NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) January 2017

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira February 27 mpaka April 2, 2017.

Anadzipereka ndi Mtima Wonse

Alongo ambiri amene anasamukira kumayiko ena poyamba ankadzikayikira. Kodi anatani kuti alimbe mtima? Kodi aphunzirapo chiyani atatumikira kudziko lina?

“Khulupirira Yehova Ndipo Chita Zabwino”

Yehova amatithandiza kuchita zinthu zimene sitikanazikwanitsa patokha. Koma amafuna kuti tiziyesetsa kuchita zonse zimene tingathe. Kodi lemba la chaka cha 2017 lingatithandize bwanji kuti tizichita zinthu moganizira mfundo ziwirizi?

Ufulu Wosankha Zochita Ndi Mphatso Yapadera

Kodi anthufe tili ndi ufulu uti, nanga Baibulo limati bwanji pa nkhani ya ufuluwo? Kodi tingalemekeze bwanji ufulu wa anzathu wosankha zochita?

Kudzichepetsa N’kofunika Kwambiri

Kodi munthu wodzichepetsa amatani? N’chifukwa chiyani tinganene kuti khalidweli ndi lofunika kwambiri?

Kodi Tingatani Kuti Nthawi Zonse Tizikhala Odzichepetsa?

Kodi tingasonyeze bwanji kudzichepetsa zinthu zikasintha, ena akatichitira zolakwika kapena akamatitamanda komanso pamene tikufuna kusankha zochita?

‘Zinthu Zimenezo Uziziphunzitsa kwa Anthu Okhulupirika’

Kodi achikulire angathandize bwanji achinyamata kuti ayenerere maudindo? Kodi achinyamata angasonyeze bwanji kuti amalemekeza achikulire amene akhala oyang’anira kwa nthawi yaitali?

Kodi Mukudziwa?

Kodi kale anthu ankanyamula bwanji moto pa ulendo?