Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalidwe la Mtengo Wapatali Kuposa Dayamondi

Khalidwe la Mtengo Wapatali Kuposa Dayamondi

Kwa nthawi yaitali, anthu akhala akuona kuti miyala ya dayamondi ndi ya mtengo wapatali. Ina mwa miyala imeneyi imagulitsidwa ndalama zambirimbiri. Komatu pali chinthu china chimene Mulungu amachiona kuti ndi chamtengo wapatali kuposa miyala ngati dayamondi.

 Wofalitsa wosabatizidwa wina dzina lake Haykanush, amakhala ku Armenia, ndipo tsiku lina anatola pasipoti pafupi ndi nyumba yake. Mkati mwa pasipotiyo munali makadi a kubanki komanso ndalama zambiri. Iye anauza mwamuna wake yemwenso anali wofalitsa wosabatizidwa.

Banjali linali ndi mavuto aakulu azachuma komanso ngongole zambiri. Komabe iwo anabweza ndalamazi kwa mwiniwake pogwiritsa ntchito adiresi yomwe inali papasipotiyo. Munthu amene anataya zinthuzi limodzi ndi banja lake anadabwa kwambiri ndi zimene zinachitikazi. Haykanush ndi mwamuna wake anafotokozera banjalo kuti zimene amaphunzira m’Baibulo n’zimene zawathandiza kukhala oona mtima n’kubweza ndalamazo. Iwo anapezerapo mwayi wowafotokozera za Mboni za Yehova komanso anawapatsa mabuku.

Munthu amene anataya zinthuzi ankafuna kupatsa Haykanush ndalama koma iye anakana. Tsiku lotsatira, mkazi wa munthuyo anapita kunyumba kwa Haykanush atamutengera mphete ya dayamondi pomuthokoza chifukwa cha zimene anachita.

Mofanana ndi banjali, anthu ambiri angadabwe chifukwa cha zimene Haykanush ndi mwamuna wake anachitazi. Koma kodi zimenezi zinamudabwitsanso Yehova? Kodi iye anamva bwanji ndi zimene anthuwa anachita? Kodi kuona mtima kwawoku kunali ndi phindu lililonse?

MAKHALIDWE OFUNIKA KWAMBIRI KUPOSA CHUMA

Mayankho a mafunso amenewa ndi osavuta. Tikutero chifukwa chakuti Akhristu amadziwa kuti makhalidwe abwino ndi ofunika kwambiri pamaso pa Yehova kuposa miyala ya mtengo wapatali kapena chuma chilichonse. Maganizo a Yehova pa nkhani ya zinthu zamtengo wapatali ndi osiyana ndi a anthu. (Yes. 55:8, 9) Akhristu amaonanso kuti kukhala ndi makhalidwe a Yehova ndi chinthu chamtengo wapatali.

Taonani zimene Baibulo limanena pa nkhani ya nzeru ndi kuzindikira. Lemba la Miyambo 3:13-15 limati: “Wodala ndi munthu amene wapeza nzeru, ndiponso munthu amene wapeza kuzindikira, chifukwa kupeza nzeru monga phindu n’kwabwino kuposa kupeza siliva monga phindu, ndipo kukhala nazo monga zokolola n’kwabwino kuposa kukhala ndi golide. N’zamtengo wapatali kuposa miyala ya korali, ndipo zonse zimene umakonda sizingafanane nazo.” Apa zikuonekeratu kuti Yehova amaona kuti makhalidwe amenewa ndi ofunika kwambiri kuposa chuma chilichonse.

Nanga kodi Yehova amaona bwanji khalidwe la kuona mtima?

Baibulo limanena kuti Yehova “sanganame” choncho ndi woona mtima. (Tito 1:2) Iye anauziranso Paulo kuti alembere Akhristu achiheberi malangizo akuti: “Pitirizani kutipempherera, pakuti tikukhulupirira kuti tili ndi chikumbumtima choona, popeza tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”—Aheb. 13:18.

Nayenso Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Pa nthawi ina, Mkulu wa Ansembe dzina lake Kayafa anamuuza kuti: “Ndikukulumbiritsa pali Mulungu wamoyo, utiuze ngati ndiwedi Khristu Mwana wa Mulungu.” Yesu anayankha moona mtima kuti iyeyo ndi Mesiya. Anachita zimenezi ngakhale kuti ankadziwa kuti mfundo imeneyi ichititsa khoti lalikulu kumuweruza kuti wanyoza Mulungu ndipo ayenera kuphedwa.—Mat. 26:63-67.

 Kodi inuyo mumayesetsa kuchita zinthu moona mtima? Nanga mungatani ngati mpata utapezeka woti mungosintha mawu enaake pang’ono n’cholinga choti mupeze ndalama?

KUKHALA WOONA MTIMA N’KOVUTA

M’masiku otsiriza ano, ndi zovuta kukhala oona mtima chifukwa anthu ambiri ndi ‘odzikonda komanso okonda ndalama.’ (2 Tim. 3:2) Mavuto azachuma ndiponso kusowa kwa ntchito, zikupangitsa anthu ambiri kuchita chinyengo. Ambiri amaona kuti ngati pali mwayi wa ndalama kapena chuma palibe vuto kuba, kunama kapena kuchita zinthu zina zachinyengo. Akhristu enanso awononga mbiri yawo mumpingo chifukwa chofuna “kupeza phindu mwachinyengo.—1 Tim. 3:8; Tito 1:7.

Komabe Akhristu ambiri amatsanzira Yesu. Iwo amazindikira kuti kukhala ndi makhalidwe abwino n’kofunika kwambiri kuposa chilichonse. Choncho Akhristu amene ali pasukulu saonera mayeso n’cholinga choti akhoze bwino. (Miy. 20:23) N’zoona kuti si nthawi zonse pamene timathokozedwa chifukwa chokhala oona mtima. Koma Mulungu amasangalala nafe tikakhala oona mtima ndiponso timakhala ndi chikumbumtima chabwino.

Chitsanzo pa nkhaniyi, ndi zimene zinachitikira munthu wina dzina lake Gagik. Iye anati: “Ndisanakhale Mkhristu ndinkagwira ntchito pakampani inayake yaikulu. Mwiniwake wa kampaniyo anapeza njira yoti asamalipire ndalama zambiri za msonkho. Popeza ndinali wamkulu pakampanipo, ndinkapereka ziphuphu kwa olandira ndalama za misonkho. Zimenezi zinachititsa kuti ndizidziwika kuti ndine wachinyengo. Ndiyeno nditaphunzira Baibulo, ndinasiya ntchitoyi ngakhale kuti inkandipezetsa ndalama zambiri. M’malomwake ndinatsegula kampani yanga. Ndipo ndinalembetsa zonse kuboma komanso ndinkapereka misonkho yonse.”—2 Akor. 8:21.

Gagik ananenanso kuti: “Panopa ndimapeza ndalama zochepa kwambiri moti zimandivuta kupezera banja langa zinthu zofunika. Komabe, ndine wosangalala podziwa kuti ndikusangalatsa Yehova. Ndikupereka chitsanzo chabwino kwa ana anga ndiponso ndili ndi mwayi wokhala ndi udindo mumpingo. Anthu oyang’anira za misonkho aja ndiponso amene ndimagwira nawo ntchito amandiona kuti ndine woona mtima.”

YEHOVA ANGATITHANDIZE

Yehova amakonda kwambiri anthu amene amamumvera n’kumasonyeza makhalidwe abwino monga kuona mtima. (Tito 2:10) Paja iye anauzira Davide kulemba kuti: “Ndinali mwana, ndipo tsopano ndakula, koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha chakudya.”—Sal. 37:25.

Chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndi Rute. Iye anapita limodzi ndi apongozi ake okalamba ku Isiraeli n’kukayamba kulambira Mulungu woona. (Rute 1:16, 17) Atafika ku Isiraeliko, Rute ankagwira ntchito mwakhama ndipo anali woona mtima. Iye ankatsatira zimene Chilamulo chinkanena pa nkhani yokunkha. Yehova anaonetsetsa kuti Rute ndi Naomi akupeza zinthu zofunika pa moyo wawo. (Rute 2:2-18) Koma pali zinanso zimene Yehova anachitira Rute. Anamusankha kuti akhale m’gulu la makolo a Davide komanso Mesiya wolonjezedwa.—Rute 4:13-17; Mat. 1:5, 16.

 Akhristu ena amavutika kwambiri kuti apeze zofunika pa moyo. Koma m’malo mochita chinyengo, amagwira ntchito mwakhama. Apa amasonyeza kuti kukhala ndi makhalidwe a Yehova monga kuona mtima, n’kofunika kwambiri kuposa chilichonse.—Miy. 12:24; Aef. 4:28.

Mofanana ndi Rute, Akhristu ambiri amakhulupirira kuti Yehova aziwathandiza. Amadziwa kuti iye analonjeza kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheb. 13:5) Yehova amathandizadi anthu ovutika amene amayesetsa kuchita zinthu moona mtima nthawi zonse. Amakwaniritsa lonjezo lake loti azitithandiza kupeza zofunika pa moyo.—Mat. 6:33.

Anthu amaona kuti miyala monga dayamondi ndi yamtengo wapatali. Koma Yehova amaona kuti makhalidwe abwino monga kuona mtima ndi amtengo wapatali kuposa chilichonse.

Tikamachita zinthu moona mtima timakhala ndi chikumbumtima chabwino ndipo timalalikira momasuka