NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) December 2016

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira January 30 mpaka February 26, 2017.

MBIRI YA MOYO WANGA

Ndayesetsa Kukhala “Zinthu Zonse kwa Anthu Osiyanasiyana”

Utumiki wosiyanasiyana umene Denton Hopkinson anachita unamuthandiza kuona kuti Yehova amakonda anthu a mitundu yonse.

Tinamasulidwa ku Uchimo Chifukwa cha Kukoma Mtima Kwakukulu

Mungapeze madalitso ambiri mukamaganizira zimene Yehova anachita kuti atipulumutse ku uchimo.

“Kuika Maganizo pa Zinthu za Mzimu Kumabweretsa Moyo ndi Mtendere”

Chaputala 8 cha Aroma chili ndi malangizo amene angakuthandizeni kuti mudzapeze madalitso amene Yehova wakonzera anthu.

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa

Muzimutulira Yehova Nkhawa Zanu Zonse

Nthawi zina, atumiki a Mulungu amakhala ndi nkhawa. Njira 4 zothandiza kuti tikhale ndi “mtendere wochokera kwa Mulungu.”

Yehova Amapereka Mphoto kwa Anthu Omufunafuna ndi Mtima Wonse

Kodi chiyembekezo chakuti Yehova adzatipatsa mphoto chimatithandiza bwanji? Kodi anapereka bwanji mphoto kwa atumiki ake akale, nanga bwanji masiku ano?

Munthu Wofatsa Amasonyeza Kuti Ndi Wanzeru

Zimakhala zovuta kuugwira mtima wina akatichitira zinthu zopanda chilungamo. Koma Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti azikhala ofatsa. Kodi tingatani kuti tikhale ndi khalidwe limeneli?

Mlozera Nkhani wa Magazini a Nsanja ya Olonda a 2016

Nkhani za mu Nsanja ya Olonda yogawira ndi yophunzira.