Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikondi Ndi Khalidwe Lamtengo Wapatali Kwambiri

Chikondi Ndi Khalidwe Lamtengo Wapatali Kwambiri

MTUMWI Paulo analemba makhalidwe 9 amene mzimu woyera umatithandiza kukhala nawo. (Agal. 5:22, 23) Mawu achigiriki amene anawagwiritsa ntchito pofotokoza makhalidwewa ndi oti “chipatso cha mzimu” ndipo iye anasonyeza kuti makhalidwewa amapanga chipatso chimodzi. * Makhalidwe amenewa ndi amene amapanganso “umunthu watsopano.” (Akol. 3:10) Mofanana ndi mtengo umene umabala bwino zipatso ngati ukusamaliridwa, munthu amatha kukhala ndi makhalidwewa ngati akulola kuti mzimu woyera uzimuthandiza.​—Sal. 1:1-3.

Khalidwe loyamba limene Paulo anatchula ndi chikondi ndipo ndi khalidwe lamtengo wapatali kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Paulo ananena kuti ‘ngati alibe chikondi sali kanthu.’ (1 Akor. 13:2) Koma kodi tingadziwe bwanji ngati munthu ali ndi chikondi? Nanga tingatani kuti tikhale nacho n’kumachisonyeza tsiku lililonse?

KODI TINGADZIWE BWANJI NGATI MUNTHU ALI NDI CHIKONDI?

Kufotokoza tanthauzo la mawu oti chikondi ndi kovuta kwambiri koma Baibulo limafotokoza mmene munthu angachisonyezere. Mwachitsanzo limanena kuti chikondi “n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima.” Limanenanso kuti ‘chimakondwera ndi choonadi, chimakwirira zinthu zonse, chimakhulupirira zinthu zonse, chimayembekezera zinthu zonse ndiponso chimapirira zinthu zonse.’ Munthu akamakonda munthu wina amamuganizira kwambiri komanso amamuona kuti ndi mnzake wapamtima. Koma munthu amene sakonda anthu ena amakhala wansanje, wodzikuza, wakhalidwe loipa, wodzikonda, wokwiyakwiya komanso wosakhululuka. Mosiyana ndi makhalidwe oipa amene tatchulawa, munthu wachikondi sasamala “zofuna zake zokha.”​—1 Akor. 13:4-8.

YEHOVA NDI YESU NDI ZITSANZO ZABWINO POSONYEZA CHIKONDI

Baibulo limanena kuti “Mulungu ndiye chikondi,” kutanthauza kuti iye ndi chimake cha chikondi. (1 Yoh. 4:8) Chilichonse chimene amachita chimasonyeza kuti ndi wachikondi. Njira yaikulu kwambiri imene anasonyezera chikondi kwa anthu ndi yotumiza Yesu kuti adzatifere. Mtumwi Yohane ananena kuti: “Mulungu anatisonyeza ife chikondi chake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzera mwa iye. Chikondi chimenechi chikutanthauza kuti ife sitinakonde Mulungu, koma iye ndi amene anatikonda ndi kutumiza Mwana wake monga nsembe yophimba machimo athu.” (1 Yoh. 4:9, 10) Chikondi cha Mulungu chimathandiza kuti anthufe tikhululukidwe, tikhale ndi chiyembekezo komanso tidzapeze moyo.

Yesu anasonyeza kuti amakonda anthu pamene analolera kuchita zimene Mulungu ankafuna. Pa nkhani imeneyi, Paulo analemba kuti: “[Yesu] ananenanso kuti: ‘Taonani! Ine ndabwera kudzachita chifuniro chanu.’ . . . Mwa ‘chifuniro’ chimenecho, tayeretsedwa kudzera m’thupi la Yesu Khristu loperekedwa nsembe kamodzi kokha.” (Aheb. 10:9, 10) Palibe munthu amene angasonyeze chikondi chachikulu kuposa chimenechi.  M’pake kuti Yesu ananena kuti: “Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.” (Yoh. 15:13) Kodi n’zotheka kuti anthu ochimwafe titsanzire chikondi chimene Yehova ndi Yesu anatisonyeza? Inde. Tiyeni tikambirane mmene tingachitire zimenezi.

“YENDANIBE M’CHIKONDI”

Paulo ananena kuti: “Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa, ndipo yendanibe m’chikondi, monganso Khristu anakukondani n’kudzipereka yekha chifukwa cha inu.” (Aef. 5:1, 2) Mawu oti “yendanibe m’chikondi” akutanthauza kuti tiyenera kusonyeza chikondi pa chilichonse chimene timachita. Timasonyeza chikondi ndi zochita zathu osati zonena zathu zokha. Paja Yohane analemba kuti: “Ana anga okondedwa, tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tizisonyezana chikondi chenicheni m’zochita zathu.” (1 Yoh. 3:18) Mwachitsanzo, ngati timakonda Mulungu ndi anzathu ndiye kuti tizilalikira ‘uthenga wabwino wa ufumu.’ (Mat. 24:14; Luka 10:27) Timayendanso m’chikondi tikamayesetsa kukhala oleza mtima, okoma mtima komanso okhululuka. M’pake kuti Baibulo limatilangiza kuti tipitirize ‘kukhululukirana ngati mmene Yehova anatikhululukira ndi mtima wonse.’​—Akol. 3:13.

Koma pali kusiyana pakati pa chikondi chenicheni ndi kutengeka maganizo. Mwachitsanzo, makolo amene angotengeka maganizo akhoza kuchita chilichonse chimene mwana wafuna n’cholinga choti mwanayo atonthole. Koma makolo amene amakondadi mwana wawo amadziwa malire ndipo sangasasatitse mwana. Umu ndi mmenenso Yehova alili. Ngakhale kuti iye ndi chikondi, ‘amalanga anthu amene amawakonda.’ (Aheb. 12:6) Ngati ifenso tili ndi chikondi chenicheni, sitingalekerere munthu amene akufunikira kulandira chilango. (Miy. 3:11, 12) Koma popereka chilangocho tiyenera kukumbukira kuti nafenso ndi ochimwa ndipo n’zosavuta kuti tichite zinthu mopanda chikondi. Choncho pa nkhani yosonyeza chikondi, aliyense ayenera kuona pamene akulephera n’kukonza. Koma kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyeni tikambirane njira zitatu.

ZIMENE ZINGATITHANDIZE KUKHALA ACHIKONDI

Choyamba, tiyenera kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu woyera kuti utithandize kukhala achikondi. Paja Yesu ananena kuti Yehova amapereka “mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Tikamapempha mzimu woyera n’kupitiriza ‘kuyenda mwa mzimuwo,’ tidzatha kuchita zinthu mwachikondi kwambiri. (Agal. 5:16) Mwachitsanzo, ngati ndinu mkulu, mukhoza kupempha mzimu woyera kuti muzipereka malangizo a m’Malemba mwachikondi. Ngati ndinu makolo, mungapemphe mzimu woyera kuti ukuthandizeni kulangiza ana anu mwachikondi osati mwaukali.

Chachiwiri, tiziganizira chitsanzo cha Yesu chosonyeza chikondi ngakhale pamene anthu ankamuvutitsa. (1 Pet. 2:21, 23) Kuganizira chitsanzochi kungatithandize kwambiri ngati anthu ena atikhumudwitsa kapena kutichitira zinthu zopanda chilungamo. Zimenezi zikachitika, ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi akanakhala Yesu akanatani pamenepa?’ Mlongo wina dzina lake Leigh anaona kuti kuganizira funsoli kunamuthandiza kuti achite zinthu mwanzeru. Iye anati: “Nthawi ina, munthu wina amene tinkagwira naye ntchito anatumiza imelo kwa anzathu ena kuntchito yonena zinthu zoipa zokhudza ineyo komanso ntchito imene ndinkagwira. Ndinakhumudwa kwambiri. Koma kenako ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi ndingatsanzire bwanji Yesu pochita zinthu ndi munthu ameneyu?’ Nditaganizira zimene Yesu akanachita ndinasankha zongoisiya nkhaniyo. Kenako ndinamva kuti munthuyo ankadwala ndipo ankada nkhawa kwambiri. Choncho ndinaona kuti mwina analemba zinthuzo asanaziganizire bwinobwino. Kuganizira chitsanzo cha Yesu chosonyeza chikondi ngakhale pamene akuvutitsidwa kunandithandiza kuti ndizisonyezanso chikondi kwa munthuyo.” Kunena zoona, tikamatsanzira Yesu tidzatha kusonyeza chikondi nthawi zonse.

Chachitatu, tiziyesetsa kukhala ndi chikondi chololera kuvutikira ena chomwe Akhristu enieni ayenera kukhala nacho. (Yoh. 13:34, 35) Pa nkhaniyi, Malemba amatilimbikitsa kuti tikhale ndi maganizo ofanana ndi a Yesu. Pochoka kumwamba, iye analolera ‘kusiya zonse zimene anali  nazo’ chifukwa cha ife ndipo anapitiriza kuchita zimenezi “mpaka imfa.” (Afil. 2:5-8) Tikamatsanzira chikondi cha Yesu, tidzayamba kuganiza ngati iyeyo ndipo tidzakhala ndi mtima wofuna kuika zofuna za ena pamalo oyamba osati zathu. Koma kodi kukhala ndi chikondi kuli ndi ubwino wina wotani?

UBWINO WOSONYEZA CHIKONDI

Tikamasonyeza chikondi timapeza madalitso ambiri. Tiyeni tikambirane madalitso awiri omwe tingapeze.

Kodi timapeza madalitso otani tikamasonyeza chikondi?

  • UBALE WAPADZIKO LONSE: Akhristufe timakondana kwambiri moti timadziwa kuti ngati titapita kumpingo uliwonse padzikoli, abale ndi alongo adzatilandira bwino. Kukondedwa ndi abale athu apadziko lonse ndi mwayi waukulu kwambiri. (1 Pet. 5:9) Chikondi choterechi chimapezeka pakati pa anthu a Mulungu okha basi.

  • MTENDERE: Timakhala mwamtendere chifukwa chakuti ‘timalolerana m’chikondi.’ (Aef. 4:2, 3) Timaona mtendere umenewu kumisonkhano yathu yampingo ndiponso ikuluikulu. Koma mukhoza kuvomereza kuti mtendere woterewu supezekapezeka m’dziko loipali. (Sal. 119:165; Yes. 54:13) Tikamayesetsa kukhala mwamtendere ndi anthu ena timasonyeza kuti timawakonda kwambiri ndipo zimenezi zimasangalatsa Atate wathu wakumwamba.​—Sal. 133:1-3; Mat. 5:9.

“CHIKONDI CHIMAMANGIRIRA”

Paulo analemba kuti: “Chikondi chimamangirira.” (1 Akor. 8:1) Koma kodi chimamangirira bwanji? Paulo anayankha funsoli m’chaputala 13 cha kalata yake yoyamba yopita kwa Akorinto. Chaputala chimenechi chimadziwikanso kuti “Salimo la Chikondi.” Mfundo imodzi imene anatchula m’chaputalachi ndi yakuti munthu akakhala ndi chikondi samangoganizira zofuna zake zokha. (1 Akor. 10:24; 13:5) Munthu wotereyu amaganiziranso anthu ena, amawalemekeza ndipo amakhala woleza mtima komanso wokoma mtima. N’chifukwa chake chikondi chimathandiza kuti mabanja aziyenda bwino komanso kuti mipingo izigwirizana.​—Akol. 3:14.

Tonsefe timakonda Mulungu ndipo chikondi chimenechi ndi chofunika kwambiri komanso chimamangirira kuposa chikondi chilichonse. Chimathandiza kuti anthu osiyana zikhalidwe, mitundu komanso zilankhulo azitumikira Yehova mogwirizana ndiponso mosangalala. (Zef. 3:9) Tiyeni tonsefe tiziyesetsa kusonyeza chikondi, chomwe ndi khalidwe lamtengo wapatali limene mzimu woyera wa Mulungu umatulutsa.

^ ndime 2 Nkhaniyi ndi yoyamba ndipo nkhani zofotokoza makhalidwe ena zituluka m’magazini am’tsogolo.