Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 9

Tiziyamikira Mphatso ya Moyo Imene Mulungu Anatipatsa

Tiziyamikira Mphatso ya Moyo Imene Mulungu Anatipatsa

“Chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.”—MAC. 17:28.

NYIMBO NA. 141 Moyo Ndi Wodabwitsa

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi moyo wathu ndi wofunika bwanji kwa Yehova?

 TAYEREKEZERANI kuti mnzanu wakupatsani chithunzi chojambulidwa mwaluso chakale koma chamtengo wapatali. Chithunzicho chili ndi malo ena akuda komanso owonongeka. Ngakhale zili choncho chithunzicho ndi chodula moti chingagulitsidwe ndi ndalama za madola mamiliyoni. N’zoonekeratu kuti mungayamikire komanso kumachiteteza. Mofanana ndi zimenezi Yehova watipatsa mphatso yamtengo wapatali ya moyo. Ndipotu Yehova anasonyeza kuti amaona kuti moyo wathu ndi wamtengo wapatali popereka Mwana wake monga dipo.​—Yoh. 3:16.

2. Mogwirizana ndi 2 Akorinto 7:1, kodi Yehova amayembekezera kuti tichite chiyani?

2 Yehova ndi Mwiniwake wa moyo. (Sal. 36:9) Mtumwi Paulo anavomereza mfundo ya choonadi imeneyi pomwe anati: “Chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” (Mac. 17:25, 28) Choncho m’pomveka kunena kuti moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Mwachikondi, iye amatipatsa zonse zomwe timafunikira kuti tikhale ndi moyo. (Mac. 14:15-17) Koma panopa sikuti Yehova amateteza moyo wathu mozizwitsa. M’malomwake amayembekezera kuti tichita zonse zomwe tingathe kuti tikhale ndi thanzi labwino komanso tipitirize kumutumikira. (Werengani 2 Akorinto 7:1.) N’chifukwa chiyani tiyenera kuteteza thanzi ndi moyo wathu, nanga tingachite bwanji zimenezi?

TIZIONA KUTI MOYO NDI WAMTENGO WAPATALI

3. Kodi ndi chifukwa chimodzi chiti chomwe chimatichititsa kuti tizisamalira thanzi lathu?

3 Chifukwa chimodzi chomwe chimatichititsa kuti tizisamalira thanzi lathu, ndi chakuti timafuna kutumikira Yehova mmene tingathere. (Maliko 12:30) Timafunitsitsa kupereka ‘matupi athu ngati nsembe yamoyo, yoyera ndi yovomerezeka kwa Mulungu.’ (Aroma 12:1) Choncho timapewa kuchita zinthu zimene tikudziwa kuti zingawononge thanzi lathu. N’zoona kuti ngakhale titayesetsa tikhoza kudwalabe, koma timachita zomwe tingathe kuti tikhale ndi thanzi labwino chifukwa timafuna kusonyeza Atate wathu wakumwamba kuti timayamikira mphatso yamoyo.

4. Kodi Mfumu Davide inkafuna kuchita chiyani?

4 Mfumu Davide inafotokoza chifukwa chake inkayamikira mphatso yamoyo yomwe Mulungu anatipatsa pomwe inalemba kuti: “Kodi magazi anga angakhale ndi phindu lanji ngati nditatsikira kudzenje la manda? Kodi fumbi lidzakutamandani? Kodi lidzalengeza kuti inu ndinu woona?” (Sal. 30:9) Davide ayenera kuti analemba mawu amenewa chakumapeto kwa moyo wake. Komabe iye ankafunitsitsa kukhalabe ndi moyo komanso thanzi labwino n’cholinga choti apitirize kutamanda Yehova. N’zosakayikitsa kuti tonsefe timafunanso zimenezi.

5. Kaya ndife okalamba kapena tikudwala, kodi tingathe kuchita chiyani?

5 Matenda komanso ukalamba zingatilepheretse kuchita zambiri ngati mmene tinkachitira poyamba. Zikatere tingafooke ndiponso kukhumudwa. Komabe sitiyenera kunyalanyaza nkhani yosamalira thanzi lathu. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa kaya takalamba kwambiri kapena tadwala chotani, tingathe kutamandabe Yehova ngati mmene inachitira Mfumu Davide. N’zolimbikitsatu kwambiri kudziwa kuti Mulungu wathu amationa kuti ndife amtengo wapatali kaya tikudwala kapena takalamba. (Mat. 10:29-31) Ngakhale titamwalira, iye amafunitsitsa kutiukitsa. (Yobu 14:14, 15) Panopo pamene tili ndi moyo timafuna kuchita zonse zomwe tingathe pousamalira.

TIZIPEWA ZIZOLOWEZI ZOIPA

6. Kodi Yehova amatiyembekezera kuti tichita chiyani pa nkhani ya zakudya ndi mowa?

6 Ngakhale kuti Baibulo si buku lofotokoza za thanzi kapena za zakudya, limatithandiza kudziwa mmene Yehova amaganizira pa nkhanizi. Mwachitsanzo, iye amatilimbikitsa kuti ‘tiziteteza thupi lathu’ ku zinthu zomwe zingaliwononge. (Mlal. 11:10) Baibulo limaletsa kudya kwambiri komanso kumwa kwambiri mowa chifukwa zimenezi zingawononge moyo. (Miy. 23:20) Yehova amayembekezera kuti tizidziletsa pa nkhani ya kuchuluka kwa chakudya komanso mowa.​—1 Akor. 6:12; 9:25.

7. Kodi malangizo a pa Miyambo 2:11, angatithandize bwanji kuti tizisankha bwino zochita pa nkhani ya thanzi lathu?

7 Tingasonyeze kuti timayamikira kwambiri mphatso ya moyo imene Mulungu anatipatsa pogwiritsa ntchito bwino luso loganiza. (Sal. 119:99, 100; werengani Miyambo 2:11.) Mwachitsanzo, tingagwiritse ntchito luso loganiza pa nkhani ya zakudya zomwe timasankha. Ngati timakonda chakudya chinachake koma timadziwa kuti tikadya chimatidwalitsa, kuganiza bwino kumatithandiza kuti tizichipewa. Tingasonyezenso kuti ndife oganiza bwino tikamagona mokwanira, kuchita masewera olimbitsa thupi nthawi zonse, kukhala aukhondo komanso kusamalira pakhomo pathu.

TIZIYESETSA KUPEWA NGOZI

8. Kodi Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amaiona bwanji nkhani yopewa ngozi?

8 Chilamulo chomwe Yehova anapatsa Aisiraeli chinali ndi malangizo omwe akanawathandiza kupewa ngozi zoopsa zomwe zikanatha kuchitikira kunyumba kapena kumalo antchito. (Eks. 21:28, 29; Deut. 22:8) Ngati munthu wapha mnzake mwangozi ankakumana ndi mavuto aakulu. (Deut. 19:4, 5) Chilamulo chinkanena kuti ngakhale anthu omwe mwangozi avulaza mwana wosabadwa, ankayenera kulangidwa. (Eks. 21:22, 23) Malemba amafotokoza momveka bwino kuti Yehova amafuna kuti tiziyesetsa kupewa ngozi.

Pa zochitika zimenezi kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza moyo? (Onani ndime 9)

9. Kodi tingachite chiyani kuti tipewe ngozi? (Onaninso zithunzi.)

9 Tingasonyeze kuti timayamikira mphatso yamoyo imene Mulungu anatipatsa, potsatira njira zopewera ngozi kunyumba komanso kuntchito. Timachita zinthu mosamala tikamataya zinthu zakuthwa, zapoizoni kapena mankhwala komanso timaika kutali ndi ana zinthu ngati zimenezi. Timakhalanso osamala ndi moto, zinthu zowira, zipangizo zamagetsi ndipo timaonetsetsa kuti sitinazisiye popanda oziyang’anira. Sitiyendetsa galimoto pamene maganizo athu asokonezedwa chifukwa choti tamwa mankhwala ena ake, mowa kapena kusagona mokwanira. Ndipo timaonetsetsa kuti sitikugwiritsa ntchito zipangizo zamakono poyendetsa galimoto.

PAKACHITIKA NGOZI ZA M’CHILENGEDWE

10. Kodi tingachite chiyani ngozi ya m’chilengedwe isanachitike komanso ikamachitika?

10 Nthawi zina sitingathe kupewa zochitika zina zomwe zingachititse kuti moyo wathu ukhale pangozi. Zimenezi zingachitike makamaka pa nthawi ya ngozi za m’chilengedwe, miliri komanso pamene kukuchitika ziwawa. Komabe zinthu ngati zimenezi zikachitika, tingathe kutetezeka komanso kupulumuka ngati titatsatira malangizo oti tichoke m’deralo kapenanso malangizo ena operekedwa ndi akuluakulu a boma. (Aroma 13:1, 5-7) Nthawi zina zingadziwike kuti kuchitika ngozi choncho tingachite bwino kutsatira malangizo a akuluakulu a boma otithandiza kukonzekera. Mwachitsanzo, zingakhale zothandiza kusunga madzi ndi zakudya zimene sizingawonongeke msanga komanso mankhwala ndi zinthu zina zothandizira munthu akavulala.

11. Ngati kwabuka matenda opatsirana, kodi tiyenera kukhala ofunitsitsa kuchita chiyani?

11 Kodi tingatani ngati matenda opatsirana akufalikira m’dera lomwe timakhala? Tiyenera kumvera malangizo omwe angatiteteze monga kusamba m’manja, kukhala motalikirana, kuvala masiki, komanso kukhala kwatokha. Tikamayesetsa kutsatira malangizowa, timasonyeza kuti timayamikira mphatso ya moyo imene Mulungu anatipatsa.

12. Kodi mfundo ya pa Miyambo 14:15, imatithandiza bwanji kusankha zomwe tiyenera kumvera pa nthawi yangozi?

12 Pa nthawi ya ngozi zosiyanasiyana tingamve nkhani zabodza kuchokera kwa anzathu, anthu oyandikana nawo nyumba komanso kwa ofalitsa nkhani. M’malo mokhulupirira “mawu alionse” amene tamva, tingachite bwino kumvera malangizo odalirika ochokera kuboma komanso kwa a zaumoyo. (Werengani Miyambo 14:15.) Bungwe Lolamulira komanso maofesi a nthambi, amayesetsa kufufuza mfundo zolondola asanapereke malangizo okhudza misonkhano yampingo komanso ntchito yolalikira. (Aheb. 13:17) Kutsatira malangizowa kumathandiza kuti ifeyo komanso anthu ena tikhale otetezeka. Timathandizanso kuti mpingo ukhale ndi mbiri yabwino m’dera lathu.​—1 Pet. 2:12.

MUZIKONZEKERA KUPEWA MAGAZI

13. Kodi timasonyeza bwanji kuti timalemekeza moyo tikamamvera lamulo la Yehova pa nkhani ya magazi?

13 A Mboni za Yehova amadziwika kuti amalemekeza kupatulika kwa magazi. Timamvera lamulo la Yehova lokhudza magazi pokana kuikidwa magazi ngakhale pamene tikufunika thandizo lamwamsanga lamankhwala. (Mac. 15:28, 29) Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti timafuna kufa. M’malomwake timayamikira mphatso yamoyo imene Mulungu anatipatsa. Timafuna thandizo labwino la mankhwala loperekedwa ndi achipatala omwe amakhala okonzeka kutithandiza popanda kuikidwa magazi.

14. Kodi tingachepetse bwanji kufunika koti tipatsidwe thandizo lalikulu la mankhwala?

14 Tikamasamalira thanzi lathu pochita zinthu zomwe takambirana munkhaniyi, tingachepetse kufunika koti tichitidwe opaleshoni, kapena kulandira thandizo lalikulu lamankhwala. Ndipo tikakhala ndi thupi lathanzi, timachira mofulumira tikachitidwa opaleshoni. Tingachepetsenso kufunika koti tichitidwe opaleshoni pochotsa zinthu zimene zingachititse ngozi kunyumba ndiponso kuntchito komanso kutsatira mosamala malamulo apamsewu.

Chifukwa chakuti timaona kuti moyo ndi wamtengo wapatali timalemba khadi lathu la DPA n’kumayenda nalo nthawi zonse (Onani ndime 15) d

15. (a) N’chifukwa chiyani n’zofunika kumayenda ndi khadi lathu lomwe lili ndi mfundo zogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu panopo? (Onaninso chithunzi.) (b) Mogwirizana ndi zimene taona muvidiyo, kodi tingatani kuti tisankhe bwino pa nkhani ya thandizo lachipatala lokhudza magazi?

15 Popeza timakonda mphatso ya moyo, timalemba Khadi Lopatsa Munthu Mphamvu Zondiimira pa Thandizo Lakuchipatala (onani zimene ndalemba m’katimu), n’kumayenda nalo nthawi zonse. b Pakhadili timafotokozapo zosankha zathu pa nkhani ya magazi komanso thandizo lina la mankhwala. Kodi zimene munalemba pakhadi lanu zikugwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanu panopa? Ngati mukufunika kulemba kapena kukonzanso zimene zili pakhadi lanu, musazengereze. Kulemba zomveka bwino pakhadi lathu kungachititse kuti tisachedwe kulandira thandizo lachipatala. Izi zingathandizenso kuti tipewe kusamvetsetsana ndi madokotala n’cholinga choti tisalandire thandizo lomwe lingaike moyo wathu pangozi. c

16. Kodi tingatani ngati sitikudziwa mmene tingalembere khadi la DPA?

16 Kaya ndife achinyamata kapena tili ndi thanzi labwino, tonsefe tikhoza kuchita ngozi ndiponso kudwala. (Mlal. 9:11) Choncho ndi chinthu chanzeru kulemba khadi lathu la DPA. Ngati simukudziwa mmene mungalembere khadili, mungapemphe akulu amumpingo wanu kuti akuthandizeni. Iwo angakuthandizeni kudziwa mmene mungalembere khadili, koma sangakusankhireni zochita pa nkhani ya thandizo lachipatala loyenera kulandira chifukwa umenewo ndi udindo wanu. (Agal. 6:4, 5) Komabe akuluwo angakuthandizeni kuti mumvetse zimene mwasankhazo komanso kuti muzilembe bwino.

TIZIKHALA OLOLERA

17. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife ololera pa nkhani yosankha thandizo lachipatala?

17 Nthawi zambiri zimene timasankha pa nkhani yokhudza thanzi lathu kapena thandizo lachipatala, zimakhala zogwirizana ndi chikumbumtima chathu chophunzitsidwa bwino Baibulo. (Mac. 24:16; 1 Tim. 3:9) Tikamasankha kapena kukambirana ndi ena nkhani zimenezi, tingachite bwino kumatsatira mfundo ya pa Afilipi 4:5, yomwe imati: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.” Tikakhala ololera sitimadera nkhawa kwambiri zokhudza thanzi lathu kapena kukakamiza ena kuti aziyendera maganizo athu pa nkhani yokhudza thandizo lachipatala. Timakonda komanso kulemekeza abale ndi alongo athu ngakhale zosankha zawo zitakhala zosiyana ndi zathu.​—Aroma 14:10-12.

18. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mphatso ya moyo?

18 Tingasonyeze kuti timayamikira Yehova yemwe ndi Mwiniwake wa moyo, pouteteza komanso kumamutumikira ndi mtima wonse. (Chiv. 4:11) Panopa timalimbanabe ndi zinthu ngati matenda komanso mavuto ena. Koma Mlengi wathu sankafuna kuti tizikhala moyo woterowu. Posachedwapa atipatsa moyo wosatha wopanda imfa komanso zowawa. (Chiv. 21:4) Koma panopa timaona kuti ndi mwayi wamtengo wapatali kukhala ndi moyo komanso kumatumikira Atate wathu wachikondi Yehova.

NYIMBO NA. 140 Tidzapeza Moyo Wosatha

a Nkhaniyi itithandiza kuti tiziyamikira kwambiri mphatso ya moyo imene Mulungu anatipatsa. Tiona njira zimene tingatsatire kuti tikhale athanzi komanso tidziteteze pakachitika ngozi za m’chilengedwe ndiponso zimene tingachite kuti tipewe ngozi zina zoopsa. Tionanso mmene tingakonzekerere ngati titafunika thandizo lachipatala lamwamsanga.

b Khadili limadziwikanso kuti DPA.

d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale wachinyamata akulemba khadi la DPA ndipo akuonetsetsa kuti nthawi zonse akuyenda nalo.