NKHANI YOPHUNZIRA 7
‘Imva Mawu a Anthu Anzeru’
“Tchera khutu lako ndi kumva mawu a anthu anzeru.”—MIY. 22:17.
NYIMBO NA. 123 Tizigonjera Mulungu Mokhulupirika
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1. Kodi tingapatsidwe malangizo m’njira ziti, nanga n’chifukwa chiyani tonsefe timafunika kulangizidwa?
TONSEFE timafunika kupatsidwa malangizo nthawi ndi nthawi. Nthawi zina tingapemphe munthu amene timamulemekeza kuti atipatse malangizo. Nthawi zinanso m’bale angabwere kudzatiuza kuti tayamba kuyenda “njira yolakwika” imene tingadzanong’oneze nayo bondo. (Agal. 6:1) Komanso tingapatsidwe malangizo podzudzulidwa chifukwa cholakwitsa zina zake. Kaya tapatsidwa malangizo m’njira yotani, tiyenera kumvera. Zimenezi zingachititse kuti zinthu zitiyendere bwino komanso kuti tipulumutse moyo wathu.—Miy. 6:23.
2. Mogwirizana ndi Miyambo 12:15, n’chifukwa chiyani tiyenera kumvera malangizo?
2 Lemba lomwe likutsogolera nkhaniyi limatilimbikitsa kumvera “mawu a anthu anzeru.” (Miy. 22:17) Palibe munthu amene amadziwa chilichonse ndipo nthawi zonse pamakhala munthu amene akudziwa zambiri kuposa ifeyo. (Werengani Miyambo 12:15.) Choncho tikamamvera malangizo timasonyeza kuti ndife odzichepetsa. Zimasonyezanso kuti timazindikira zimene sitingakwanitse komanso kuti timafunika kuthandizidwa kuti tikwaniritse zolinga zathu. Mfumu yanzeru Solomo, mouziridwa inalemba kuti: ‘Aphungu akachuluka zolingalira zimakwaniritsidwa.’—Miy. 15:22.
3. Kodi tingapatsidwe malangizo m’njira ziti?
3 Tikhoza kupatsidwa malangizo achindunji kapenanso osakhala achindunji. Kodi tikutanthauza chiyani tikati malangizo osakhala achindunji? Tingawerenge zinazake m’Baibulo kapena m’mabuku athu zomwe zingachititse kuti tiganizire zimene tikuchita n’kusintha. (Aheb. 4:12) Pamenepa tingati tapatsidwa malangizo osakhala achindunji. Nanga tikutanthauza chiyani tikati kupatsidwa malangizo mwachindunji? Mkulu kapena m’bale wina angatiuze zinthu zimene tikufunika kukonza. Pamenepatu tingakhale tikupatsidwa malangizo achindunji. Ngati munthu wina amatikonda kwambiri mpaka kufika potipatsa malangizo ochokera m’Baibulo, tingasonyeze kuti tikuyamikira pomvetsera zimene akufuna kutiuza komanso kutsatira malangizo amene watipatsa.
4. Mogwirizana ndi Mlaliki 7:9, kodi tiyenera kupewa kuchita chiyani tikapatsidwa malangizo?
4 Kunena zoona zingakhale zovuta kuvomereza malangizo amene tikupatsidwa mwachindunji. Mwinanso tikhoza kukhumudwa. Chifukwa chiyani? Ngakhale kuti timavomereza kuti si ife angwiro, komabe zingativute kuvomereza malangizo, munthu wina akatiuza zenizeni zimene talakwitsa. (Werengani Mlaliki 7:9.) Tikhoza kumadziikira kumbuyo. Mwinanso tingamakaikire zolinga za munthu amene watipatsa malangizoyo kapenanso kukhumudwa ndi mmene watipatsira. Tikhozanso kuyamba kumupezera zifukwa n’kumanena kuti: ‘Kodi iyeyu ndi ndani kuti andipatse malangizo? Nayenso amalakwitsa zinthu.’ Komanso ngati malangizo amene tapatsidwa sanatisangalatse, sitingawamvere komanso mwina tikhoza kukafunsa kwa munthu wina amene angatipatse malangizo amene angatikomere.
5. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
5 Munkhaniyi tikambirana zitsanzo za m’Baibulo za anthu amene anakana ndi amene anavomera malangizo. Tionanso zimene zingatithandize kuti tizivomera malangizo ndiponso mmene kuchita zimenezo kungatithandizire.
ANTHU AMENE ANAKANA MALANGIZO
6. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Rehobowamu anachita atapatsidwa malangizo?
6 Taganizirani chitsanzo cha Rehobowamu. Ataikidwa kukhala mfumu ya Isiraeli, anthu ake anabwera kudzamupempha kuti awachepetsereko ntchito imene bambo ake Solomo, anawalamula kuti azigwira. Rehobowamu anachita zinthu mwanzeru pofunsa amuna achikulire a mu Isiraeli kuti amuthandize kudziwa mmene angawayankhire anthuwo. Amuna achikulirewo anamulangiza kuti ngati angamvere zimene amupemphazo, anthuwo adzapitiriza kukhala kumbali yake. (1 Maf. 12:3-7) Koma zikuoneka kuti Rehobowamu sanasangalale ndi malangizo amene anapatsidwa, choncho anakafunsa malangizo kwa amuna amsinkhu wake. Amunawo ayenera kuti anali a zaka za m’ma 40, choncho n’kutheka kuti ankadziwako zinthu zina pa moyo. (2 Mbiri 12:13) Koma pa nthawiyi iwo anapatsa Rehobowamu malangizo olakwika. Anamulangiza kuti awawonjezere anthuwo ntchito. (1 Maf. 12:8-11) Popeza kuti anapatsidwa malangizo osiyana, Rehobowamu akanatha kupempha Yehova kuti amuthandize kudziwa malangizo oyenera kutsatira. M’malomwake iye anasankha malangizo amene anamusangalatsa ndipo anamvera zimene amuna amsinkhu wake aja anamuuza. Zotsatira zake n’zakuti iyeyo limodzi ndi Aisiraeli anakumana ndi mavuto. Ifenso si nthawi zonse pamene tingapatsidwe malangizo omwe akutisangalatsa. Komabe ngati ali ochokera m’Mawu a Mulungu tiyenera kuwavomereza.
7. Kodi zimene zinachitikira Mfumu Uziya zikutiphunzitsa chiyani?
7 Mfumu Uziya anakana malangizo. Iye analowa mbali ina ya kachisi wa Yehova yomwe ndi ansembe okha ankaloledwa kulowamo kuti akafukize nsembe. Ansembewo anamuuza kuti: “Mfumu Uziya, si ntchito yanu kufukiza kwa Yehova koma ntchito yofukizayi ndi ya ansembe.” Kodi Uziya anatani atauzidwa zimenezi? Iye akanatsatira malangizowo modzichepetsa n’kutuluka nthawi yomweyo m’kachisimo, mwina Yehova akanamukhululukira. M’malomwake “Uziya anakwiya kwambiri.” N’chifukwa chiyani iye anakana kulandira malangizo? Mwachionekere ankaganiza kuti ali ndi ufulu wochita chilichonse chifukwa ndi mfumu. Koma Yehova sankaona choncho. Chifukwa cha khalidwe lake lodzikudza, mfumu Uziya inakanthidwa ndi khate ndipo “inakhalabe yakhate mpaka tsiku limene inamwalira.” (2 Mbiri 26:16-21) Zimene zinachitikira Uziya zikutiphunzitsa kuti kaya ndife ndani, Yehova angasiye kutikonda ngati titakana kumvera malangizo a m’Baibulo.
ANTHU AMENE ANAMVERA MALANGIZO
8. Kodi Yobu anatani atapatsidwa malangizo?
8 Mosiyana ndi zitsanzo zoipa zimene takambiranazi, m’Baibulo mulinso zitsanzo zabwino za anthu amene anadalitsidwa chifukwa chomvera malangizo. Taganizirani za Yobu. Ngakhale kuti anali woopa Mulungu sanali wangwiro. Chifukwa chopanikizika iye analankhula zinthu zina zolakwika. Choncho analandira malangizo osapita mbali kuchokera kwa Elihu komanso Yehova. Kodi Yobu anatani? Anadzichepetsa n’kumvera malangizowo. Iye anati: “Ndinalankhula, koma sindinali kuzindikira . . . ndikubweza mawu anga, ndipo ndikulapa m’fumbi ndi m’phulusa.” Yehova anadalitsa Yobu chifukwa chochita zinthu modzichepetsa.—Yobu 42:3-6, 12-17.
9. Kodi Mose anasonyeza bwanji chitsanzo chabwino pa nkhani yomvera malangizo?
9 Mose ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha munthu amene anavomera kuwongoleredwa atalakwitsa kwambiri zinthu. Pa nthawi ina, iye anakwiya kwambiri ndipo sanalemekeze Yehova. Chifukwa cha zimenezi anataya mwayi wolowa m’dziko lolonjezedwa. (Num. 20:1-13) Mose atapempha Yehova kuti asinthe maganizo ake pankhaniyi, iye anamuuza kuti: “Usatchulenso nkhani imeneyi kwa ine.” (Deut. 3:23-27) Mose sanakwiye nazo zimenezi. M’malomwake anavomereza zimene Yehova anasankha ndipo iye anapitiriza kumugwiritsa ntchito potsogolera Aisiraeli. (Deut. 4:1) Yobu ndi Mose ndi zitsanzo zabwino kwambiri zimene tingatengere pa nkhani yovomera kupatsidwa malangizo. Yobu anasintha mmene ankaonera zinthu ndipo sanadziikire kumbuyo. Mose anasonyeza kuti anavomera malangizo amene Yehova anamupatsa pokhalabe wokhulupirika ngakhale kuti anali atataya mwayi umene unali wamtengo wapatali kwa iye.
10. (a) Kodi lemba la Miyambo 4:10-13, limasonyeza kuti timapindula bwanji tikavomereza kulandira malangizo? (b) Kodi anthu ena asonyeza bwanji kuti amaona moyenera malangizo amene amapatsidwa?
10 Timapindula kwambiri tikamatsanzira anthu okhulupirika monga Yobu ndi Mose. (Werengani Miyambo 4:10-13.) Abale ndi alongo athu ambiri akhala akuwatsanzira polola kulangizidwa. Taonani zimene m’bale wina wa ku Congo dzina lake Emmanuel ananena pa zimene anachenjezedwa. Iye anati: “Abale olimba mwauzimu mumpingo wathu anaona kuti ubwenzi wanga ndi Yehova unali utatsala pang’ono kusokonekera ndipo anandithandiza. Ndinagwiritsa ntchito malangizo amene anandipatsa ndipo ndinapewa mavuto ambiri.” * Ponena za malangizo amene wakhala akupatsidwa, mpainiya wina wa ku Canada dzina lake Megan ananena kuti: “Si nthawi zonse pamene malangizowo ankakhala osangalatsa kumva koma ndi malangizo amene ndinkafunikira.” M’bale wina wa ku Croatia dzina lake Marko ananena kuti: “Ndinataya mwayi wautumiki komabe ndikaganizira, ndimaona kuti malangizo amene ndinapatsidwa pa nthawiyo anandithandiza kuti ndikonzenso ubwenzi wanga ndi Yehova.”
11. Kodi M’bale Karl Klein ananena chiyani zokhudza kuvomereza malangizo?
11 Chitsanzo china cha munthu amene anapindula chifukwa chovomera kupatsidwa malangizo ndi M’bale Karl Klein, amene ankatumikira m’Bungwe Lolamulira. Munkhani yofotokoza mbiri ya moyo wake, M’bale Klein anatchula za nthawi ina pamene anapatsidwa malangizo amphamvu ndi M’bale Joseph F. Rutherford yemwe anali mnzake wapamtima. M’bale Klein anavomereza kuti poyamba sanalandire bwino malangizowo. Iye anati: “Pa nthawi ina M’bale Rutherford atandiona, mosangalala anati, ‘Mulibwanji M’bale Klein!’ Koma chifukwa chakuti malangizo aja ankandiwawabe, ndinayankha moniyo monyinyirika. Ndiye iye anati, ‘M’bale Klein, samalani! Mdyerekezi akufuna akukoleni!’ Mwamanyazi ndinayankha kuti, ‘Sindinakhumudwe ndi kalikonse M’bale Rutherford.’ Koma iye ankadziwa kuti ndinali nditakhumudwa choncho anabwerezanso kundichenjeza kuti, ‘Chabwino, ingokhalani osamala. Mdyerekezi akufuna kukukolani.’ Iyetu ankanena zoona. Ngati tingapitirize kukwiyira m’bale wathu makamaka chifukwa chakuti watiuza zinthu zimene amafunika kutiuza . . . , timakhala tikumupatsa malo Mdyerekezi kuti atikole m’misampha yake.” * (Aef. 4:25-27) M’bale Klein anavomereza malangizo amene M’bale Rutherford anamupatsa ndipo anapitirizabe kukhala ogwirizana.
KODI N’CHIYANI CHINGATITHANDIZE KUTI TIZIVOMERA MALANGIZO?
12. Kodi kudzichepetsa kungatithandize bwanji kuti tizivomera kupatsidwa malangizo? (Salimo 141:5)
12 Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizivomera kupatsidwa malangizo? Tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumakumbukira kuti si ife angwiro ndipo nthawi zina tingachite zinthu mosaganiza bwino. Monga taonera kale, Yobu ankaona zinthu molakwika. Koma pambuyo pake anasintha mmene ankaganizira ndipo Yehova anamudalitsa. N’chifukwa chiyani? Chifukwa Yobu anali wodzichepetsa. Iye anasonyeza kuti analidi wodzichepetsa povomera malangizo amene Elihu anamupatsa, ngakhale kuti Elihuyo anali wamng’ono kwa iye. (Yobu 32:6, 7) Kudzichepetsa kudzatithandiza kuti tigwiritse ntchito malangizo amene tapatsidwa ngakhale pamene tikuona kuti sitimayenera kupatsidwa malangizowo, kapenanso ngati amene watipatsa malangizoyo ndi wamng’ono kwa ife. Mkulu wina wa ku Canada ananena kuti: “Popeza sitimadziona ngati mmene ena amationera, kodi tingapite bwanji patsogolo ngati palibe amene akutipatsa malangizo?” Ndi ndani wa ife amene safuna kupita patsogolo pokulitsa makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa kapenanso pa ntchito yathu yolalikira?—Werengani Salimo 141:5.
13. Kodi tiyenera kumaona bwanji malangizo amene timapatsidwa?
13 Tiziona kuti kupatsidwa malangizo ndi umboni wakuti Yehova amatikonda. Yehova amatifunira zabwino. (Miy. 4:20-22) Iye akatipatsa malangizo kudzera m’Mawu ake, m’mabuku ofotokoza Baibulo kapena kudzera mwa Mkhristu mnzathu, amakhala akutisonyeza chikondi chake. Lemba la Aheberi 12:9, 10 limati, ‘amatilangiza kuti tipindule.’
14. Kodi tiyenera kumaganizira kwambiri chiyani tikamapatsidwa malangizo?
14 Tiziganizira kwambiri malangizowo osati mmene aperekedwera. Nthawi zina tingaone ngati munthu sanatipatse malangizo m’njira yoyenera. N’zoona kuti aliyense amene akufuna kupereka malangizo ayenera kuyesetsa kuchita zimenezo m’njira yabwino. * (Agal. 6:1) Ngati ndife amene tikulangizidwa, tingachite bwino kuganizira malangizo amene tapatsidwa, ngakhale titaona kuti munthu amene watipatsa malangizowo akanatha kuchita zimenezo m’njira yabwino. Mwina tingadzifunse kuti: ‘Ngakhale kuti sindinakonde njira imene wandipatsira malangizowo kodi pali zimene ndingaphunzirepo? Kodi ndinganyalanyaze zimene amene wandipatsa malangizoyo amalakwitsa, n’kugwiritsa ntchito malangizo amene waperekawo?’ Tingakhale anzeru ngati nthawi zonse timayesetsa kuti tizipindula ndi malangizo amene tapatsidwa.—Miy. 15:31.
MUZIPEMPHA MALANGIZO NDIPO MUDZAPINDULA KWAMBIRI
15. N’chifukwa chiyani tiyenera kupempha malangizo kwa ena?
15 Baibulo limatilimbikitsa kuti tizipempha malangizo. Lemba la Miyambo 13:10 limati: “Anthu amene amakhala pamodzi n’kumakambirana amakhala ndi nzeru.” Zimenezitu ndi zoona. Anthu amene amapempha malangizo m’malo modikira kuti ena awapatse malangizowo amapita patsogolo kwambiri mwauzimu kusiyana ndi anthu amene safufuza malangizo. Choncho muziyamba ndi inuyo kupempha ena kuti akupatseni malangizo.
16. Kodi tingapemphe malangizo pa zochitika ngati ziti?
16 Kodi ndi pa nthawi iti pamene tingapemphe malangizo kwa Akhristu anzathu? Tingapemphe malangizo pa zochitika ngati izi: (1) Mlongo wina akupempha wofalitsa waluso kuti apite naye kuphunziro la Baibulo ndipo kenako akumupempha malangizo amene angamuthandize kuti aziphunzitsa bwino. (2) Mlongo wina wosakwatiwa akufuna kugula zovala ndiye akupempha mlongo wina wolimba mwauzimu kuti amuthandize kusankha zovala zabwino. (3) M’bale wapemphedwa kuti akambe nkhani ya onse kwa nthawi yoyamba. Iye akupempha m’bale amene ali ndi luso lokamba nkhani kuti amvetsere nkhani yakeyo komanso kumupatsa malangizo amene angamuthandize kuwonjezera luso lake. Ngakhale m’bale amene wakhala akukamba nkhani kwa zaka zambiri angachite bwino kupempha malangizo kwa abale aluso n’kuwagwiritsa ntchito.
17. Kodi tingatani kuti tizipindula ndi malangizo amene tapatsidwa?
17 M’milungu kapena m’miyezi ikubwerayi tonsefe tikhoza kupatsidwa malangizo kaya achindunji kapena osakhala achindunji. Ngati zimenezi zitatichitikira tidzakumbukire mfundo zimene tangokambiranazi. Muzikhala odzichepetsa. Muziganizira kwambiri malangizo amene mwapatsidwa osati mmene aperekedwera ndipo muziwagwiritsa ntchito. Palibe amene amabadwa ali wanzeru. Koma ‘tikamamvera uphungu ndi kutsatira malangizo,’ Mawu a Mulungu amalonjeza kuti ‘tidzakhala anzeru.’—Miy. 19:20.
NYIMBO NA. 124 Tizikhulupirika Nthawi Zonse
^ ndime 5 Anthu a Yehova amazindikira kufunika kotsatira malangizo a m’Baibulo. Komabe si nthawi zonse pamene zimakhala zophweka kuvomereza malangizo. N’chifukwa chiyani zili choncho? Ndipo n’chiyani chingatithandize kuti tizipindula ndi malangizo amene timalandira?
^ ndime 10 Mayina ena asinthidwa.
^ ndime 11 Onani Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya October 1, 1984, tsamba 21-28.
^ ndime 14 Munkhani yotsatira tidzakambirana zimene munthu angachite kuti azipereka malangizo m’njira yabwino.