Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzikhala Okhulupirika kwa Yehova

Muzikhala Okhulupirika kwa Yehova

“Yehova akhale pakati pa iwe ndi ine, ndi pakati pa ana ako ndi ana anga mpaka kalekale.”—1 SAM. 20:42.

NYIMBO: 125, 62

1, 2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yonatani ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kukhulupirika?

YONATANI ayenera kuti anadabwa kwambiri pamene Davide anapha Goliati. Kenako Davide anapita kwa Mfumu Sauli “ali ndi mutu wa [Goliati] m’manja mwake.” (1 Sam. 17:57) Mosakayikira, Yonatani anachita chidwi ndi Davide chifukwa anali mnyamata wolimba mtima kwambiri ndipo zinali zoonekeratu kuti Mulungu ankamuthandiza. Kenako anthu awiriwa anayamba kugwirizana kwambiri moti “anachita pangano, chifukwa Yonatani anali kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondera.” (1 Sam. 18:1-3) Ndiyeno Yonatani anakhala wokhulupirika kwa Davide moyo wake wonse.

2 Yonatani anapitiriza kukonda Davide ngakhale kuti Mulungu anamusankha kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli. Pamene Sauli ankafuna kupha Davide, Yonatani ankadera nkhawa kwambiri mnzakeyu. Choncho anapita kukamuona m’chipululu kumene ankabisala pafupi ndi Horesi. Iye anamulimbikitsa kuti azidalira Yehova ndipo anamuuzanso kuti: “Usachite mantha, . . . iwe ukhaladi mfumu ya  Isiraeli, ndipo ine ndidzakhala wachiwiri kwa iwe.”—1 Sam. 23:16, 17.

3. Kodi Yonatani ankaona kuti chofunika kwambiri n’chiyani, ndipo tikudziwa bwanji zimenezi? (Onani chithunzi patsamba 21.)

3 Tonsefe timaona kuti kukhulupirika ndi khalidwe lofunika kwambiri. Yonatani ndi chitsanzo chabwino pa nkhaniyi chifukwa anali wokhulupirika kwa Davide. Koma kodi n’chifukwa chiyani anali wokhulupirika kwa Davide m’malo momuchitira nsanje? N’chifukwa chakuti Yonatani analinso wokhulupirika kwa Yehova. Iye ankaona kuti kukhala wokhulupirika kwa Yehova ndi kofunika kuposa chilichonse. Paja analimbikitsa Davide kuti azidalira Yehova. Ndipotu onsewa anachita zinthu mogwirizana ndi pangano lawo lakuti: “Yehova akhale pakati pa iwe ndi ine, ndi pakati pa ana ako ndi ana anga mpaka kalekale.”—1 Sam. 20:42.

4. (a) Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizikhala osangalala? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

4 Ifenso tiziyesetsa kukhala okhulupirika kwa achibale athu, anzathu ndiponso abale ndi alongo mumpingo. (1 Ates. 2:10, 11) Koma chofunika kwambiri, tizikhala okhulupirika kwa Yehova chifukwa ndi amene anatipatsa moyo. (Chiv. 4:11) Tikamachita zimenezi timakhala osangalala. Koma tiyenera kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu ngakhale pamene takumana ndi mavuto. M’nkhaniyi tikambirana mmene chitsanzo cha Yonatani chingatithandizire kukhala okhulupirika kwa Yehova (1) munthu waudindo akamachita zolakwika, (2) posankha kuti tikhala okhulupirika kwa ndani, (3) ngati abale atichitira kapena kutiganizira molakwika ndiponso (4) ngati zinthu zavuta.

MUNTHU WAUDINDO AKAMACHITA ZOLAKWIKA

5. N’chifukwa chiyani Aisiraeli ankavutika kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu pamene Sauli anali mfumu?

5 Sauli, bambo a Yonatani, anali mfumu yosankhidwa ndi Mulungu. Koma pa nthawi ina anayamba kuchita zinthu zosakhulupirika ndipo Yehova sankasangalalanso naye. (1 Sam. 15:17-23) Komabe Yehova sanamuchotse pampando nthawi yomweyi. Choncho pa nthawiyi Aisiraeli ankavutika kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu chifukwa munthu amene anali “pampando wachifumu wa Yehova,” ankachita zoipa.—1 Mbiri 29:23.

6. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Yonatani anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova.

6 Koma Sauli atayamba kuchita zoipa, Yonatani anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova. (1 Sam. 13:13, 14) Pa nthawi ina mneneri Samueli ananena kuti: “Chifukwa cha dzina lake lalikulu, Yehova sadzasiya anthu ake.” (1 Sam. 12:22) Yonatani anasonyeza kuti ankakhulupirira mawuwa pamene gulu lankhondo la Afilisiti lapamagaleta okwana 30,000 linkafuna kumenyana ndi Aisiraeli. Sauli anali ndi asilikali 600 okha ndipo iye yekha ndi Yonatani ndi omwe anali ndi zida. Komabe Yonatani anakamenyana ndi gulu lina la Afilisiti ndipo anangopita ndi mtumiki wake. Iye anati: “Palibe chimene chingalepheretse Yehova kupulumutsa anthu ake pogwiritsa ntchito anthu ambiri kapena ochepa.” Yonatani ndi mtumiki wakeyo anapha Afilisiti 20. Kenako Mulungu anachititsa kuti ‘nthaka iyambe kugwedezeka.’ Izi zinasokoneza Afilisiti ndipo anayamba kuphana okhaokha. Choncho Yehova anadalitsa Yonatani chifukwa choti anali ndi chikhulupiriro ndipo Aisiraeli anapambana.—1 Sam. 13:5, 15, 22; 14:1, 2, 6, 14, 15, 20.

7. Kodi Yonatani anasonyeza bwanji kuti ankalemekeza bambo ake?

7 Ngakhale kuti Sauli anapitiriza kuchita zosakhulupirika, Yonatani ankamulemekezabe komanso kuchita naye zinthu zina. Mwachitsanzo, anapita naye kukamenya nkhondo poteteza anthu a Mulungu.—1 Sam. 31:1, 2.

8, 9. Kodi timasonyeza bwanji kuti ndife okhulupirika kwa Mulungu tikamalemekeza athu audindo?

8 Nafenso tingasonyeze kuti ndife okhulupirika  kwa Yehova tikamamvera akuluakulu a boma pa zinthu zoyenera. Tingachite zimenezi ngakhale kuti nthawi zina sachita zabwino. Mwachitsanzo, olamulira akhoza kukhala achinyengo, koma tiyenera kuwalemekezabe chifukwa Yehova amafuna kuti tizichita zimenezi. (Werengani Aroma 13:1, 2.) Komanso timasonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova tikamamvera anthu amene Yehova wawapatsa udindo.—1 Akor. 11:3; Aheb. 13:17.

Tikamalemekeza mwamuna kapena mkazi wathu amene si Mboni, timasonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova (Onani ndime 9)

9 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina wa ku South America, dzina lake Olga. [1] Iye ankalemekezabe mwamuna wake ngakhale kuti ankamuchitira zinthu zambiri zankhanza. Mwamunayo sankasangalala kuti mkazi wake ndi wa Mboni. Choncho nthawi zina ankamunyoza, kukana kulankhula naye komanso ankamuopseza kuti atenga ana awo n’kuchoka panyumba. Koma Olga sankabwezera zoipa zimene mwamuna wake ankachitazi. Ankayesetsa kukhala mkazi wabwino ndipo ankamuphikira mwamuna wakeyo, kumuchapira ndiponso kusamalira achibale ake. (Aroma 12:17) Nthawi zina mwamunayo akamapita kukacheza ndi achibale kapena anzake, ankapita naye limodzi. Komanso pamene mwamuna wakeyo ankapita kumaliro a bambo ake mumzinda wina, mlongoyu anakonzekera zonse zofunika ndipo iye ndi ana onse anapita naye limodzi. Ndiyeno pamene mwambo wa maliro unkachitika, anamudikira panja pa tchalitchi. Olga anapitirizabe kulemekeza mwamuna wakeyo ndiponso kukhala woleza mtima. Patapita nthawi, izi zinachititsa kuti mwamunayo asiye kumuchitira nkhanza. Panopa amamulimbikitsa kusonkhana, amakamusiya ku Nyumba ya Ufumu ndipo nthawi zina amasonkhana naye limodzi.—1 Pet. 3:1.

POSANKHA KUTI TIKHALA WOKHULUPIRIKA KWA NDANI

10. N’chifukwa chiyani Yonatani anasankha kukhala wokhulupirika kwa Davide?

10 Yonatani atadziwa kuti Sauli akufuna kupha Davide, anafunika kusankha kuti akhala wokhulupirika kwa ndani. Iye anali atachita pangano ndi Davide komanso ankafuna kuti azimvera bambo ake. Komabe Yonatani ankadziwa kuti Mulungu ankathandiza Davide osati Sauli. Choncho anakhala wokhulupirika kwa Davide. Ndiyeno anamuchenjeza kuti akabisale ndipo  kenako anauza Sauli zinthu zabwino zokhudza iyeyo.—Werengani 1 Samueli 19:1-6.

11, 12. Kodi kukonda Mulungu kungatithandize bwanji kukhala okhulupirika kwa iye?

11 Mlongo wina wa ku Australia dzina lake Alice anafunikanso kusankha kuti akhala wokhulupirika kwa ndani. Atayamba kuphunzira Baibulo ankakonda kuuza achibale ake zimene waphunzira. Kenako anawauzanso kuti sazikondwerera nawo Khirisimasi ndipo anawafotokozera chifukwa chake. Achibale akewo sanagwirizane nazo kwenikweni ndipo kenako anayamba kumukwiyira kwambiri chifukwa choti ankaganiza kuti wasiya kuwakonda. Alice anati: “Mayi anga anafika ponena kuti si inenso mwana wawo. Ndinadabwa ndi zimenezi ndipo zinandikhumudwitsa kwambiri chifukwa ndimakonda abale angawa. Komabe ndinatsimikiza kuti ndizikonda kwambiri Yehova ndi Mwana wake kuposa wina aliyense ndipo ndinabatizidwa pamsonkhano wotsatira.”—Mat. 10:37.

12 Sitiyeneranso kulola kuti mtundu wathu, sukulu yathu kapena timu yathu yamasewera zikhale zofunika kwambiri kwa ife moti n’kutilepheretsa kukhala okhulupirika kwa Yehova. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mnyamata wina dzina lake Henry amene amakonda kwambiri masewera enaake. Iye ankaimira sukulu yake pa masewerawa ndipo ankafunitsitsa kuti sukulu yawoyo ipambane. Henry anati: “Pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kukonda kwambiri masewerawa komanso sukulu yanga kuposa kutumikira Mulungu. Tinkasewera Loweruka ndi Lamlungu lililonse moti ndinkasowa nthawi yolalikira ndiponso yosonkhana. Choncho ndinasankha kuti ndisiye kusewera mu timu ya sukulu yathu.”—Mat. 6:33.

13. Kodi kukhala okhulupirika kwa Mulungu kungatithandize bwanji kuthetsa mavuto a m’banja?

13 Nthawi zina zimakhala zovuta kukhala okhulupirika kwa onse a m’banja lathu. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina dzina lake Ken. Iye anati: “Ndinkafuna kuti ndizipita pafupipafupi kukaona mayi anga amene ndi achikulire kwambiri. Ndinkafunanso kuti nthawi zina azibwera kudzakhala kunyumba kwathu. Komabe mayiwa ndi mkazi wanga sankagwirizana. Choncho zinali zovuta kuti ndichite zinthu zimene onse awiri angasangalale nazo. Koma kenako ndinazindikira kuti choyamba ndiyenera kukhala wokhulupirika kwa mkazi wanga. Ndiyeno ndinasankha kuti ndizichita zinthu zimene mkazi wanga angagwirizane nazo.” Ken ankafunitsitsa kukhala wokhulupirika kwa Mulungu ndiponso kuchita zinthu mogwirizana ndi Mawu ake. Choncho analimba mtima n’kufotokozera mkazi wakeyo chifukwa chake ayenera kuchitira zabwino mayiwo. Anafotokozeranso mayi akewo chifukwa chake ayenera kulemekeza mkazi wake.—Werengani Genesis 2:24; 1 Akorinto 13:4, 5.

NGATI ABALE ATICHITIRA KAPENA KUTIGANIZIRA MOLAKWIKA

14. Kodi Yonatani anakumana ndi vuto lotani?

14 Zimakhalanso zovuta kukhala wokhulupirika kwa Mulungu ngati m’bale waudindo watiganizira molakwika. Yonatani anakumananso ndi vuto ngati limeneli. Mfumu Sauli, yemwe anali wodzozedwa wa Yehova, ankadziwa kuti Yonatani ankagwirizana kwambiri ndi Davide koma sankadziwa chifukwa chake. Choncho pa nthawi ina, Sauli anakwiya kwambiri ndipo anachititsa manyazi Yonatani pa maso pa anthu. Koma Yonatani sanabwezere. Iye anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu komanso kwa Davide yemwe kenako anakhala mfumu ya Isiraeli.—1 Sam. 20:30-41.

15. Kodi tizitani abale akatichitira zolakwika?

15 Abale amene akutsogolera mumpingo amayesetsa kuchitira aliyense zinthu zachilungamo. Komabe popeza anthuwa si angwiro, nthawi  zina angatichitire kapena kutiganizira molakwa. (1 Sam. 1:13-17) Zoterezi zikachitika, tiziyesetsa kukhalabe okhulupirika kwa Yehova.

NGATI ZINTHU ZAVUTA

16. Kodi tiyenera kusonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Mulungu pa zinthu ziti?

16 Sauli ankauza Yonatani kuti achite zinthu zimene zikanapangitsa kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli. (1 Sam. 20:31) Koma Yonatani anali wokhulupirika kwa Mulungu ndipo anapitiriza kugwirizana ndi Davide m’malo molakalaka kuti adzakhale mfumu. Iye sanasinthe zimene analonjezana ndi Davide. Tiyeni tizitsanzira Yonatani ndipo tizikumbukira kuti Yehova amakonda munthu amene “akalumbira kuchita zinthu zimene kenako zakhala zoipa kwa iye, sasintha malingaliro ake.” (Sal. 15:4) Mwachitsanzo, ngati tinagwirizana zinazake pa nkhani za bizinezi, tiyenera kukhala okhulupirika kwa Mulungu poyesetsa kukwaniritsa zomwe tinagwirizanazo. Tiyenera kuchita zimenezi ngakhale pamene zinthu sizikuyenda mmene tinkaganizira. Nanga kodi tingatani ngati banja lathu silikuyenda bwino ngati mmene tinkayembekezera? Ngati timakondadi Mulungu, tidzayesetsa kukhalabe okhulupirika kwa mnzathuyo.—Werengani Malaki 2:13-16.

Tikamakwaniritsa zimene tinagwirizana pa nkhani za bizinezi, timasonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Mulungu (Onani ndime 16)

17. Kodi taphunzira chiyani m’nkhaniyi?

17 Tiyeni tonse tiziyesetsa kutsanzira Yonatani pa nkhani yokhala okhulupirika kwa Mulungu. Tizikhalabe okhulupirika zinthu zikavuta. Komanso tizikhalabe okhulupirika kwa anthu a Mulungu, ngakhale atatikhumudwitsa. Tikamachita zimenezi, timasangalatsa Yehova ndipo ifenso timasangalala kwambiri. (Miy. 27:11) Ndipotu tikapitiriza kukhala okhulupirika kwa Yehova, adzatidalitsa ndipo zinthu zidzatiyendera bwino. M’nkhani yotsatira tidzakambirana zimene tingaphunzire kwa anthu ena a m’nthawi ya Davide amene anali okhulupirika komanso ena amene anali osakhulupirika.

^ [1] (ndime 9) Mayina ena asinthidwa.