizana?

18 Kodi tingatani kuti zimenezi zisatichitikire? Paulo anapereka malangizo othandiza kwambiri kwa Akhristu amene ankakhala mumzinda wotukuka wa Efeso, momwe munkakhala anthu osiyanasiyana. (Werengani Aefeso 4:1-3.) Palembali, Paulo anatchula makhalidwe monga kudzichepetsa, kufatsa, kuleza mtima komanso chikondi. Makhalidwe amenewa ali ngati zipilala zothandiza kuti nyumba ikhale yolimba. Komabe kuti nyumba isagwe, pamafunika kuikonza nthawi ndi nthawi. Ndiyeno Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Efeso kuti aziyesetsa ndi mtima wonse ‘kusunga umodzi mothandizidwa ndi mzimu woyera.’

19 Tonsefe tiyenera kuyesetsa kuti tizilimbikitsa mgwirizano mumpingo. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Choyamba tiyenera kukhala ndi makhalidwe amene Paulo anatchula aja. Kenako tiyenera kuyesetsa ‘kukhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chotigwirizanitsa.’ Kusamvetsetsana kuli ngati ming’alu imene ingatilepheretse kugwirizana ndi abale ndi alongo athu. Choncho tiyeni tiziyesetsa kuthetsa kusamvana kuti tipitirize kukhala mwamtendere ndiponso mogwirizana.

20. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikudziwa zoti “Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi”?

20 Mfundo yoti “Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi” ndi yofunika kwambiri. Inathandiza Aisiraeli kupirira mavuto osiyanasiyana polowa m’Dziko Lolonjezedwa. Ifenso tikamakumbukira mfundo imeneyi, tidzatha kupirira mavuto amene tingakumane nawo pa chisautso chachikulu n’kulowa m’Paradaiso. Choncho tiyeni tipitirize kulambira Yehova yekha basi. Tizimukonda ndiponso kumutumikira ndi mtima wonse komanso tiziyesetsa kukhalabe ogwirizana. Tikamachita zimenezi tidzaona kukwaniritsidwa kwa mawu a Yesu, onena za anthu omwe adzaweruzidwe kuti ndi nkhosa akuti: “Bwerani, inu amene mwadalitsidwa ndi Atate wanga. Lowani mu ufumu umene anakonzera inu kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.”—Mat. 25:34.