Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anadzipereka ndi Mtima Wonse

Anadzipereka ndi Mtima Wonse

PALI alongo osakwatiwa ambiri amene anasamukira kumadera komwe kuli ofalitsa Ufumu ochepa. Ena mwa alongowa anasamukira m’mayiko ena ndipo atumikira kwa zaka zambiri. Kodi n’chiyani chinawapangitsa kuti asamukire kudziko lina? Kodi aphunzira chiyani pa utumikiwu? Nanga apeza madalitso otani? Tinacheza ndi alongo angapo kuti afotokoze okha. Ngati ndinu mlongo wosakwatiwa ndipo mumalakalaka mutachita utumiki wosangalatsa kwambiri, tikukhulupirira kuti zimene alongowa ananena zikuthandizani. Komabe zitsanzo zawo ndi zothandiza kwa tonsefe.

KODI ANATANI KUTI ASIYE KUDZIKAYIKIRA?

Mlongo Anita

Mwina mumaganiza kuti, ‘Kodi ineyo ndingathe kukachita upainiya kudziko lina n’kumakasangalala bwinobwino?’ Mlongo Anita panopa ali ndi zaka 75 ndipo poyamba nawonso ankadzikayikira. Iwo anakulira ku England ndipo anayamba upainiya ali ndi zaka 18. Mlongo Anita anati: “Ndinkakonda kuphunzitsa anthu za Yehova, koma sindinkalotako n’komwe zoti ndingadzakatumikire kudziko lina. Ndinali ndisanaphunzirepo chinenero cha dziko lina ndipo ndinkaona kuti sindingakwanitse. Choncho nditalandira kalata yoti ndikalowe Sukulu ya Giliyadi ndinadabwa kwambiri. Ndinkaganiza kuti zatheka bwanji kuti munthu wamba ngati ine ndiitanidwe kusukuluyi. Koma kenako ndinaganiza kuti, ‘Ngati Yehova waona kuti ndingathe, ndikayesetsa kuchita mbali yanga.’ Panopa patha zaka 50 ndikuchita umishonale ku Japan. Nthawi zina ndimauza alongo achitsikana mocheza kuti, ‘Nanunso ingoberekerani zikwama ndipo tipitire limodzi mukaone nokha mmene ntchitoyi imasangalatsira.’ Ndimasangalala kuona kuti ambiri ayambadi ntchitoyi.”

N’CHIYANI CHINAWATHANDIZA KUTI ALIMBE MTIMA?

Alongo ambiri amene akutumikira kudziko lina poyamba ankazengereza zosamuka. Ndiye kodi n’chiyani chinawalimbitsa mtima?

Mlongo Maureen

Mlongo Maureen omwe panopa ali ndi zaka 64 anati: “Kuyambira ndili wamng’ono, ndinkafunitsitsa kuthandiza anthu.” Ndiyeno atakwanitsa zaka 20 anasamukira ku Quebec, m’dziko la Canada chifukwa choti kunkafunika apainiya ambiri. Mlongoyu anati: “Kenako ndinaitanidwa ku Sukulu ya Giliyadi koma ndinkaopa kupita kumalo achilendo kopanda anzanga. Ndinkafunanso kuti ndizithandiza mayi anga kusamalira bambo anga amene ankadwala. Nthawi zambiri ndinkapempha Yehova usiku kuti andithandize kudziwa  zochita ndipo ndinkachita izi uku ndikulira. Nditakambirana ndi makolo anga, anandilimbikitsa kuti ndipite. Komanso mpingo unkasamalira bwino makolo angawo. Nditaona kuti Yehova akundithandiza ndinatsimikizira kuti akandisamaliranso kudziko linalo. Apa tsopano ndinaona kuti ndikhoza kupita.” Mlongo Maureen anasamukira ku West Africa mu 1979 ndipo anachita umishonale kumeneko kwa zaka zoposa 30. Panopa mlongoyu anabwerera ku Canada kuti azikasamalira mayi ake ndipo akuchita upainiya wapadera. Akaganizira zaka zimene watumikira Yehova m’dziko lina amanena kuti: “Yehova wakhala akundipatsa zinthu zofunika pa nthawi yoyenera.”

Mlongo Wendy

Mlongo wina dzina lake Wendy anayamba upainiya ku Australia asanakwanitse zaka 20 ndipo panopa ali ndi zaka 65. Mlongoyu anati: “Munthune ndinali wamantha ndipo ndinkaopa kulankhula ndi anthu osawadziwa. Koma upainiya unandithandiza kuti ndizilankhula bwinobwino ndi anthu a mitundu yonse ndipo ndinasiya kudzikayikira. Unandithandizanso kuti ndizidalira kwambiri Yehova komanso kuti ndizilakalaka kukatumikira kudziko lina. Ndiyeno mlongo wina amene anachita umishonale ku Japan kwa zaka zoposa 30 anandipempha kuti ndipite kukalalikira naye ku Japan kwa miyezi itatu. Ndinapitadi ndipo izi zinachititsa kuti ndiyambe kulakalaka kwambiri kusamuka.” Mu 1986, a Wendy anasamukira kuchilumba cha Vanuatu chomwe chili pa mtunda wa makilomita 1,770 kum’mawa kwa Australia.

Panopa a Wendy adakali ku Vanuatu, ndipo akutumikira pa ofesi yomasulira mabuku. Iwo anati: “Ndimasangalala kwambiri kuona m’madera akumidzi mukukhazikitsidwa mipingo ndi timagulu. Ndi mwayi waukulu kwambiri kuthandiza nawo pa ntchito ya Yehova pachilumbachi.

Mlongo Kumiko (ali pakati)

Mlongo Kumiko panopa ali ndi zaka 65 ndipo poyamba ankachita upainiya ku Japan. Kenako mnzake amene ankachita naye upainiya anamupempha kuti asamukire limodzi ku Nepal. Mlongo Kumiko anati: “Mnzangayu analimbikira kuti tisamuke koma ine ndinkakana. Ndinkada nkhawa ndi zokaphunzira chinenero komanso chikhalidwe chatsopano. Vuto linanso linali la ndalama zoti tizikagwiritsa ntchito. Koma kenako ndinachita ngozi ya njinga yamoto ndipo anandigoneka m’chipatala. Ndili m’chipatalamo ndinaganiza kuti, ‘Si bwino kumangozengereza zosamukazi. Zachitikazi zikusonyeza kuti mwina ndikhoza kudwala kwambiri n’kudzalephera kukachita upainiya kudziko lina. Mwinatu ndingopita kukalalikira kudziko lina kwa chaka chimodzi chokha.’ Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize.” Mlongo Kumiko atatuluka m’chipatala anapita kukacheza ku Nepal ndipo kenako anasamukira m’dzikoli, limodzi ndi mnzawo uja.

 Panopa patha zaka 10 ali m’dzikoli ndipo anati: “Mavuto onse amene ankandidetsa nkhawa aja anamwazika ngati madzi omwe anagawikana pa Nyanja Yofiira. Ndimasangalala kwambiri kuti ndinasamukira kumene kunali ofalitsa ochepa. Nthawi zambiri tikamachita phunziro ndi banja, anthu okwana 5 kapena 6 amabwera kudzamvetsera nawo. Komanso ana amandipempha kuti ndiwapatse timapepala. N’zosangalatsa kwambiri kulalikira m’gawo la anthu omvetsera chonchi.”

KODI AMATHANA BWANJI NDI MAVUTO?

N’zosachita kufunsa kuti alongo amene amasamukira kudziko lina amakumananso ndi mavuto. Ndiye kodi amathana nawo bwanji?

Mlongo Diane

Mlongo Diane a ku Canada panopa ali ndi zaka 62 ndipo anachitapo umishonale zaka 20 ku Ivory Coast (panopa ndi Côte d’Ivoire). Iwo anati: “Poyamba zinkandivuta kukhala kutali ndi achibale anga. Koma ndinapempha Yehova kuti andithandize kuti ndizikonda anthu a kumeneku. Tili ku Sukulu ya Giliyadi, M’bale Jack Redford, yemwe anali mlangizi wathu ananena kuti tingathe kukumana ndi zinthu zokhumudwitsa makamaka m’mayiko osauka kwambiri. Koma iwo anati: ‘Musamakaganizire kwambiri za kusaukako. Muzikaganizira za anthu komanso mmene asinthira moyo wawo chifukwa chophunzira choonadi.’ Ndinkachitadi zimenezi ndipo ndinapeza madalitso ambiri. Ndikamauza anthu madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse, ndinkaona kuti ayamba kuoneka osangalala.” Ndiye kodi n’chiyani chinawathandiza a Diane kuti azolowere moyo wa kumeneku? Iwo anati: “Ndinayesetsa kuti ndizikonda kwambiri anthu amene ndinkaphunzira nawo komanso ndinkasangalala ndikaona kuti ayamba kutumikira Yehova. Choncho ku Ivory Coast ndinayamba kukuona ngati kwathu. Mogwirizana ndi zimene Yesu ananena, ndinapeza amayi, abambo, azichimwene komanso azichemwali.”—Maliko 10:29, 30.

Mlongo Anne, yemwe panopa ali ndi zaka 46 akutumikira ku Asia m’dziko lomwe ntchito yathu ndi yoletsedwa. Iye anati: “M’malo osiyanasiyana amene ndatumikira, ndakhalapo ndi alongo ochokera kumadera osiyanasiyananso. Alongowa amachita zosiyana kwambiri ndi zimene ine ndinazolowera kwathu. Izi zinkachititsa kuti tisamamvetsetsane komanso tizikhumudwitsana. Koma zoterezi zikachitika, ndinkayesetsa kuti ndizigwirizana ndi anthu omwe ndinkakhala nawo. Ndinkayesetsanso kuphunzira chikhalidwe chawo, kuwakonda kwambiri komanso kuwamvetsa.  Izi zachititsa kuti ndikhale ndi anzanga ambiri omwe amandithandiza pa utumiki wanga.”

Mlongo Ute

Mlongo Ute a ku Germany panopa ali ndi zaka 53 ndipo mu 1993, anatumizidwa ku Madagascar kuti akakhale mmishonale. Iwo anati: “Poyamba ndinavutika kuphunzira chilankhulo, kuzolowera nyengo yakumeneko komanso kulimbana ndi malungo ndi tizilombo tina toyambitsa matenda. Koma abale ndi alongo anandithandiza. Alongo akumeneko, ana awo ndiponso maphunziro anga anandithandiza kuti ndiphunzire chilankhulo chawo. Komanso nditadwala, mlongo amene ndinkachita naye umishonale anandithandiza. Koma Yehova ndi amene anandithandiza kwambiri. Ndinkapemphera kuchokera pansi pa mtima n’kumuuza nkhawa zanga zonse. Ndikatero ndinkadikira moleza mtima kwa masiku kapenanso miyezi kuti andiyankhe. Yehova ankandithandiza pa vuto lililonse.” Panopa a Ute achita umishonale ku Madagascar kwa zaka 23.

YEHOVA AMAWADALITSA KWAMBIRI

Mofanana ndi anthu ena onse amene amasamukira m’mayiko ena, alongowa nawonso apeza madalitso ambiri. Tiyeni tione ena mwa madalitso amenewa.

Mlongo Heidi

Mlongo Heidi wa ku Germany panopa ali ndi zaka 73 ndipo wakhala akuchita umishonale ku Côte d’Ivoire kuyambira mu 1968. Mlongo Heidi anati: “Ine ndimasangalala kwambiri kuona anthu amene ndawaphunzitsa ‘akupitiriza kuyenda m’choonadi.’ Anthu ena amene ndinawaphunzitsa panopa ndi apainiya kapena akulu. Ambiri amangondinena kuti Amama kapena Agogo. Mkulu wina, mkazi wake komanso ana ake atatu amangonditenga ngati munthu wa m’banja lawo. Apatu Yehova wandipatsa mwana, mpongozi komanso adzukulu atatu.”—3 Yoh. 4.

Mlongo Karen (ali pakati)

Mlongo Karen wa ku Canada, panopa ali ndi zaka 72 ndipo anali mmishonale ku West Africa kwa zaka zoposa 20. Mlongoyu anati: “Umishonale unandiphunzitsa kukhala wachikondi, woleza mtima ndiponso wodzipereka pothandiza ena. Komanso kukhala ndi anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana kwandithandiza kuti ndidziwe zambiri. Ndaphunzira kuti pali njira zambiri zochitira zinthu. Ndipotu kukhala ndi anzanga apamtima ochokera m’mayiko osiyanasiyana ndi madalitso. Ngakhale kuti moyo wathu komanso utumiki wathu unasintha, ubwenzi wathu udakalipobe.

Mlongo Margaret a ku England panopa ali ndi zaka 79 ndipo anachitapo umishonale ku Laos. Iwo anati: “Kutumikira m’dziko lina kunandithandiza kumvetsa mfundo yoti Yehova amakoka anthu a mitundu komanso zikhalidwe zosiyanasiyana kuti akhale m’gulu lake. Zimenezi zinalimbitsa chikhulupiriro changa. Zimandithandizanso kuti ndizikhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova akutsogolera gulu lake ndipo adzakwaniritsa cholinga chake.”

Zimene taona m’nkhaniyi zikusonyeza kuti alongo osakwatiwa akuchita zambiri pa ntchito yolalikira. Choncho ndi ofunika kumawayamikira. (Ower. 11:40) Ndipotu chiwerengero chawo chikupitiriza kuwonjezeka. (Sal. 68:11) Kodi inuyo mungathe kusintha zinthu zina pa moyo wanu n’kusamukira kumene kukufunika ofalitsa ambiri ngati mmene anachitira alongowa? Mukatero mudzakhala ngati ‘mukulawa ndipo mudzaona kuti Yehova ndi wabwino.’—Sal. 34:8.