Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi kale anthu ankanyamula bwanji moto pa ulendo?

Lemba la Genesis 22:6 limanena kuti pamene Abulahamu ankapita kukapereka nsembe kuphiri ‘anatenga nkhuni zokawotchera nsembe n’kumusenzetsa Isaki. Iye ananyamula moto ndi mpeni wophera nyama, ndipo iwo anapitira limodzi.’

Baibulo silifotokoza mmene anthu ankayatsira moto kale. Pa nkhani ya Abulahamuyi, munthu wina ananena kuti n’zokayikitsa kuti munthu ankatha kutenga moto woyaka n’kuyenda nawo ulendo wautali. Izi zikusonyeza kuti Abulahamu sanatenge moto woyaka koma anatenga chinthu chinachake chomwe anaikamo zinthu zoti akayatsire moto.

Koma anthu ena amanena kuti kale kuyatsa moto kunali kovuta kwambiri. Amati anthu ankaona kuti bola kungopala moto kusiyana n’kuyamba kuyatsa. Choncho akatswiri ambiri amakhulupirira kuti Abulahamu anatenga chinthu changati mphika chokhala ndi chingwe cha tcheni ndipo munali makala a moto. (Yes. 30:14) Munthu akatenga makala a moto mumphika ngati umenewo ankatha kuyenda nawo kwa nthawi yaitali n’kukayatsira moto akafika kumene akupita.