NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) January 2020

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa March 2–April 5, 2020.

‘Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzira Anga’

Lemba la chaka cha 2020 litithandiza kuti tiziyesetsa kuwafika pamtima anthu amene timaphunzira nawo.

Mukhoza Kuthandiza Anthu Komanso Kuwalimbikitsa

Pali makhalidwe atatu amene angatithandize kuti tizithandiza komanso kulimbikitsa anthu ena.

Yehova Amaona Kuti Ndinu Amtengo Wapatali

Tikamavutika ndi matenda, mavuto azachuma kapena ukalamba tiyenera kukumbukira kuti palibe chimene chingatisiyanitse ndi chikondi cha Atate wathu wakumwamba.

‘Mzimu Umachitira Umboni’

Kodi munthu amadziwa bwanji kuti wadzozedwa ndi mzimu woyera? Kodi chimachitika n’chiyani munthu akadzozedwa?

Tipita Nanu Limodzi

Kodi tiyenera kuwaona bwanji anthu amene amadya zizindikiro pa Chikumbutso? Kodi tiyenera kudandaula ngati chiwerengero cha odya pa Chikumbutso chikuwonjezereka?