Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani nkhani zokhudza moyo wa Yesu ali mwana zimene Mateyu ndi Luka analemba zimasiyana?

Nkhani zimene Mateyu ndi Luka analemba zokhudza kubadwa kwa Yesu komanso moyo wake ali mwana zimasiyana pang’ono chifukwa iwo ankafotokoza kwambiri za anthu osiyana.

Nkhani ya Mateyu imafotokoza kwambiri za Yosefe. Mwachitsanzo, imafotokoza zimene Yosefe anachita atadziwa kuti Mariya ali ndi mimba, zimene mngelo anamuuza m’maloto zokhudza nkhaniyi komanso zimene Yosefe anachita atamva mawu a mngeloyo. (Mat. 1:19-25) Mateyu anafotokoza kuti mngelo anauza Yosefe m’maloto kuti athawire ku Iguputo ndipo Yosefe ndi banja lake anathawa. Anafotokozanso kuti mngelo anamuuza kuti abwerere ku Isiraeli ndipo Yosefeyo atabwerera anasankha kuti akakhale ku Nazareti. (Mat. 2:13, 14, 19-23) M’machaputala oyambirira a buku la Mateyu, dzina la Yosefe limapezekamo maulendo 9 pomwe dzina la Mariya limapezeka maulendo 4 basi.

Koma Luka analemba kwambiri zokhudza Mariya. Iye analemba zimene zinachitika pamene mngelo Gabirieli analankhula naye, pamene anakaona m’bale wake Elizabeti komanso zimene Mariya ananena potamanda Yehova. (Luka 1:26-56) Luka anatchulanso mawu amene Simiyoni anauza Mariya okhudza mavuto amene Yesu anadzakumana nawo. Pofotokoza za ulendo wopita kukachisi pamene Yesu anali ndi zaka 12, Luka analemba zimene Mariya ananena osati Yosefe. Luka anafotokozanso mmene zonsezi zinakhudzira Mariya. (Luka 2:19, 34, 35, 48, 51) M’machaputala awiri oyamba a buku la Luka, dzina la Mariya limatchulidwa maulendo 15 pomwe dzina la Yosefe limatchulidwa katatu kokha. Choncho Mateyu amafotokoza kwambiri maganizo ndiponso zochita za Yosefe pamene Luka amafotokoza kwambiri za Mariya.

Mndandanda wa makolo a Yesu umene Mateyu ndi Luka analemba umasiyananso. Mateyu analemba mndandanda wa makolo a Yosefe ndipo umasonyeza kuti Yesu, yemwe anali mwana wopeza wa Yosefe, anali woyenera kulowa ufumu wa Davide mogwirizana ndi malamulo. Zili choncho chifukwa Yosefe anali mwana wa Mfumu Davide kudzera mwa mwana wake Solomo. (Mat. 1:6, 16) Koma Luka analemba mndandanda wa makolo a Mariya ndipo umasonyeza kuti Yesu anali woyenera kulowa ufumu wa Davide chifukwa cha munthu amene anamubereka. (Aroma 1:3) Zili choncho chifukwa Mariya anabadwa m’banja la Davide kudzera mwa mwana wake Natani. (Luka 3:31) Koma n’chifukwa chiyani pamndandandawu, Luka sanalembe kuti Mariya ndi mwana wa Heli? Sanachite zimenezi chifukwa polemba mndandanda wa makolo, anthu ankagwiritsa ntchito dzina la mwamuna. Choncho pamene Luka analemba kuti Yosefe ndi mwana wa Heli, ankatanthauza kuti Yosefe anali mkamwini wa Heli osati mwana wake weniweni.​—Luka 3:23.

Mndandanda umene Mateyu komanso Luka analemba umasonyeza kuti Yesu analidi Mesiya. Mfundo yoti Yesu anabadwa m’banja la Davide inali yodziwika kwambiri moti ngakhale Afarisi ndi Asaduki sakanaitsutsa. Masiku ano, mndandanda wa Mateyu komanso wa Luka umatithandizanso kukhulupirira kuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa.