Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutamanda Yehova?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutamanda Yehova?

‘Kutamanda Ya n’kosangalatsa komanso koyenera.’—SAL. 147:1.

NYIMBO: 104, 152

1-3. (a) Kodi zikuoneka kuti Salimo 147 linalembedwa liti? (b) Kodi tingaphunzire chiyani pa salimoli?

ANTHUFE timakonda kuyamikira munthu akagwira bwino ntchito inayake, kapena akasonyeza makhalidwe abwino kwambiri. Ngati timachita zimenezi ndi anthu, kuli bwanji Yehova Mulungu? Tiyenera kumutamanda chifukwa ali ndi mphamvu zopanda malire ndipo tikayang’ana zinthu zodabwitsa zimene analenga timaona umboni wa mphamvuzo. Tiyeneranso kumutamanda chifukwa cha chikondi chake ndipo umboni wa chikondicho timauona tikaganizira zoti anapereka Mwana wake kuti akhale dipo lotipulumutsa.

2 Munthu amene analemba Salimo 147 anaona kuti ndi bwino kutamanda Yehova. Iye analimbikitsanso anthu ena kuti azitamanda Mulungu.​—Werengani Salimo 147:1, 7, 12.

3 Sitikudziwa kuti amene analemba salimoli ndi ndani. Koma zikuoneka kuti munthuyu anali ndi moyo pa nthawi imene Aisiraeli anabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo ku Babulo. (Sal. 147:2) Munthu amene analemba salimoli ayenera kuti ankatamanda Yehova chifukwa choyamikira kuti Aisiraeli anabwerera kumalo  amene angathe kulambira Mulungu woona. Iye anatchulanso zifukwa zina zomveka zotamandira Yehova. Kodi zifukwa zake ndi ziti? Nanga inuyo muli ndi zifukwa ziti zonenera kuti “Tamandani Ya”?​—Sal. 147:1.

YEHOVA AMACHIRITSA ANTHU OSWEKA MTIMA

4. (a) Kodi Aisiraeli ayenera kuti anamva bwanji atamasulidwa ndi Koresi? (b) N’chifukwa chiyani mwayankha choncho?

4 Kodi inuyo mukuganiza kuti Aisiraeli ankamva bwanji ali ku Babulo? Anthu a ku Babuloko ankawaseka kuti: “Tatiimbireni nyimbo imodzi ya ku Ziyoni.” Pa nthawiyi mzinda wa Yerusalemu umene unkachititsa Aisiraeli kutamanda kwambiri Yehova unali utawonongedwa. (Sal. 137:1-3, 6) Choncho Ayudawo sankafuna kuimba ngakhale pang’ono. Mitima yawo inali itasweka ndipo chimene ankafuna ndi kulimbikitsidwa basi. Mogwirizana ndi ulosi wa m’Mawu a Mulungu, Mfumu ya ku Perisiya dzina lake Koresi inawapulumutsa. Koresi anagonjetsa Babulo n’kulengeza kuti: “Yehova . . . wandituma kuti ndim’mangire nyumba ku Yerusalemu. . . . Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Yehova Mulungu wake akhale naye. Choncho apite.” (2 Mbiri 36:23) Aisiraeli amene anali ku Babulo ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri atamva mawu amenewa.

5. Kodi wolemba Salimo 147 ananena kuti Yehova amathandiza bwanji anthu?

5 Sikuti Yehova ankangolimbikitsa Aisiraeli monga gulu koma ankalimbikitsanso aliyense payekha. Ndi mmene amachitiranso masiku ano. Wolemba Salimo 147 uja ananena kuti Mulungu “amachiritsa anthu osweka mtima, ndipo amamanga zilonda zawo zopweteka.” (Sal. 147:3) Izi zikusonyeza kuti Yehova amasamalira anthu amene akudwala komanso amene ali ndi nkhawa. Masiku anonso, Yehova amafunitsitsa kutitonthoza komanso kutilimbikitsa tikakhala ndi nkhawa. (Sal. 34:18; Yes. 57:15) Iye amatipatsa nzeru komanso mphamvu kuti tithe kupirira vuto lililonse limene tingakumane nalo.​—Yak. 1:5.

6. Kodi zimene wolemba salimo anafotokoza zokhudza kumwamba pa Salimo 147:4, zingatithandize bwanji? (Onani chithunzi choyambirira.)

6 Kenako, wolemba salimoyo anayamba kufotokoza zakumwamba. Iye ananena kuti Yehova “amawerenga nyenyezi zonse, ndipo zonsezo amazitchula mayina ake.” (Sal. 147:4) Mwina mukudabwa kuti n’chifukwa chiyani anangosintha nkhaniyi n’kuyamba kufotokoza zakumwamba? Taganizirani izi: Munthu amene analemba salimoli ankatha kuona nyenyezi koma sankadziwa kuti zilipo zingati. Panopa chiwerengero cha nyenyezi zimene anthu angathe kuziona chawonjezereka kwambiri. Ena amanena kuti mlalang’amba wathu wotchedwa Milky Way uli ndi nyenyezi mabiliyoni ambiri. Komatu milalang’ambayo ilipo yambirimbiri m’chilengedwechi. Choncho m’pomveka kunena kuti nyenyezi zilipo zosawerengeka. Koma Mlengi wathu amatha kupereka dzina kwa nyenyezi iliyonse. Izi zikusonyeza kuti Yehova amaona kuti nyenyezi iliyonse ndi yosiyana ndi inzake. (1 Akor. 15:41) Nanga bwanji za anthufe? Ngati Yehova amadziwa pamene pali nyenyezi iliyonse pa nthawi ina iliyonse ndiye kuti amadziwanso za munthu aliyense payekha. Izi zikutanthauza kuti amadziwa kumene muli, mmene mukumvera mumtima mwanu komanso chimene mukufunikira pa nthawi ina iliyonse.

7, 8. (a) Kodi Yehova akamathandiza athu ake amakumbukira chiyani? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Yehova amathandiza anthu mwachifundo.

7 Sikuti Yehova amangodziwa bwino za inuyo panokha. Iye ndi wamphamvu komanso wachifundo moti angathe kukuthandizani pa vuto lanu lililonse. (Werengani Salimo 147:5.) Mwina nthawi zina mumaganiza kuti mavuto anu ndi aakulu kwambiri moti simungathe kuwapirira. Koma Yehova ndi wanzeru ndipo amadziwa zimene simungakwanitse komanso ‘amakumbukira  kuti ndinu fumbi.’ (Sal. 103:14) Popeza si ife angwiro, timalakwitsa zinthu nthawi ndi nthawi. Timadandaula pamene talankhula mawu olakwika, kuchita zinthu zolakwika kapena kusirira zimene anthu ena ali nazo. Yehova alibe mavuto ngati amenewa koma amatimvetsa bwino kwambiri.​—Yes. 40:28.

8 Mwina inuyo panokha mwaona Yehova akukuthandizani pa vuto linalake. (Yes. 41:10, 13) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Kyoko amene akuchita upainiya. Pa nthawi ina, mlongoyu anakhumudwa kwambiri atapita kudera lina. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti anamvetsa mavuto ake? Mlongoyu anapeza kuti abale ndi alongo akumeneko ankamumvetsa kwambiri. Anamva ngati Yehova akumuuza kuti: “Ndimakukonda kwambiri, osati chifukwa choti ndiwe mpainiya basi, koma chifukwa choti ndiwe mwana wanga komanso unadzipereka kwa ineyo. Ndiwe Mboni yanga ndipo ndimafuna kuti uzisangalala ponditumikira.” Kodi inuyo mukukumbukira nthawi ina pa moyo wanu pamene Wamphamvuyonse anasonyeza kuti “nzeru zake zilibe malire”?

YEHOVA AMATIPATSA ZIMENE TIMAFUNIKIRA

9, 10. Kodi Yehova akafuna kutithandiza amayamba ndi chiyani? Perekani chitsanzo.

9 Kodi ndi zinthu ziti zimene timafunikira pa moyo wathu? Nthawi zina timada nkhawa kuti mwina sitingapeze chakudya chokwanira. Koma tiyenera kukumbukira kuti Yehova ndi amene amachititsa kuti mvula igwe n’kumeretsa zinthu, n’cholinga choti ngakhale chakudya ‘chimene akhwangwala amalirira’ chizipezeka. (Werengani Salimo 147:8, 9.) Ngati Yehova amasamalira akhwangwala, kodi angalephere kukuthandizani kuti mupeze zofunika pa moyo wanu?​—Sal. 37:25.

10 Koma chofunika kwambiri n’chakuti Yehova amatithandiza mwauzimu. Iye amatipatsa “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Afil. 4:6, 7) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale Mutsuo ndi mkazi wake. Iwo anaona Yehova akuwalimbikitsa madzi atasefukira ku Japan mu 2011. Madziwo anachuluka kwambiri moti iwo anathawira padenga la nyumba yawo koma zinthu zawo zonse zinawonongeka. Madziwo atachepa, anakagona m’chipinda cham’mwamba cha nyumba yawo yomwe inali itawonongeka. Kutacha anayamba kufufuza chilichonse chimene chingawalimbikitse mwauzimu. Kenako anapeza Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2006. Nthawi yomweyo anapeza nkhani yofotokoza za chivomezi chimene chinachitika mu 2004 ku Sumatra. Chivomezichi chinali chachikulu kwambiri chifukwa chinachititsa kuti madzi asefukire mpaka kufika mayiko ena. Mutsuo ndi mkazi wake ankalira pamene ankawerenga zomwe zinachitikazo. Iwo anaona kuti Yehova wawapatsa thandizo labwino pa nthawi yoyenera. Yehova anawathandizanso kupeza zofunika pa moyo. Iwo analandira chithandizo kuchokera kwa abale ndi alongo. Koma chimene chinawathandiza kwambiri ndi kubwera kwa abale otumizidwa ndi gulu la Yehova kuti adzawalimbikitse. Mutsuo anati: “Zinali ngati Yehova wabwera n’kukhala pafupi ndi munthu aliyense n’kumamusamalira. Tinalimbikitsidwa kwambiri.” Yehova amayamba watilimbikitsa mwauzimu kenako n’kutipatsa zinthu zina zofunika pa moyo wathu.

KODI TINGATANI KUTI MULUNGU AZITITHANDIZA?

11. Kodi munthu amene akufuna kuti Yehova azimuthandiza ayenera kuchita chiyani?

11 Yehova amakhala wokonzeka nthawi zonse kuti ‘athandize anthu ofatsa.’ (Sal. 147:6a) Koma kodi ifeyo tingatani kuti Mulungu azitithandiza? Chofunika ndi kukhala naye pa ubwenzi. Kuti zimenezi zitheke tiyenera kuyesetsa kukhala anthu ofatsa. (Zef. 2:3) Munthu wofatsa amayembekezera Yehova kuti akonze zolakwika komanso athetse mavuto amene wakumana nawo. Ndiyeno Yehova amasangalala kwambiri ndi anthu oterewa.

12, 13. (a) Ngati tikufuna kuti Yehova azitithandiza, kodi tiyenera kupewa chiyani? (b) Kodi Yehova amasangalala ndi anthu otani?

 12 Koma Malemba amati Mulungu ‘amagwetsera pansi anthu oipa.’ (Sal. 147:6b) Mawuwatu ndi amphamvu kwambiri. Choncho kuti Yehova asatikwiyire koma azitikomera mtima, tiyenera kudana ndi zimene iye amadana nazo. (Sal. 97:10) Mwachitsanzo, tiyenera kudana ndi chiwerewere. Izi zikutanthauza kuti tiyenera kudana ndi zinthu zilizonse zimene zingatipangitse kuchita chiwerewere. Zina mwa zinthu zimenezi ndi kuonera zolaula. (Sal. 119:37; Mat. 5:28) Kupewa zimenezi n’kovuta koma tiyenera kuchita chilichonse chimene tingathe kuti Yehova atidalitse.

13 Kuti tipambane pa nkhondo yolimbana ndi zinthu zimenezi tiyenera kudalira Yehova osati kudzidalira. Yehova sangasangalale kuona kuti tikudalira “mphamvu za hatchi,” kapena kuti zinthu zimene anthu a m’dzikoli amadalira. Si bwinonso kudalira “miyendo ya munthu,” kapena kuti kuganiza zoti tingapulumuke chifukwa cha mphamvu zathu kapena za anthu ena. (Sal. 147:10) M’malomwake, tiyenera kuchonderera Yehova kuti atithandize. Mosiyana ndi alangizi a m’dzikoli, Yehova satopa tikamamupempha thandizo, ngakhale titachita zimenezi mobwerezabwereza. Paja “Yehova amasangalala ndi anthu amene amamuopa, amene amayembekezera kukoma mtima kwake kosatha.” (Sal. 147:11) Tisamakayikire kuti iye ndi wokoma mtima ndipo angatithandize kuti tisiye kulakalaka zinthu zolakwika.

14. Kodi wolemba Salimo 147 analimbikitsidwa atadziwa mfundo iti?

14 Yehova watipatsa zifukwa zotsimikizira kuti iye amathandiza anthu akakhala pa mavuto. Poganizira zimene zinachitika Ayuda atabwerera ku Yerusalemu, wolemba salimo anafotokoza za Yehova kuti: “Pakuti walimbitsa mipiringidzo ya zipata zako. Wadalitsa ana ako amene ali mwa iwe. Iye akukhazikitsa mtendere m’dziko lako.” (Sal. 147:13, 14) Wolemba salimoyu ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri kudziwa kuti Mulungu adzalimbitsa mageti n’cholinga choti anthu amene amamulambira akhale otetezeka.

Kodi Mawu a Mulungu angatithandize bwanji tikakumana ndi mavuto? (Onani ndime 15-17)

15-17. (a) Kodi nthawi zina tingamve bwanji tikakumana ndi mavuto? (b) Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji Mawu ake potithandiza? (c) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti ‘mawu a Mulungu amathamanga kwambiri.’

15 Mwina mungakumane ndi mavuto amene angakudetseni nkhawa kwambiri. Koma Yehova angakupatseni nzeru zokuthandizani kuthana ndi mavutowo. Wolemba salimoyo ananena kuti Mulungu “amatumiza mawu ake padziko lapansi, ndipo mawu akewo amathamanga kwambiri.” Iye ananenanso kuti Yehova ‘amapereka chipale chofewa, amamwaza mame oundana komanso amaponya madzi oundana.’ Kenako anafunsa kuti: “Ndani angaime m’chisanu chake?” Iye ananenanso kuti Yehova “amatumiza mawu ake ndi kusungunula madzi oundanawo.” (Sal. 147:15-18) Mulungu wathu ndi wanzeru kwambiri, wamphamvu zonse komanso akhoza kuletsa matalala kapena chipale chofewa kuti zisagwe. Choncho akhozanso kukuthandizani kuthana ndi vuto lililonse limene mungakumane nalo.

16 Masiku ano, Yehova amagwiritsa ntchito Mawu ake opezeka m’Baibulo kuti azititsogolera. Ndipo tinganene kuti “mawu akewo amathamanga kwambiri” chifukwa Yehova amatipatsa malangizo oyenera pa nthawi iliyonse imene tikufunikira malangizowo. Taganizirani za malangizo othandiza amene mumalandira mukamawerenga Baibulo, kuphunzira mabuku a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” kuonera JW Broadcasting, kupita pa jw.org, kulankhula ndi akulu komanso kucheza ndi Akhristu anzanu. (Mat. 24:45) Muyenera kuti mwaona kuti Yehova sachedwa kukupatsani malangizo othandiza.

17 Mlongo wina dzina lake Simone waona umboni wakuti Mawu a Mulungu ndi amphamvu.  Iye ankadziona ngati wachabechabe moti ankaona kuti Mulungu sangasangalale naye. Ngakhale zinali choncho, akakhumudwa kwambiri sankasiya kupempha Yehova kuti amuthandize. Anapitirizanso kuphunzira Baibulo nthawi zonse. Iye anati: “Nthawi zonse ndimaona kuti Yehova akundipatsa mphamvu komanso kunditsogolera.” Zimenezi zimamuthandiza kuti asataye mtima.

18. (a) Kodi n’chiyani chimakuchititsani inuyo kumva kuti muli ndi mwayi waukulu? (b) Kodi inuyo muli ndi zifukwa ziti zonenera kuti “Tamandani Ya”?

18 Wolemba salimo uja ankadziwa kuti Aisiraeli anali ndi mwayi waukulu kwambiri. Zili choncho chifukwa ndi iwo okha amene anapatsidwa “mawu” a Mulungu komanso “malangizo ake ndi zigamulo zake.” (Werengani Salimo 147:19, 20.) Masiku ano, nafenso tili ndi mwayi waukulu chifukwa ndi ife tokha amene timadziwika ndi dzina la Mulungu. Timakhalanso pa ubwenzi wolimba ndi Yehova chifukwa chomudziwa ndiponso kutsogoleredwa ndi Mawu ake. Mofanana ndi wolemba Salimo 147, nanunso muyenera kuti muli ndi zifukwa zambiri zonenera kuti “Tamandani Ya” komanso zolimbikitsira anthu ena kuti azichita zimenezi.