Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tetezani Maganizo Anu

Tetezani Maganizo Anu

PANOPA inuyo muli pa nkhondo. Mdani wanu ndi Satana ndipo akugwiritsa ntchito chida choopsa kwambiri. Chida chake ndi mfundo zabodza. Iye amagwiritsa ntchito mfundo zabodza pofuna kusokoneza maganizo anu.

Mtumwi Paulo ankadziwa kuopsa kwa mfundo zabodza za Satana koma Akhristu ena a nthawi yake sankadziwa. Mwachitsanzo, zikuoneka kuti Akhristu ena ku Korinto ankadzidalira kwambiri moti ankaganiza kuti sangagwe mwauzimu. (1 Akor. 10:12) N’chifukwa chake Paulo anapereka chenjezo lakuti: “Nkhawa yanga ndi yakuti mwina, monga mmene njoka inanamizira Hava ndi chinyengo chake, maganizo anunso angapotozedwe kuti musakhalenso oona mtima ndi oyera ngati mmene muyenera kuchitira kwa Khristu.”​—2 Akor. 11:3.

Mawu a Paulowa akusonyeza kuti si nzeru kudzidalira. Ngati tikufuna kupambana pa nkhondoyi, tiyenera kuzindikira kuopsa kwa mfundo zabodza za Satana n’kuteteza maganizo athu.

KODI MFUNDO ZABODZA NDI ZOOPSA BWANJI?

Munkhaniyi tikunena za mfundo zabodza zomwe zikhoza kupusitsa anthu, kusokoneza maganizo awo komanso kuipitsa khalidwe lawo. Buku lina limanena kuti kugwiritsa ntchito mfundo zabodza pofuna kupusitsa anthu ndi kosayenera, ndi koopsa komanso si chilungamo. Anthu ena amaona kuti anthu amene amafalitsa mfundo zabodza amafuna kulamulira maganizo a ena.​—Propaganda and Persuasion.

Kodi mfundo zabodza ndi zoopsa bwanji? Ndi zoopsa kwambiri ngati mpweya wakupha umene sumveka fungo lililonse. Zili choncho chifukwa mofanana ndi mpweyawu mfundozi zikhoza kulowa m’maganizo a munthu popanda munthuyo kuzindikira. Katswiri wina wamakhalidwe a anthu dzina lake Vance Packard ananena kuti: “Ambirife timasokonezedwa ndi mfundo zabodza kuposa mmene tikuganizira.” Katswiri wina ananenanso kuti anthu ambiri akhala “akusokonezedwa mosavuta ndi mfundo zabodza mpaka kuchita zinthu zoopsa kwambiri.” Akhoza kuchita zinthu monga ‘kupha anthu ambiri, kuyambitsa nkhondo,  kudanitsa mitundu ya anthu komanso kudana ndi anthu azipembedzo zina.’​—Easily Led​—A History of Propaganda.

Ndiye ngati anthu angatipusitse ndi mfundo zawo zabodza kuli bwanji Satana? Iye wakhala akuona zimene anthu amachita kuyambira pamene anthu oyambirira analengedwa. Ndipo Baibulo limati panopa “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” Choncho Satana akhoza kugwiritsa ntchito mbali iliyonse ya dzikoli kuti afalitse mfundo zake zabodza. (1 Yoh. 5:19; Yoh. 8:44) Satana ndi waluso kwambiri pa nkhani ‘yochititsa khungu maganizo a anthu’ ndipo “akusocheretsa dziko lonse lapansi.” (2 Akor. 4:4; Chiv. 12:9) Ndiye kodi tingadziteteze bwanji?

KODI MUNGADZITETEZE BWANJI?

Yesu anatchula mfundo yosavuta yotithandiza kuti tidziteteze. Iye anati: “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yoh. 8:31, 32) Pa nkhondo, msilikali amafunika kudziwa kumene angapeze mfundo zolondola chifukwa adani ake akhoza kufalitsa mfundo zabodza n’cholinga choti amupusitse. Ndiye kodi ifeyo tingapeze kuti mfundo zoona? Yehova anapereka mfundo zimenezi m’Baibulo ndipo zikhoza kutithandiza kuti Satana asatipusitse.​—2 Tim. 3:16, 17.

Koma Satana nayenso amadziwa kuti anthu angapeze mfundo zolondola m’Baibulo. Choncho amagwiritsa ntchito zinthu za m’dzikoli kuti alepheretse anthu kuwerenga komanso kuphunzira Baibulo. Musalole kuti nanunso akupusitseni ndi zochita zake zachinyengo. (Aef. 6:11) Choncho ndi bwino kuyesetsa kuti ‘tidziwe bwino’ mfundo zachoonadi. (Aef. 3:18) Kuti zimenezi zitheke pamafunika khama ndithu. Koma ndi bwino kukumbukira mfundo imene wolemba mabuku wina dzina lake Noam Chomsky ananena. Iye anati: “Palibe amene angatenge choonadi n’kuchikhuthulira m’mutu mwanu. Aliyense ayenera kuyesetsa payekha kuti adziwe zoona.” Choncho tiyeni tiziyesetsa patokha kuti tsiku ndi tsiku tiziphunzira komanso “kufufuza Malemba mosamala.”​—Mac. 17:11.

Ngati tikufuna kupambana pa nkhondoyi, tiyenera kuzindikira kuopsa kwa mfundo zabodza za Satana n’kuteteza maganizo athu

Tisaiwalenso kuti Satana safuna kuti anthu aziganiza bwino. Zimene amachitazi n’zogwirizana ndi mfundo imene inalembedwa m’buku lina. Bukulo linanena kuti mfundo zabodza zimasokoneza munthu mosavuta ngati munthuyo sakuganizira mbali zonse za nkhaniyo. (Media and Society in the Twentieth Century) Choncho si nzeru kumangokhulupirira  chilichonse chimene tamva popanda kuchiganizira bwinobwino. (Miy. 14:15) M’malomwake tiyenera kugwiritsa ntchito luso limene Mulungu anatipatsa loti tiziganiza bwino n’cholinga choti tidziwe bwino mfundo za m’Baibulo ndiponso kuzikhulupirira ndi mtima wonse.​—Miy. 2:10-15; Aroma 12:1, 2.

TISALOLE KUTI MGWIRIZANO WATHU USOKONEZEDWE

Asilikali amatha kuchita mantha n’kufooka chifukwa choti amva mfundo zabodza. Nthawi zina, mfundo zabodzazo zimachititsa kuti asilikali ena asiyane ndi gulu lawo kapena ayambe kuukirana okhaokha. Mkulu wina wa asilikali a dziko la Germany ananena kuti chimenechi ndi chimodzi mwa zifukwa zimene zinachititsa kuti asilikali a dzikoli agonjetsedwe pa nkhondo yoyamba yapadziko lonse. Iye ananena kuti zimenezi zinasokoneza kwambiri asilikali moti anangogonja basi. Izi n’zimenenso Satana amachita pofuna kusokoneza mgwirizano wa Akhristu. Mwachitsanzo, iye amafuna kuyambitsa mikangano pakati pa abale. Koma nthawi zina amachititsa Akhristu ena kuganiza kuti gulu la Yehova lalakwitsa zinazake kapena silinachite zinthu mwachilungamo ndipo amachoka m’gulu.

Koma musalole kuti Satana akupusitseni. Nthawi zonse muzitsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, pa nkhani yogwirizana ndi Akhristu anzathu, Baibulo limatiuza kuti ‘tipitirize kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse komanso kuti tikasiyana maganizo tizithetsa nkhaniyo mwamsanga.’ (Akol. 3:13, 14; Mat. 5:23, 24) Baibulo limanenanso kuti kudzipatula n’kusiya kugwirizana ndi mpingo n’koopsa kwambiri. (Miy. 18:1) Choncho ndi bwino kudzifufuza kuti tione ngati Satana sanatisokoneze. Mwachitsanzo, tingadzifunse kuti: ‘Kodi nthawi yomaliza imene Mkhristu mnzanga anandikhumudwitsa ndinatani? Kodi ndinatsatira maganizo a Yehova kapena a Satana?’​—Agal. 5:16-26; Aef. 2:2, 3.

MUSASIYE KUKHULUPIRIRA YEHOVA NDI GULU LAKE

Msilikali amene sakhulupirira mtsogoleri wake samenya bwino nkhondo. Choncho adani amakonda kuchititsa asilikali kuti asamakhulupirire atsogoleri awo. Mwina angamanene kuti: “Atsogoleri anutu sangakuthandizeni!” kapena kuti “Musalole kuti akupweteketseni!” Pofuna kuti zonena zawozo zimveke zanzeru, amatha kutchula zinthu zina zimene atsogoleriwo analakwitsa.  Satana amachitanso chimodzimodzi. Iye nthawi zonse amafufuza njira zoti atichititse kukayikira anthu amene Yehova akuwagwiritsa ntchito potitsogolera.

Ndiye kodi tingadziteteze bwanji? Tiyenera kuyesetsa kukhala okhulupirika kwa Yehova komanso gulu lake. Tizikhalanso okhulupirika kwa anthu amene Yehova akuwagwiritsa ntchito ngakhale kuti si angwiro. (1 Ates. 5:12, 13) Nthawi zina anthu ampatuko komanso anthu ena achinyengo amanena zinthu zoipa zokhudza gulu lathu. Ngakhale zonena zawozo zitaoneka ngati zoona, “musafulumire kugwedezeka pa maganizo anu.” (2 Ates. 2:2; Tito 1:10) Tingachite bwino kutsatira malangizo amene Timoteyo anapatsidwa. Tizikumbukira mfundo zachoonadi zimene tinaphunzira komanso kumene tinaziphunzira. (2 Tim. 3:14, 15) Pali umboni wambirimbiri wotsimikizira kuti Yehova wakhala akugwiritsa ntchito kapolo wokhulupirika kwa zaka pafupifupi 100 kuti azitiphunzitsa choonadi.​—Mat. 24:45-47; Aheb. 13:7, 17.

MUSAFOOKE CHIFUKWA CHOCHITA MANTHA

Koma tisaiwale kuti Satana ali ndi njira zina zosokonezera anthu. Nthawi zina amayendera njira yoopseza anthu ndipo buku lina linanena kuti iyi ndi njira yakalekale yosokonezera maganizo a anthu. Pulofesa wina wa ku Britain dzina lake Philip M. Taylor ananena kuti Asuri ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha anthu amene ankaopseza ena ndiponso kugwiritsa ntchito mfundo zabodza pofuna kusokoneza maganizo awo. Satana amafuna kuti ifenso tiziopa anthu, kuopa kuzunzidwa, kuopa kufa komanso kuopa zinthu zina n’cholinga choti tisiye kutumikira Yehova.​—Yes. 8:12; Yer. 42:11; Aheb. 2:15.

Musalole kuti Satana akuchititseni kufooka chifukwa cha mantha mpaka kufika posiya kukhala okhulupirika kwa Yehova. Yesu ananena kuti: “Musamaope amene amapha thupi lokha, amene sangathe kuchita zoposa pamenepa.” (Luka 12:4) Musamakayikire mfundo yoti Yehova azikuyang’anirani ndipo adzakupatsani “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti ikulimbikitseni mukakumana ndi chinthu chilichonse chokuchititsani mantha.​—2 Akor. 4:7-9; 1 Pet. 3:14.

N’zoona kuti pa moyo wathu tikhoza kukumana ndi zinthu zimene zingatichititse mantha kwambiri. Koma tizikumbukira mawu amene Yehova anauza Yoswa akuti: “Ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usachite mantha kapena kuopa, pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.” (Yos. 1:9) Chinachake chikamakudetsani nkhawa muzingopemphera kwa Yehova n’kumufotokozera zonse zimene zili mumtima mwanu. Mukatero, ‘mtendere wa Mulungu udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu’ ndipo Satana sadzatha kukupusitsani ndi mfundo zake zabodza.​—Afil. 4:6, 7, 13.

Kodi mukukumbukira zimene Rabisake anachita pofuna kufooketsa anthu a Mulungu? Tingati iye ananena kuti, ‘Palibe angakutetezeni kwa Asuri. Ngakhale Mulungu wanu Yehovayo sangachite kalikonse.’ Kenako anapitiriza kuti: ‘Yehova weniweniyo ndi amene watituma kuti tidzawononge dzikoli.’ Kodi Yehova anayankha bwanji mawu amenewa? Iye anati: “Usachite mantha chifukwa cha mawu amene wamva, amene atumiki a mfumu ya Asuri andilankhulira monyoza.” (2 Maf. 18:22-25; 19:6) Kenako Yehova anatumiza mngelo amene anapha Asuri 185,000 usiku umodzi wokha.​—2 Maf. 19:35.

KHALANI ANZERU NDIPO MUZIMVERA YEHOVA NTHAWI ZONSE

Kodi inuyo munaonerapo filimu inayake n’kudziwiratu kuti munthu wina akupusitsidwa? Mwina munanenapo mumtima mwanu kuti: ‘Iwe asakupusitse! Akunamatu ameneyo!’ Ndiye muziyerekezera angelo akukuuzani kuti: “Iwe zabodza zimenezo! Asakupusitse Satanayo.”

Choncho musalole kuti Satana akupusitseni. (Miy. 26:24, 25) Muzimvera Yehova ndipo muzimukhulupirira pa chilichonse. (Miy. 3:5-7) Iye amakukondani ndipo amakuuzani kuti: “Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga.” (Miy. 27:11) Mukamachita zimenezi mudzapambana pa nkhondo yoteteza maganizo anu.