Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tisasiye Kutumikira Mulungu Chifukwa cha Zochita za Ena

Tisasiye Kutumikira Mulungu Chifukwa cha Zochita za Ena

“Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.”AKOL. 3:13.

NYIMBO: 121, 75

1, 2. Kodi ndi ulosi uti wa m’Baibulo umene unaneneratu kuti atumiki a Yehova adzawonjezeka?

GULU la Mboni za Yehova ndi gulu lapadera padziko lonse. N’zoona kuti anthu ake si angwiro ndipo amalakwitsa zinthu zina. Koma Mulungu amawatsogolera ndi mzimu wake woyera kuti gulu lawo lizikula komanso zinthu ziziyenda bwino. Tiyeni tione zinthu zina zimene Yehova wakhala akuchita pothandiza anthu ake ngakhale kuti si angwiro.

2 Pamene masiku otsiriza ankayamba mu 1914, atumiki a Mulungu padzikoli anali ochepa kwambiri. Koma Yehova anadalitsa ntchito yawo yolalikira ndipo m’zaka zotsatira, anthu mamiliyoni anayamba kuphunzira Baibulo n’kukhala Mboni za Yehova. Yehova ananeneratu zimenezi pamene anati: “Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu. Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi pa nthawi yake.” (Yes. 60:22) Ulosi umenewu ukukwaniritsidwa masiku otsiriza ano moti pali mayiko ambiri padziko lapansi amene  chiwerengero cha anthu ake n’chochepa poyerekezera ndi cha Mboni za Yehova padziko lonse.

3. Kodi atumiki a Mulungu anasonyeza bwanji chikondi?

3 M’masiku otsiriza ano, Yehova wathandizanso anthu ake kuti azitsanzira kwambiri khalidwe lake la chikondi. (1 Yoh. 4:8) Yesu amatsanzira Mulungu pa nkhaniyi ndipo anauza otsatira ake kuti: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. . . . Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:34, 35) A Mboni za Yehova anasonyeza chikondi chimenechi pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Pa nthawiyi, anthu okwana 55 miliyoni anaphedwa. Koma a Mboni sanamenye nawo nkhondoyi. (Werengani Mika 4:1, 3.) Zimenezi zinawathandiza kuti akhalebe ‘oyera pa mlandu wa magazi a anthu onse.’—Mac. 20:26.

4. N’chifukwa chiyani n’zochititsa chidwi kuti chiwerengero cha anthu a Yehova chikuwonjezeka?

4 Anthu a Mulungu akuwonjezeka ngakhale kuti akukhala m’dziko limene wolamulira wake ndi Satana. Baibulo limati iye ndi “mulungu wa nthawi ino.” (2 Akor. 4:4) Satana amagwiritsa ntchito anthu andale komanso ofalitsa nkhani kuti alepheretse ntchito yolalikira, koma zimenezi sizingatheke. Komabe podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa, Satana akuyesetsa kuchititsa anthu kuti asiye kulambira Mulungu ndipo akugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana.—Chiv. 12:12.

KODI MUDZAKHALABE OKHULUPIRIKA?

5. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa anthu ena akatikhumudwitsa? (Onani chithunzi patsamba 23.)

5 Gulu la Yehova limatilimbikitsa kuti tizikonda kwambiri Mulungu komanso anzathu. Yesu anasonyeza kuti tiyeneradi kuchita zimenezi. Mwachitsanzo, munthu wina atamufunsa za lamulo lalikulu kwambiri anayankha kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba. Lachiwiri lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’” (Mat. 22:35-39) Koma Baibulo limanena kuti anthufe tinatengera uchimo wa Adamu choncho si ife angwiro. (Werengani Aroma 5:12, 19.) Izi zingachititse kuti anthu ena alankhule kapena kuchita zinthu zotikhumudwitsa. Kupanda kusamala, zoterezi zingachititse kuti tisiye kukonda Yehova ndi anthu ake. Kodi inuyo mungatani wina atakukhumudwitsani? M’Baibulo muli nkhani zosonyeza kuti atumiki a Mulungu ena analankhula kapena kuchita zinthu zimene zinakhumudwitsa anzawo. Tiyeni tikambirane zimene tikuphunzira pa zimenezi.

Kodi mukanatani mukanakhala ku Isiraeli pamene Eli ankalekerera ana ake? (Onani ndime 6)

6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Eli ankalephera kudzudzula ana ake?

6 Mwachitsanzo, Eli, yemwe anali Mkulu wa Ansembe, anali ndi ana awiri amene sankatsatira malamulo a Yehova. Baibulo limati: “Ana aamuna a Eli anali anthu opanda pake. Iwo anali kunyalanyaza Yehova.” (1 Sam. 2:12) Ngakhale kuti bambo awo ankalimbikitsa kulambira koona, anawa ankachita machimo akuluakulu. Eli ankadziwa zimene anawa ankachita koma ankangowalekerera osawadzudzula mwamphamvu. Izi zinachititsa kuti Mulungu alange banja lonse la Eli ndipo anthu a m’banja lake anasiya kukhala akulu a ansembe. (1 Sam. 3:10-14) Kodi inuyo mukanatani mukanakhalapo pa nthawi imene Eli ankalekerera ana akewa? Kodi mukanakhumudwa mpaka kufika posiya kutumikira Mulungu?

7. Kodi Davide anachita machimo ati, nanga Mulungu anatani?

 7 Yehova ankakonda kwambiri Davide moti ananena kuti iye anali “munthu wapamtima pake.” (1 Sam. 13:13, 14; Mac. 13:22) Koma kenako Davide anachita chigololo ndi Bati-seba, mkazi wa Uriya, ndipo mkaziyu anatenga pakati. Izi zinachitika mwamuna wake ali kunkhondo. Mwamunayo atabwera, Davide anamuuza kuti apite kwawo n’cholinga choti akagone ndi mkazi wakeyo. Anachita izi kuti tchimo lakelo lisaonekere. Koma Uriya anakana ndipo Davide anakonza zoti iye aphedwe kunkhondo. Izi zinabweretsa mavuto aakulu m’banja la Davide. (2 Sam. 12:9-12) Koma Mulungu anamuchitira chifundo n’kumukhululukira chifukwa choti ankayesetsa kumutumikira ndi “mtima wosagawanika.” (1 Maf. 9:4) Kodi inuyo mukanakhala ku Isiraeli pa nthawiyo mukanatani? Kodi mukanasiya kutumikira Mulungu chifukwa cha zimene Davide anachitazi?

8. (a) Kodi mtumwi Petulo analakwitsa zinthu ziti? (b) N’chifukwa chiyani Yehova anapitirizabe kumugwiritsa ntchito?

8 Chitsanzo china ndi cha mtumwi Petulo. Yesu anamusankha kuti akhale mmodzi wa atumwi. Koma pa nthawi ina Petulo anachita zinthu zimene ananong’oneza nazo bondo. Mwachitsanzo, ananena kuti ngakhale atumwi enawo atamusiya Yesu, iye sadzamusiya. (Maliko 14:27-31, 50) Koma pamene Yesu ankagwidwa, atumwi onse, ndi Petulo yemwe, anamuthawa. Komanso iye anakana katatu zoti amadziwa Yesu. (Maliko 14:53, 54, 66-72) Komabe Petulo analapa machimo akewa ndipo Yehova anapitiriza kumugwiritsa ntchito. Inuyo mukanakhala mmodzi wa ophunzira pa nthawiyo, kodi mukanatani? Kodi mukanasiya kutumikira Mulungu chifukwa cha zimene Petulo anachitazi?

9. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kuti nthawi zonse Yehova amachita zoyenera?

 9 M’Baibulo muli nkhani za atumiki a Yehova ambiri amene anachita zinthu zimene zinakhumudwitsa ena, ndipo apa tangokambirana zitsanzo zochepa chabe. Zimenezi zimachitikanso masiku ano. Koma nkhani yagona pakuti, kodi mungatani zoterezi zitachitika? Kodi mungasiye kutumikira Yehova komanso kusonkhana? Kapena mungazindikire kuti Yehova ndi wachifundo ndipo angapereke mpata kwa munthuyo woti alape? Nanga mumakhulupirira kuti iye amakonza zinthu pa nthawi yake komanso moyenera? Nthawi zinanso munthu amene wachita tchimo angasonyeze kuti sakuzindikira kulakwa kwake ndipo sangalape. Zikatere, kodi mungakhale ndi chikhulupiriro choti Yehova adzaweruza munthuyo pa nthawi yake mwinanso kuchititsa kuti achotsedwe?

MUSASIYE YEHOVA NDI GULU LAKE

10. Kodi Yesu anatani ngakhale kuti Yudasi Isikariyoti ndi Petulo anamukhumudwitsa?

10 M’Baibulo muli zitsanzo za atumiki a Mulungu amene anakhalabe okhulupirika ngakhale kuti anthu ena anachita zolakwika. Mwachitsanzo, Yesu atapemphera usiku wonse anasankha atumwi ake 12. Mmodzi mwa atumwiwa anali Yudasi Isikariyoti. Koma patapita nthawi Yudasiyo anamupereka komanso Petulo anamukana. Komabe Yesu Khristu sanalole kuti zimenezi zisokoneze ubwenzi wake ndi Yehova. (Luka 6:12-16; 22:2-6, 31, 32) Iye ankadziwa kuti vuto ndi anthuwa, osati Yehova kapena anthu ake. Choncho anapitirizabe kugwira ntchito yake. Yehova anamudalitsa pomuukitsa n’kumupatsa mwayi woti adzakhale Mfumu ya Ufumu wakumwamba.—Mat. 28:7, 18-20.

11. Kodi Baibulo linaneneratu chiyani zokhudza anthu a Mulungu?

11 Chitsanzo cha Yesu chikutiphunzitsa kuti nafenso tiyenera kukhulupirira Yehova komanso anthu ake. Ndipotu tikaona zimene Yehova akuchita kudzera mwa atumiki ake masiku otsiriza ano, timasowa chonena. Mwachitsanzo, ndife ogwirizana ndipo tikukwanitsa kulalikira padziko lonse. Koma anthu ena satha kuchita zimenezi chifukwa alibe mzimu wa Yehova. Lemba la Yesaya 65:14 limafotokoza mmene zinthu zilili pakati pa anthu a Mulungu. Limati: “Atumiki anga adzafuula mokondwa chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima.”

12. Kodi sitiyenera kuchita chiyani anthu ena akamachita zolakwika?

12 Anthu a Yehovafe timasangalala kwambiri chifukwa Yehova amatitsogolera komanso amatithandiza kuchita zambiri. Koma anthu a m’dziko la Satanali sizikuwayendera bwino chifukwa zinthu zikungoipiraipira. Choncho si bwino kuimba mlandu Yehova kapena gulu lake chifukwa cha zimene Akhristu ena angalakwitse. Tizikhalabe okhulupirika kwa Yehova n’kumatsatira malangizo ake. Tiyeneranso kudziwa zoyenera kuchita anthu ena akatikhumudwitsa.

ZIMENE TIYENERA KUCHITA

13, 14. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kukhumudwa kwambiri ndi zolakwa za ena? (b) Kodi tiyenera kukumbukira lonjezo liti?

13 Ndiye kodi tizitani ngati Mkhristu wina walankhula kapena kuchita zinthu zotikhumudwitsa? Tiyenera kutsatira mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Usamafulumire kukwiya mumtima mwako, pakuti anthu opusa ndi amene sachedwa kupsa mtima.” (Mlal. 7:9) Tizikumbukira kuti anthu anasiya kukhala  angwiro zaka 6,000 zapitazo, choncho tonse timalakwitsa zinthu zambiri. Ndiye si bwino kuyembekezera kuti ena azichita bwino chilichonse. Si nzerunso kusiya kusangalala ndi Akhristu anzathu chifukwa cha zolakwa za ena. Kungakhalenso kulakwa kwambiri ngati titafika posiya gulu la Yehova chifukwa chokhumudwa. Tikutero chifukwa chakuti zimenezi zingatitayitse mwayi wotumikira Mulungu komanso wodzapeza moyo wosatha m’dziko latsopano.

14 Kuti tizikhalabe osangalala komanso tisataye mtima, tiyenera kukumbukira lonjezo la Yehova lakuti: “Pakuti ndikulenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.” (Yes. 65:17; 2 Pet. 3:13) Tiyeni tisalole kuti zolakwa za ena zitilepheretse kudzalandira madalitso amenewa.

15. Kodi Yesu ananena kuti tizitani ena akatilakwira?

15 Popeza sitinalowe m’dziko latsopano, tiyenera kutsatira malangizo a Yehova okhudza zimene tingachite ngati ena atikhumudwitsa. Mwachitsanzo, tizikumbukira mfundo imene Yesu ananena yakuti: “Mukamakhululukira anthu machimo awo, inunso Atate wanu wakumwamba adzakukhululukirani. Koma ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate wanu sadzakukhululukirani machimo anu.” Komanso Petulo atafunsa ngati tiyenera kukhululuka maulendo 7, Yesu ananena kuti: “Ndikukuuza kuti, osati nthawi 7 zokha ayi, koma, mpaka nthawi 77.” Apa Yesu ankatanthauza kuti tizikhala ndi mtima wokhululuka nthawi zonse.—Mat. 6:14, 15; 18:21, 22.

16. Kodi Yosefe anapereka chitsanzo chotani?

16 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yosefe. Azichimwene ake 10 ankamuda kwambiri chifukwa choti bambo awo ankamukonda. Anafika pomugulitsa n’kukakhala kapolo ku Iguputo. Kumeneko iye ankalimbikira kwambiri ntchito moti kenako mfumu ya ku Iguputo inamusankha kukhala wachiwiri wake. Pamene kunagwa njala, azichimwene ake a Yosefe anapita ku Iguputo kuti akagule chakudya ndipo sanamuzindikire m’bale wawoyo. Apatu Yosefe akanatha kuwabwezera zimene anamuchitira. Koma iye sanatero m’malomwake anangowayesa kuti aone ngati anasintha. Ataona kuti anasintha, Yosefe anadziulula kwa azichimwene akewo. Patapita nthawi anawalimbikitsa kuti: “Musachite mantha. Ine ndipitiriza kukugawirani chakudya limodzi ndi ana anu.”—Gen. 50:21.

17. Kodi tizitani anthu ena akatilakwira?

17 Tizikumbukiranso kuti tonsefe tingalakwitse zinazake ndipo tingathe kukhumudwitsa ena. Choncho tikazindikira kuti takhumudwitsa munthu wina, tiyenera kutsatira malangizo a m’Baibulo oti tizipita kwa munthuyo n’kukakambirana naye. (Werengani Mateyu 5:23, 24.) Timasangalala anthu ena akatikhululukira choncho nafenso tizichita chimodzimodzi. Lemba la Akolose 3:13 limatilimbikitsa kuti: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.” Pa 1 Akorinto 13:5, Baibulo limasonyeza kuti ngati timakondadi abale athu, sitingawasungire zifukwa. Ndipotu Yehova amatikhululukira ngati nafenso timakhululukira ena. Choncho ena akatilakwira tizitsanzira Atate wathu wachifundo amene amatikhululukira.—Werengani Salimo 103:12-14.