Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi ndi nzeru kuti Mkhristu azisunga mfuti pofuna kudziteteza kwa anthu?

Akhristu ayenera kutsatira mfundo za m’Baibulo posankha njira zodzitetezera. Malinga ndi mfundo za m’Malemba, si bwino kugwiritsa ntchito mfuti pofuna kudziteteza kwa anthu ena. Tikutero pa zifukwa zotsatirazi:

Yehova amaona kuti moyo wa munthu ndi wamtengo wapatali komanso wopatulika. Davide analemba kuti Yehova ndi “kasupe wa moyo.” (Sal. 36:9) Choncho Mkhristu akamadziteteza kapena kuteteza chuma chake amayesetsa kupewa kupha munthu kuti asakhale ndi mlandu wa magazi.​—Deut. 22:8; Sal. 51:14.

N’zoona kuti munthu akhoza kupha mnzake ngati atagwiritsa ntchito chida chilichonse, koma ngati watenga mfuti zimakhala zosavuta kuti aphe mnzake mwadala kapena mwangozi. * Vuto lina ndi lakuti munthu wachiwembu akaona kuti wina ali ndi mfuti amaopa ndipo zimene angachite pofuna kudziteteza zingachititse kuti pafe munthu.

Pamene Yesu anauza ophunzira ake kuti atenge lupanga sankafuna kuti agwiritse ntchito podziteteza. (Luka 22:36, 38) Yesu anachita izi pofuna kuwaphunzitsa kuti asamachite zinthu mwachiwawa, ngakhale pamene akumana ndi gulu lokhala ndi zida. (Luka 22:52) Mwachitsanzo, Petulo atasolola lupanga lake n’kutema nalo kapolo wa  mkulu wa ansembe, Yesu anamuuza kuti: “Bwezera lupanga lako m’chimake.” Kenako ananena mfundo imene tonse tiyenera kuikumbukira yakuti: “Onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.”​—Mat. 26:51, 52.

Mogwirizana ndi Mika 4:3 anthu a Mulungu ‘amasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo.’ Mfundo imeneyi ndi imene Akhristu amayendera ndipo ikugwirizana ndi malangizo amene mtumwi Paulo ananena akuti: “Musabwezere choipa pa choipa. . . . Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.” (Aroma 12:17, 18) Ngakhale kuti Paulo anakumana ndi achifwamba komanso mavuto ena ambiri, iye ankatsatira mfundo imeneyi ndipo sanayese kudziteteza m’njira yosemphana ndi Malemba. (2 Akor. 11:26) M’malomwake ankadalira Yehova ndipo ankayendera nzeru yopezeka m’Mawu a Mulungu yomwe ndi yabwino “kuposa kukhala ndi zida zomenyera nkhondo.”​—Mlal. 9:18.

Akhristu amaona kuti moyo ndi wofunika kuposa katundu. Baibulo limanena kuti moyo wa munthu “suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Choncho ngati mwakumana ndi wachifwamba ndipo sizikutheka kukambirana naye mofatsa, ndi bwino kutsatira malangizo amene Yesu ananena akuti: “Usalimbane ndi munthu woipa.” Tingati nthawi imeneyi ndi yoyenera kungomupatsa malaya amkati ndi akunja omwe. (Mat. 5:39, 40; Luka 6:29) * Koma chofunika kwambiri pa nkhani imeneyi ndi kupewa. Tikamapewa mtima ‘wodzionetsera ndi zimene tili nazo’ komanso anthu akamadziwa kuti ndife okonda mtendere, zigawenga sizingatilondelonde.​—1 Yoh. 2:16; Miy. 18:10.

Akhristu amalemekeza chikumbumtima cha anzawo. (Aroma 14:21) Abale ndi alongo akhoza kudabwa mwinanso kukhumudwa atamva kuti munthu wina mumpingo ali ndi mfuti yoti azidzitetezera kwa anthu. Koma ngati ndife achikondi timaganizira zofuna za ena n’kulolera kuti tisakhale ndi zinthu zina, ngakhale zimene timaona kuti tili ndi ufulu wokhala nazo.​—1 Akor. 10:32, 33; 13:4, 5.

Akhristu ayenera kupereka chitsanzo chabwino. (2 Akor. 4:2; 1 Pet. 5:2, 3) Ngati Mkhristu wapatsidwa malangizo a m’Malemba koma akusungabe mfuti kuti azidzitetezera kwa anthu, sangapereke chitsanzo chabwino. Choncho sangayenerere kupatsidwa udindo kapena utumiki wapadera mumpingo. N’chimodzimodzinso ndi munthu amene ntchito yake imachititsa kuti azitenga mfuti. Angachite bwino kungofufuza ntchito ina basi. *

Munthu aliyense akhoza kusankha yekha ntchito komanso njira yotetezera moyo wake, banja lake kapena katundu wake. Ngakhale zili choncho, mfundo za m’Baibulo zimasonyeza kuti Mulungu ndi wanzeru ndipo amatikonda. Chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulozi, Akhristu ozindikira sasunga mfuti pofuna kudziteteza kwa anthu. Iwo amadziwa kuti munthu amatetezeka kwambiri ngati amakhulupirira Yehova komanso kutsatira mfundo za m’Baibulo.​—Sal. 97:10; Miy. 1:33; 2:6, 7.

Pa chisautso chachikulu, Akhristu adzadalira Yehova ndipo sadzayesa kudziteteza okha

^ ndime 3 Mkhristu angasankhe kukhala ndi mfuti kuti azigwiritsa ntchito posaka kapena podziteteza ku nyama zolusa. Koma zingakhale bwino kusunga mfutiyo pamalo obisika ilibe zipolopolo kapena ili yomasula. M’mayiko amene amaletsa kukhala ndi mfuti kapena salola kukhala nayo chisawawa, Akhristu ayenera kutsatira malamulowo.​—Aroma 13:1.

^ ndime 2 Mukafuna kudziwa zimene mungachite ngati munthu akufuna kukugwirirani werengani nkhani yakuti “Njira Zopewera Kugwiriridwa Chigololo” mu Galamukani! ya March 8, 1993.

^ ndime 4 Mfundo zina zothandiza pa nkhani ya ntchito zomwe zimachititsa kuti munthu azitenga mfuti mungazipeze mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2005, tsamba 31 komanso Nsanja ya Olonda yachingelezi ya July 15, 1983, tsamba 25-26.