NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) August 2017

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa September 25 mpaka October 22, 2017.

Kodi Mukhoza Kuyembekezera Moleza Mtima?

Atumiki okhulupirika a Yehova akale anafunsa kuti ayenera kupirira mavuto mpaka liti. Koma Mulungu sanawadzudzule chifukwa chofunsa zimenezi.

‘Mtendere wa Mulungu Umaposa Kuganiza Mozama Kulikonse’

Kodi munadzifunsapo chifukwa chimene Mulungu analolera kuti mukumane ndi mavuto enaake? Ngati ndi choncho, n’chiyani chingakuthandizeni kupirira mavuto uku mukukhulupirirabe Mulungu ndi mtima wonse?

MBIRI YA MOYO WANGA

Tikapirira Mavuto Tidzadalitsidwa

N’chifukwa chiyani anthu amene anatumizidwa ku Siberia ankafunsa za ng’ombe pamene ankafuna nkhosa? Mungapeze yankho la funsoli mu mbiri ya moyo wa Pavel ndi Maria Sivulsky.

Vulani Umunthu Wakale Ndipo Musauvalenso

Tiyenera kuvula umunthu wakale ndipo tisauvalenso. Kodi n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi ngakhale kuti kale tinkachita zinthu zoipa kwambiri?

Valani Umunthu Watsopano Ndipo Musauvulenso

Yehova angakuthandizeni kuti mukhale ndi makhalidwe amene amamusangalatsa. Werengani kuti mudziwe njira zina zimene mungasonyezere chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa komanso kufatsa.

Chikondi Ndi Khalidwe Lamtengo Wapatali Kwambiri

Malemba amasonyeza kuti chikondi ndi khalidwe lina limene mzimu woyera umatulutsa. Koma kodi munthu wachikondi amatani? Kodi mungatani kuti mukhale achikondi? Nanga mungatani kuti muzisonyeza khalidweli tsiku lililonse?

KALE LATHU

“Kodi Tichitanso Liti Msonkhano Wina?”

N’chifukwa chiyani msonkhano wa mu 1932 wa ku Mexico City umene anthu 150 okha anapezeka ndi wosaiwalika?

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani nkhani imene Mateyu analemba yokhudza moyo wa Yesu ali mwana komanso makolo ake ndi yosiyana ndi ya Luka?