NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) February 2020
M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira April 6–May 3, 2020.
Atate Wathu Yehova Amatikonda Kwambiri
Tisamakayikire kuti Atate wathu Yehova amatikonda komanso kutisamalira ndipo sangatisiye.
Timakonda Kwambiri Atate Wathu Yehova
Onani zinthu zimene tingachite posonyeza kuti timakonda kwambiri Atate wathu Yehova.
Muzipewa Nsanje Kuti Muzikhala Mwamtendere
Nthawi zina tikhoza kumavutika ndi mtima wa nsanje. Onani zimene tingachite kuti tipewe nsanje n’kumakhala mwamtendere ndi anzathu.
Muzilola Kuti Yehova Azikutonthozani
Hana, mtumwi Paulo ndi Mfumu Davide ankavutika ndi nkhawa. Kodi tingaphunzire chiyani tikaganizira mmene Yehova anawatonthozera?
MBIRI YA MOYO WANGA
Ndadalitsidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Ndinaphunzira kwa Anthu Ena
Léonce Crépeault akufotokoza mmene chitsanzo cha anthu okhulupirika chinamuthandizira kuthetsa mantha ake komanso kusangalala ndi madalitso ambiri pa zaka pafupifupi 58 zimene wachita utumiki wa nthawi zonse.
Kodi Mukudziwa?
Kodi zimene asayansi apeza zikutsimikizira bwanji kuti Belisazara anali mfumu ku Babulo?

