Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi Yesu ankanena za machimo ati pamene ankapereka malangizo a pa Mateyu 18:15-17?

Ankanena za nkhani zimene zingathe kuthetsedwa ndi anthu amene alakwiranawo. Koma nkhani yake iyenera kukhala yaikulu yoti ngati wolakwayo sanavomereze kulakwa kwake angathe kuchotsedwa. Mwachitsanzo, ingakhale yokhudza kuipitsira mbiri munthu wina kapena kuchita chinyengo.—w16.05, tsa. 7.

Kodi mungatani kuti muzipindula kwambiri ndi kuwerenga Baibulo?

Muziona kuti nkhani iliyonse ingakuthandizeni. Muzidzifunsa mafunso monga akuti, ‘Kodi mfundo zimenezi ndingazigwiritse ntchito bwanji pothandiza ena?’ Komanso muzifufuza mfundo zina pogwiritsa ntchito zinthu zofufuzira zomwe tili nazo.—w16.05, tsa. 24-26.

Kodi n’kulakwa kuti Mkhristu amene amakhulupirira zoti akufa adzauka azimva chisoni akaferedwa?

Chikhulupiriro chakuti akufa adzauka sichichititsa kuti Mkhristu asakhale ndi chisoni akaferedwa. Abulahamu analira mkazi wake Sara atamwalira. (Gen. 23:2) Komabe pakapita nthawi chisoni chimayamba kuchepa.—wp16.3, tsa. 4.

Kodi munthu wokhala ndi kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki ndi zolembera komanso amuna 6 okhala ndi zida, omwe Ezekieli anaona akuimira ndani?

Anthuwa akuimira gulu lankhondo lakumwamba limene linagwira nawo ntchito yowononga Yerusalemu komanso limene lidzagwire nawo ntchito yowononga dziko la Satanali pa Aramagedo. Masiku ano, munthu wokhala ndi kachikwama ka mlembi akuimira Yesu Khristu, amene adzalembe chizindikiro anthu oyenera kupulumuka.—w16.06, tsa. 16-17.

Kodi Baibulo linapulumuka mavuto ati?

(1) Baibulo likanatha kuwola chifukwa linkalembedwa pa zinthu monga gumbwa komanso zikopa. (2) Andale komanso atsogoleri azipembedzo sankalifuna. (3) Anthu ena ankafuna kusintha uthenga wake.—wp16.4, tsa. 4-7.

Kodi mungatani kuti muzikhala moyo wosalira zambiri?

Pezani zimene mumafunikadi pa moyo wanu komanso ganizirani zomwe mukuona kuti n’zosafunika kugula. Lembani bajeti. Chotsani zinthu zimene simuzigwiritsa ntchito ndipo lipiriani ngongole zanu zonse. Chepetsani nthawi imene mumagwira ntchito komanso ganizirani utumiki wina umene mungachite.—w16.07, tsa. 10.

Kodi Baibulo limati chinthu chamtengo wapatali kuposa golide ndi chiyani?

Lemba la Yobu 28:12, 15 limati nzeru zochokera kwa Mulungu ndi zamtengo wapatali kuposa golide kapena siliva. Mukamafufuza nzeru zimenezi muziyesetsa kukhalabe odzichepetsa komanso muzilimbitsa chikhulupiriro chanu.—w16.08, tsa. 18-19.

Kodi masiku ano n’koyenera kuti abale azisunga ndevu?

M’madera ena si vuto kukhala ndi ndevu zoduliridwa bwino ndipo sizingalepheretse anthu kumvetsera uthenga wa Ufumu. Komabe abale ena amasankha kuti asamasunge ndevu. (1 Akor. 8:9) M’mayiko ena mulibe chikhalidwe chimenechi ndipo anthu amaona kuti n’zosayenera kuti atumiki a Mulungu azisunga ndevu.—w16.09 tsa. 21.

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kuti nkhani ya m’Baibulo ya Davide ndi Goliyati inachitikadi?

Baibulo limanena kuti Goliyati anali wamtali masentimita 15 okha kuposa munthu wamtali kwambiri padziko lonse. Davide anakhalakodi ndipo umboni wa zimenezi tingaupeze m’zolemba zakale komanso pa zimene Yesu ananena. Palinso umboni wosonyeza kuti malo otchulidwa m’nkhani ya Davide alipodi.—wp16.5, tsa. 13.

Kodi kudziwa zinthu, kumvetsa zinthu komanso nzeru zimasiyana bwanji?

Munthu wodziwa zinthu amakhala kuti wangotolera mfundo. Munthu womvetsa zinthu amazindikira kugwirizana kwa mfundozo. Koma munthu wanzeru ndi amene amadziwa zinthu, kuzimvetsa komanso kuzigwiritsa ntchito m’njira yopindulitsa.—w16.10, tsa. 18.