Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mungapezenso Pawebusaiti

Zimene Mungapezenso Pawebusaiti

Kupeza Nkhani Zimene Zimaikidwa Patsamba Loyamba

Abale ndi alongo ambiri amagwiritsa ntchito nkhani zimene zimaikidwa patsamba loyamba pa jw.org mu utumiki. Nkhanizi n’zosavuta kutumizira ena, komanso nthawi zambiri zimafotokoza mmene zinthu zimene zikuchitika zikukwaniritsira maulosi a m’Baibulo. Pofotokoza za nkhanizi, m’bale wina analemba kuti “nkhanizi n’zapanthawi yake komanso zogwirizana ndi mmene tikumalalikirira masiku ano.”

Koma nthawi zambiri nkhani zomwe zimaikidwa patsamba loyamba zimasinthidwa. Ndiye kodi mungatani kuti mupeze nkhani zomwe sizikuonekanso patsambali?

  • Patsamba loyamba pa jw.org, pitani pamene pali linki yakuti “Onani Zambiri.” Linkiyi ikutsegulirani tsamba lakuti “Nkhani Zimene Zapezeka Posachedwapa Patsamba Loyamba.” Pamenepo mungapezepo nkhani zambiri zomwe zinaikidwa patsambali posachedwapa.

  • Pa jw.org kapena pa JW Library®, pitani pa “Laibulale,” kenako “Nkhani Zosiyanasiyana,” ndipo kenako “Nkhani Zina.” Pagawo limeneli pali nkhani zambiri zomwe zinaikidwapo patsamba loyamba.