Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

[kuchokera kumanzere] Marcelo, Yomara, ndi Hiver, aliyense wanyamula voliyumu ya Chisipanishi ya Baibulo la Dziko Latsopano ya zilembo za anthu osaona

Anaona Chikondi cha Abale ndi Alongo

Anaona Chikondi cha Abale ndi Alongo

YOMARA ndi azichimwene ake awiri Marcelo ndi Hiver amakhala m’mudzi wina waung’ono ku Guatemala. Yomara anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni ndipo patapita nthawi azichimwene akenso anayamba kuphunzira. Koma panali vuto. Onse atatu ali ndi vuto losaona ndipo sankadziwa kuwerenga zilembo za anthu osaona. Choncho amene ankawaphunzitsa Baibulo, ankawawerengera ndime komanso mavesi pa phunziro lililonse.

Zinalinso zovuta kuti azipezeka pamisonkhano yampingo. Sakanatha kuyenda okha ulendo wa 40 minitsi kupita ku Nyumba ya Ufumu yapafupi. Koma abale ankaonetsetsa kuti akuwathandiza kuti azipezeka pamisonkhano yonse. Iwo atayamba kukamba nkhani pamisonkhano ya mkati mwa mlungu, abale ankawathandiza kuloweza nkhani zawozo.

Mu May 2019, misonkhano yampingo inayamba kuchitikira m’mudzi mwawo. Pa nthawiyo banja lina lomwe linkachita upainiya wokhazikika linasamukira m’mudziwo. Iwo anakonza kuti aphunzitse anthu atatuwa kulemba ndi kuwerenga zilembo za anthu osaona ngakhale kuti nawonso sankadziwa mmene angachitire zimenezi. Choncho anapita ku laibulale kuti akapeze mabuku ophunzitsa kulemba ndi kuwerenga zilembozi komanso kuti adziwe mmene angaphunzitsire ena.

Marcelo akuyankha pamisonkhano yampingo

Patangopita miyezi yochepa, anthu atatuwo anayamba kudziwa kuwerenga zilembozi ndipo zimenezi zinawathandiza kuti apite patsogolo mwamsanga. Panopa Yomara, Marcelo ndi Hiver akuchita upainiya wokhazikika ndipo Marcelo ndi mtumiki wothandiza. Kwa mlungu wonse iwo amakhala otanganidwa ndi zinthu zokhudza kulambira. Khama lawo limathandizanso ena kukhala akhama.

Atatuwa amayamikira kwambiri chikondi cha abale ndi alongo a mumpingo mwawo. Yomara ananena kuti, “Kungoyambira pamene tinakumana ndi a Mboni, iwo akhala akutisonyeza chikondi chenicheni.” Marcelo anawonjezera kuti, “Tili ndi anzathu abwino kwambiri kumpingo ndipo tili m’banja lapadziko lonse lokondana komanso logwirizana.” Yomara ndi azichimwene ake akuyembekezera mwachidwi kudzaona Yehova akukonza dzikoli kukhala labwino.​—Sal. 37:10, 11; Yes. 35:5.