Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata, “Pitirizani Kukonza Chipulumutso Chanu”

Achinyamata, “Pitirizani Kukonza Chipulumutso Chanu”

“Monga mmene mwakhalira omvera nthawi zonse, . . . pitirizani kukonza chipulumutso chanu, mwamantha ndi kunjenjemera.”​—AFIL. 2:12.

NYIMBO: 133, 135

1. Kodi kubatizidwa n’kofunika bwanji? (Onani chithunzi choyambirira.)

CHAKA chilichonse anthu ambirimbiri amabatizidwa. Ambiri mwa anthuwa amakhala achinyamata ndipo ena ndi oti anabadwira m’banja la Mboni. Ngati inunso munabatizidwa, munachita bwino kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti Mkhristu aliyense amafunika kubatizidwa kuti adzapulumuke.​—Mat. 28:19, 20; 1 Pet. 3:21.

2. N’chifukwa chiyani simuyenera kuopa kubatizidwa?

2 Munthu akabatizidwa amapeza madalitso ambiri koma amakhalanso ndi udindo waukulu. Tikutero chifukwa chakuti pa tsiku la ubatizo, munthu amayankha kuti “inde” pa funso lakuti: “Pa maziko a nsembe ya Yesu Khristu, kodi munalapa machimo anu ndi kudzipereka kwa Yehova kuti muchite chifuniro chake?” Ndiyeno pamene munabatizidwa munasonyeza kuti mwadzipereka kwa Yehova. Munalonjeza Yehova kuti muzimukonda komanso muziika zofuna zake patsogolo nthawi zonse. Lonjezo limenelitu ndi lalikulu kwambiri. Koma simuyenera kuganiza kuti munalakwitsa kulipanga. Simudzanong’oneza bondo ngakhale pang’ono chifukwa chodzipereka m’manja mwa Yehova. Tikutero chifukwa chakuti munthu amene sakutumikira Yehova amalamuliridwa ndi Satana. Ndipo Satanayo safunira anthu zabwino. Iye angasangalale mutakana ulamuliro wa Yehova n’kukhala kumbali yake ndipo pa mapeto pake musadzapeze moyo wosatha.

3. Kodi munthu akadzipereka kwa Yehova amakhala ndi mwayi uti?

3 Koma taganizirani madalitso amene muli nawo chifukwa chodzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa. Popeza munapereka moyo wanu kwa Yehova, mukhoza kunena molimba mtima kwambiri kuti: “Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa. Munthu wochokera kufumbi angandichite chiyani?” (Sal. 118:6) Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala kumbali ya Yehova n’kumadziwa kuti akusangalala nanu.

UDINDO WA ALIYENSE PAYEKHA

4, 5. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kudzipereka kwa Mulungu ndi udindo wa aliyense payekha? (b) Kodi Mkhristu aliyense angakumane ndi mayesero ati?

4 Popeza kuti munabatizidwa, panokha muli ndi udindo wolimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Ubwenziwu suli ngati bilu ya magetsi imene makolo akangolipira ndiye kuti inunso muzigwiritsa nawo ntchito. Choncho ngakhale kuti mukukhalabe ndi makolo anu, udindo wochita zinthu zokuthandizani kudzapulumuka ndi wanu. Muyenera kukumbukira mfundoyi chifukwa chakuti simungadziwe zimene mungadzakumane nazo m’tsogolo. Mwachitsanzo, ngati munabatizidwa muli wamng’ono, pamene mukukula mukhoza kuyamba kulakalaka zinthu zina komanso kukumana ndi mayesero osiyanasiyana. Pa nkhaniyi, mtsikana wina anati: “Kamwana sikangaganize kuti kukhala wa Mboni za Yehova n’koipa chifukwa choti kakumanidwa keke imene ana anzake akudya pa tsiku lawo lobadwa. Koma akamakula n’kuyamba kulakalaka kugonana, amafunika kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu chomuthandiza kukumbukira kuti kutsatira malamulo a Yehova n’kothandiza nthawi zonse.”

5 N’zoona kuti munthu wamsinkhu uliwonse akhoza kukumana ndi mayesero atsopano. Ngakhale anthu amene anabatizidwa atakula kale amakumananso ndi mayesero amene sankawayembekezera. Akhoza kukumana ndi mavuto a m’banja, matenda kapena mavuto ena okhudza ntchito. Choncho munthu aliyense, kaya ndi wamkulu kapena wamng’ono, adzakumana ndi mayesero enaake ndipo adzafunika kusonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa Yehova.​—Yak. 1:12-14.

6. (a) Kodi munthu amene wadzipereka kwa Yehova amalonjeza kuchita chiyani? (b) Kodi lemba la Afilipi 4:11-13 lingakuthandizeni bwanji?

6 Kukumbukira kuti simungasinthe zimene munalonjeza podzipereka kwa Yehova kungakuthandizeni kukhalabe wokhulupirika. Paja munalonjeza Wolamulira chilengedwe chonse kuti mudzamutumikirabe ngakhale makolo kapena anzanu atasiya kumutumikira. (Sal. 27:10) Yehova angakuthandizeni nthawi zonse kukhala ndi mphamvu zoti muzikwaniritsa zimene munalonjezazo.​—Werengani Afilipi 4:11-13.

7. Kodi mawu oti “pitirizani kukonza chipulumutso chanu, mwamantha ndi kunjenjemera” amatanthauza chiyani?

7 Yehova amafuna kuti mukhale mnzake. Koma muyenera kuchita khama kuti mukhalebe pa ubwenzi ndi Yehova komanso kuti mudzapulumuke. N’chifukwa chake lemba la Afilipi 2:12 limati: “Pitirizani kukonza chipulumutso chanu, mwamantha ndi kunjenjemera.” Mawuwa akusonyeza kuti muyenera kuganizira zimene zingakuthandizeni kukhala wokhulupirika kwa Yehova zivute zitani. Si bwino kudzidalira pa nkhani imeneyi chifukwa ngakhale anthu amene akhala akutumikira Yehova kwa nthawi yaitali amasokonezeka. Ndiye kodi mungakonze bwanji chipulumutso chanu?

KUPHUNZIRA BAIBULO N’KOFUNIKA

8. Kodi tiyenera kuchita chiyani pophunzira Baibulo, nanga kuchita zimenezi kungatithandize bwanji?

8 Kuti munthu akhale pa ubwenzi ndi Yehova pamafunika kumvetsera mawu ake komanso kulankhula naye. Timamvetsera mawu a Yehova makamaka tikamaphunzira Baibulo patokha. Timachita zimenezi powerenga ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu komanso mabuku ofotokoza Baibulo. Koma tizikumbukiranso kuti pophunzira Baibulo tisamakhale ngati munthu amene akungofuna kuloweza zinazake kuti adzakhoze mayeso. Tizikhala ngati munthu amene ali pa ulendo wopita kudera lachilendo n’cholinga choti akafufuze zinthu zochititsa chidwi. Mukamafufuza mfundo zatsopano zokhudza Yehova mudzatha kumuyandikira ndipo iye adzakuyandikiraninso.​—Yak. 4:8.

Kodi mumamvetsera mawu a Yehova komanso kulankhula naye? (Onani ndime 8-11)

9. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimakuthandizani inuyo pophunzira Baibulo?

9 Gulu la Yehova latipatsa zinthu zambiri zotithandiza kuti tizipindula pophunzira Baibulo. Mwachitsanzo, pawebusaiti yathu pali nkhani zakuti “Zoti Muchite Pophunzira Baibulo.” Nkhani zimenezi zimapezeka pamene alemba kuti “Achinyamata” ndipo zikhoza kukuthandizani kuti muzipindula kwambiri pophunzira Baibulo. Pawebusaitiyi palinso nkhani zakuti “Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?” zimene zingakuthandizeni pophunzira. Nkhani zimenezi zikhoza kukuthandizani kuti musamakayikire zimene mumakhulupirira ndipo muzitha kuzifotokoza mosavuta kwa anthu ena. Mfundo zina zothandiza mungazipeze mu Galamukani ya April 2009 pa nkhani yakuti “Kodi Ndingatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzindisangalatsa?” yomwe ili pansi pa mutu wakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa.” Kunena zoona, kuphunzira Mawu a Mulungu komanso kusinkhasinkha kungatithandize kuti tikonze chipulumutso chathu.​—Werengani Salimo 119:105.

KUPEMPHERA N’KOFUNIKA

10. N’chifukwa chiyani Mkhristu aliyense wobatizidwa ayenera kupemphera?

10 Monga tanena kale, munthu akamaphunzira Baibulo amamvetsera mawu a Yehova koma akamapemphera amalankhula naye. Mkhristu sayenera kuganiza kuti kupemphera ndi mwambo chabe kapena chithumwa chothandiza kuti zinthu zinazake zitiyendere bwino. M’malomwake ayenera kuona kuti ndi njira imene imatithandiza kuti tilankhule ndi Mlengi wathu. Yehova amafuna kumva maganizo athu. (Werengani Afilipi 4:6.) Ndipo Baibulo limatilangiza kuti ngati pali zinthu zina zimene zikutisowetsa mtendere, ‘tizitulira Yehova nkhawa zathu.’ (Sal. 55:22) Kodi inuyo mumaona kuti malangizo amenewa ndi othandiza? Abale ndi alongo mamiliyoni ambiri amavomereza kuti zimenezi zimathandiza. Choncho zikhoza kukuthandizaninso inuyo.

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira Yehova nthawi zonse?

11 Koma si bwino kumangopemphera tikafuna kuti Yehova atithandize pa vuto linalake. Paja Baibulo limatiuza kuti: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.” (Akol. 3:15) Nthawi zina tikhoza kumangoganizira mavuto athu n’kuiwaliratu madalitso ambirimbiri amene tili nawo. Choncho zingakhale bwino kuti tsiku lililonse tiziganizira zinthu zabwino, mwina zokwana zitatu, zimene tiyenera kuyamikira. Kenako tizipemphera kwa Yehova n’kumuyamikira pa zinthu zimenezo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mtsikana wina dzina lake Abigail amene anabatizidwa ali ndi zaka 12. Iye anati: “Ndimaona kuti Yehova ndi woyenera kumuyamikira kuposa aliyense m’chilengedwechi. Tiyenera kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti tiyamikire zinthu zambirimbiri zimene amatipatsa. Tsiku lina ndinamva funso limene limandikumbutsa kuti ndiziyamikira Yehova. Funso lake ndi lakuti: ‘Kodi mawa kutacha n’kupezeka kuti zinthu zimene ndatsala nazo ndi zokhazo zimene ndayamikira lero m’pemphero, ndidzatsala ndi chiyani?’” *

MUZIONA NOKHA UBWINO WA YEHOVA

12, 13. N’chifukwa chiyani muyenera kuganizira njira zimene Yehova wakusonyezerani ubwino wake?

12 Mfumu Davide anapulumutsidwa m’mavuto akuluakulu ndipo anaimba kuti: “Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino. Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathawira kwa iye.” (Sal. 34:8) Vesi limeneli likusonyeza kuti aliyense ayenera kuona payekha ubwino wa Yehova. Tikamawerenga Baibulo kapena mabuku athu komanso kupezeka pamisonkhano, timamva mmene Yehova anathandizira anthu ena kuti akhalebe okhulupirika. Koma pamene mukukula mwauzimu mumafunika kuona nokha Yehova akukuthandizani. Nanga inuyo Yehova wakuthandizani m’njira ziti?

13 Njira imodzi imene Yehova wasonyezera ubwino wake kwa Mkhristu aliyense ndi yomuthandiza kuti amuyandikire iyeyo komanso Mwana wake. Paja Yesu ananena kuti: “Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine.” (Yoh. 6:44) Kodi mumaona kuti mwakokedwa ndi Yehova? Mwina wachinyamata angaganize kuti, ‘Yehova anakoka makolo anga ndipo ine ndimangowatsatira.’ Koma ngati munadzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa, munasonyeza kuti inuyo muli pa ubwenzi wapadera ndi Yehovayo moti amakudziwani bwino. Pa nkhani imeneyi, Baibulo limati: “Ngati munthu akukonda Mulungu, ameneyo amadziwika kwa Mulungu.” (1 Akor. 8:3) Choncho muziyamikira kwambiri mwayi umene muli nawo wokhala m’gulu la Yehova.

14, 15. Kodi ntchito yolalikira ingalimbitse bwanji chikhulupiriro chanu?

14 Timaonanso ubwino wa Yehova akamatithandiza kulalikira, kaya tili mu utumiki kapena kusukulu. Anthu ena amavutika kulalikira kwa anzawo kusukulu, ndipo n’zomveka chifukwa sadziwa kuti anzawowo angachite chiyani. Komanso zimavuta kwambiri kulankhula ndi gulu kusiyana ndi kulankhula ndi munthu mmodzi. Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni?

15 Choyamba muyenera kuganizira zimene zimakutsimikizirani kuti zomwe mumakhulupirira ndi zolondola. Ngati nkhani zapawebusaiti yathu zakuti “Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?” zilipo m’chilankhulo chanu, muyenera kuzigwiritsa ntchito. Nkhani zimenezi zikhoza kukuthandizani kuganizira mfundo zimene mumakhulupirira, kutsimikizira kuti n’zolondola komanso kuti muzitha kuzifotokoza kwa anthu ena. Mukatsimikizira mfundozo n’kuzikonzekera bwino, mudzakhala ofunitsitsa kuuza ena za Yehova.​—Yer. 20:8, 9.

16. Kodi mungatani ngati mumavutika kuuza ena zimene mumakhulupirira?

16 Koma nthawi zina munthu akhoza kuvutika kulalikira ngakhale atakonzekera bwino. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina wazaka 18, amene anabatizidwa ali ndi zaka 13. Iye anati: “Ndimadziwa bwino zimene ndimakhulupirira koma nthawi zina zimandivuta kuti ndifotokozere anthu ena.” Ndiye kodi amatani ndi vuto lakeli? Iye anati: “Ndimangoyesetsa kuwalalikira ndikamacheza nawo. Anzanga amanena momasuka zinthu zimene amachita. Ndiye ndimaona kuti ndi bwino kuti nanenso ndizimasuka kunena zimene ndimachita. Choncho tikamakamba nkhani zina ndimatha kungonena kuti, ‘Tsiku lina ndikuphunzitsa munthu Baibulo ndinachita zakutizakuti.’ Kenako ndimapitiriza nkhaniyo. Ngakhale kuti za Baibulo ndimangozitchula modutsa, anthu ena amandifunsa zimene ndimachita pophunzitsa anthu Baibulolo. Njira imeneyi imandithandiza kwambiri ndipo ndi yosavuta. Ndikachita zimenezi ndimasangalala kwambiri.”

17. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muzifotokoza momasuka zimene mumakhulupirira?

17 Mukamalemekeza anthu ena komanso kuchita zinthu mowaganizira, zikhoza kuthandiza kuti nawonso azikulemekezani n’kumvetsera uthenga wanu. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina wazaka 17 dzina lake Olivia, yemwe anabatizidwa ali wamng’ono. Iye anati: “M’mbuyo monsemu, ndinkaganiza kuti ndikamatchula Baibulo pocheza ndi anthu, sizingawasangalatse.” Koma mlongoyu anasintha maganizo ake. M’malo moganizira zimene ankaopazi, iye anayamba kuganiza kuti: “Achinyamata ambiri sadziwa chilichonse chokhudza Mboni za Yehova. Koma a Mboni amene tili pafupi nawo ndi ifeyo. Choncho khalidwe lathu ndi limene lingachititse kuti azitimvetsera kapena ayi. Ndiye kodi iwo angatani akaona kuti timachita manyazi kapena mantha pofotokoza zimene timakhulupirira? Akhoza kuganiza kuti sitinyadira kukhala a Mboni za Yehova. Mwinanso sangamvetsere zimene tikuwauza chifukwa choona kuti timakayikakayika. Koma ngati timamasuka n’kumafotokoza zimene timakhulupirira pocheza nawo, akhoza kutilemekeza.”

PITIRIZANI KUKONZA CHIPULUMUTSO CHANU

18. Kodi muyenera kuchita zinthu ziti kuti mukonze chipulumutso chanu?

18 Monga taonera, kukonza chipulumutso chanu ndi udindo waukulu kwambiri. Taona kuti muyenera kuwerenga Mawu a Mulungu, kuwasinkhasinkha, kupemphera ndiponso kuganizira zinthu zabwino zimene Yehova wakuchitirani. Mukamachita zinthu zimenezi mwakhama, mudzayamba kukhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova ndi mnzanu wapamtima. Zimenezi zidzakuthandizani kuuza anthu molimba mtima zimene mumakhulupirira.​—Werengani Salimo 73:28.

19. Kodi chingachitike n’chiyani mukamayesetsa kukonza chipulumutso chanu?

19 Yesu ananena kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo ndipo anditsatire mosalekeza.” (Mat. 16:24) Apa zikuonekeratu kuti munthu amene akufuna kukhala Mkhristu ayenera kudzipereka kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa. Munthu akachita zimenezi adzapeza madalitso ambiri panopa komanso moyo wosatha m’dziko latsopano. Choncho pitirizani kuchita zonse zimene mungathe kuti mukonze chipulumutso chanu.

^ ndime 11 Kuti mumve zambiri, pitani pawebusaiti ya jw.org/ny pa mutu wakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa” ndipo werengani nkhani yakuti “Kodi Kupemphera N’kothandiza?” komanso “Zoti Achinyamata Achite” zomwe zikugwirizana ndi nkhaniyi.