Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kudzipereka Kwathu Kumachititsa Kuti Yehova Atamandidwe

Kudzipereka Kwathu Kumachititsa Kuti Yehova Atamandidwe

Chifukwa cha kudzipereka mwaufulu kwa anthu, tamandani Yehova.”​OWER. 5:2.

NYIMBO: 150, 10

1, 2. (a) Kodi Elifazi ndi Bilidadi anati Yehova amaona bwanji zimene timachita pomutumikira? (b) Kodi Yehova anatani posonyeza kuti zimene anthuwa ananena zinali zabodza?

“KODI mwamuna wamphamvu angakhale waphindu kwa Mulungu? Kodi aliyense wozindikira angakhale waphindu kwa iye? Kodi Wamphamvuyonse amasangalala kuti ndiwe wolungama?” (Yobu 22:1-3) Elifazi wa ku Temani ndi amene anafunsa Yobu mafunso amenewa. Kodi inuyo mukuganiza kuti yankho la mafunsowa ndi chiyani? Elifazi ankaganiza kuti yankho la mafunso amenewa ndi lakuti ayi. Komanso Bilidadi wa ku Shuwa ananena kuti n’zosatheka kuti Yehova aone kuti munthu ndi wolungama.—Werengani Yobu 25:4.

2 Elifazi ndi Bilidadi ankafuna kuti Yobu aziona ngati Yehova sankayamikira zabwino zimene ankachita pomutumikira. Iwo ankafuna kuti Yobu aziganiza zoti Yehova ankaona kuti iye ndi wonyozeka ngati kadziwotche, mphutsi kapena nyongolotsi. (Yobu 4:19; 25:6) Kungomva koyamba mawu a Elifazi ndi Bilidadiwa, munthu angaganize kuti iwo ananena zimenezi chifukwa chodzichepetsa. (Yobu 22:29) N’zoona kuti Yehova ndi wapamwamba kwambiri tikamuyerekezera  ndi anthufe. Tikayang’ana pansi tili pamwamba pa phiri kapena tili mundege, zinthu zimene zili padzikoli zimaoneka zing’onozing’ono kwambiri. Koma kodi ndi mmenenso Yehova amaonera zimene timachita pomutumikira padzikoli? Ayi. Tikutero chifukwa anadzudzula Elifazi, Bilidadi ndi Zofari chifukwa chonama kuti iye sankasangalala ndi Yobu ndipo anatchula Yobuyo kuti “mtumiki wanga.” (Yobu 42:7, 8) Izi zikusonyeza kuti munthu ndi “waphindu kwa Mulungu.”

“KODI MUMAM’PATSA CHIYANI?”

3. Kodi Elihu ananena chiyani zokhudza Yehova, ndipo ankatanthauza chiyani?

3 Elihu ankamvetsera zimene Yobu ankakambirana ndi amuna atatu aja. Kenako iye anafunsa Yobu kuti: “Ngati ndinudi wosalakwa, kodi mumam’patsa chiyani [Mulungu]? Kodi amalandira chiyani kuchokera m’manja mwanu?” (Yobu 35:7) Kodi pamenepa Elihu ankatanthauza kuti zimene timachita potumikira Mulungu n’zopanda ntchito? Ayi. Tikutero chifukwa Yehova sanamudzudzule ngati mmene anachitira ndi amuna atatu aja. Elihu ankatanthauza kuti Yehova ali ndi chilichonse ndipo samadalira zimene timachita pomulambira. Ifeyo sitingamuthandize kuti akhale wolemera kapena wamphamvu kuposa mmene alili. Iye ndi amene amatipatsa luso, mphamvu komanso zinthu zilizonse zabwino zimene tili nazo ndipo amaona mmene timazigwiritsira ntchito.

4. Kodi Yehova amaona bwanji zabwino zimene timachitira ena?

4 Tikachitira zabwino Akhristu anzathu, Yehova amaona kuti tachitira iyeyo. Lemba la Miyambo 19:17 limati: “Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.” Lembali likutanthauza kuti Yehova amaona zabwino zilizonse zimene timachitira anthu ooneka ngati onyozeka. Ngakhale kuti iye ndi Mlengi wa chilengedwe chonse amadziwa zabwino zimene anthufe timachitira ena. Amaona kuti tamukongoza iyeyo ndipo adzatibwezera potidalitsa. Zimene Mwana wake ananena zimasonyeza kuti mfundo imeneyi ndi yoona.​—Werengani Luka 14:13, 14.

5. Kodi tikambirana mafunso ati?

5 Yehova anapempha mneneri Yesaya kuti aziuza anthu uthenga wake. Izi zikusonyeza kuti iye amasangalala kugwiritsa ntchito anthu okhulupirika pokwaniritsa cholinga chake. (Yes. 6:8-10) Yesaya anavomera ndi mtima wonse utumiki umene Yehova anamupatsawu. Masiku anonso pali atumiki ambiri a Yehova amene mofanana ndi Yesaya amati, “Ine ndilipo! Nditumizeni.” Iwo amalolera kuchita utumiki wovuta. Komabe mwina mungafunse kuti: ‘Ndimaona kuti ndi mwayi kuti Yehova analola kuti ndizimutumikira, koma kodi iye amaonadi zimene ndimachita? Kodi iye sangathe kukwaniritsa cholinga chake popanda ineyo?’ Kuti tipeze mayankho a mafunsowa, tiyeni tione zimene zinachitika pa nthawi ya Debora ndi Baraki.

MULUNGU ANAWATHANDIZA KUKHALA OLIMBA MTIMA

6. N’chiyani chikusonyeza kuti asilikali a Yabini akanagonjetsa Aisiraeli mosavuta?

6 Kwa zaka 20, Aisiraeli ‘anaponderezedwa kwambiri’ ndi mfumu ya Akanani dzina lake Yabini. Asilikali a Yabini anali ankhanza kwambiri ndipo Aisiraeli ankachita mantha moti ankaopa kutuluka m’nyumba. Asilikaliwo anali ndi magaleta 900 okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa m’mawilo. Koma Aisiraeli analibe zida zankhondo zokwanira.​—Ower. 4:1-3, 13; 5:6-8. *

7, 8. (a) Kodi Yehova anapereka malangizo otani kwa Baraki? (b) Kodi Aisiraeli anagonjetsa bwanji asilikali a Yabini? (Onani chithunzi choyambirira.)

7 Koma Yehova anatuma Debora kukauza  Baraki kuti: “Tenga amuna 10,000 pakati pa ana a Nafitali ndi ana a Zebuloni ndipo mukasonkhane paphiri la Tabori. Ine ndidzakokera kwa iwe m’chigwa cha Kisoni, Sisera mkulu wa gulu lankhondo la Yabini, pamodzi ndi magaleta ake ankhondo ndi gulu lake lonse. Pamenepo ndidzam’pereka m’manja mwako.”​—Ower. 4:4-7.

8 Uthenga woti pakufunika amuna 10,000 odzipereka unafika paliponse ndipo anthu amene anadziperekawo anasonkhana paphiri la Tabori. Nthawi yomweyo Baraki anatenga amunawo n’kupita kukakumana ndi adani awo ku Taanaki. (Werengani Oweruza 4:14-16.) Pa nkhondoyo Yehova anathandiza Aisiraeli. Mwadzidzidzi, kunagwa chimvula champhepo ndipo dera lonselo linali matope okhaokha. Apa tsopano Aisiraeli zinayamba kuwayendera moti Baraki anathamangitsa asilikali a Sisera mpaka mtunda wa makilomita 24 kukafika ku Haroseti. Kenako galeta la Sisera linatitimira m’matope moti iye anangotsikamo n’kuyamba kuthawa wapansi mpaka kufika ku Zaananimu pafupi ndi Kadesi. Iye anakapempha malo muhema wa mkazi wina dzina lake Yaeli ndipo anamulandira bwino. Chifukwa chotopa, anangofikira kugona. Atagona, Yaeli analimba mtima n’kumupha. (Ower. 4:17-21) Apatu Yehova anathandiza Aisiraeli kuti agonjetse adani awo. *

ENA ANASONYEZA MTIMA WODZIPEREKA POMWE ENA SANASONYEZE

9. Kodi lemba la Oweruza 5:20, 21 limatiuza mfundo ziti zokhudza nkhondo yolimbana ndi Sisera?

9 Tingamvetse bwino mfundo zina zimene zili mu Oweruza chaputala 4 tikawerenga chaputala 5. Mwachitsanzo, lemba la Oweruza 5:20, 21 limati: “Nyenyezi zinamenya nkhondo zili kumwamba, zinamenyana ndi Sisera zili m’njira zawo. Mtsinje wa Kisoni unawakokolola.” Kodi lembali likutanthauza kuti angelo anathandiza pa nkhondo ija, kapena likunena kuti nyenyezi zinkathothoka ndipo izi zinathandiza kuti Aisiraeli apambane? Baibulo silifotokoza. Koma zingakhale zomveka kunena kuti Yehova anapulumutsa anthu ake pobweretsa chimvula chomwe chinachititsa kuti magaleta 900 aja azilephera kuyenda. Lemba la Oweruza 4:14, 15 limanena katatu konse kuti Yehova anathandiza anthu ake kuti apambane. Choncho palibe aliyense wa Aisiraeli 10,000 amene anadzipereka aja amene akanaganiza kuti gulu lawo lapambana chifukwa cha iyeyo.

10, 11. Kodi “Merozi” anali chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani anatembereredwa?

10 Aisiraeli atapambana, Debora ndi Baraki anaimba nyimbo yotamanda Yehova. N’zochititsa chidwi kuti munyimboyi ankanena kuti: “Mngelo wa Yehova anati: ‘Tembererani Merozi, tembererani anthu ake mosaleka, chifukwa sanathandize Yehova, sanabwere ndi anthu amphamvu kudzathandiza Yehova.’”​—Ower. 5:23.

11 Kodi Merozi anali chiyani? Sitikudziwa chifukwa zikuoneka kuti tembereroli linayamba kugwira ntchito nthawi yomweyo moti zinali zovuta kudziwa chilichonse chokhudza mawuwa. N’kutheka kuti Merozi unali mzinda ndipo anthu amumzindawu anamva uthenga wochokera kwa Baraki wakuti pakufunika anthu oti apite kunkhondo, koma sanadzipereke. Apo ayi, mwina Merozi unali mzinda umene Sisera anadutsa pamene ankathawa Baraki. Ngati ndi choncho, ndiye kuti anthu amumzindawu anaona Sisera akuthawa. Anthuwa akanamugwira, akanathandiza kukwaniritsa cholinga cha Yehova ndipo akanadalitsidwa. Koma n’zomvetsa chisoni kuti anangokhala osachita chilichonse. Zikuoneka kuti anthu a mumzinda wa Merozi anali osiyana ndi Yaeli amene anachita zinthu molimba mtima.​—Ower. 5:24-27.

12. Kodi lemba la Oweruza 5:9, 10 likusonyeza kuti anthu amene anadzipereka aja anasiyana bwanji ndi amene sanadzipereke, nanga tikuphunzirapo chiyani?

 12 Lemba la Oweruza 5:9, 10 limasonyeza kuti anthu amene anadzipereka kupita ndi Baraki aja anali osiyana ndi anthu amene sanadzipereke. Mwachitsanzo, Debora ndi Baraki anayamikira “atsogoleri a asilikali a Isiraeli, amene anadzipereka mwaufulu pakati pa anthu awo.” Anthu amenewa anali ndi mtima wodzipereka kusiyana ndi “okwera abulu ofiirira,” amene anali onyada ndipo sanafune kupita nawo kunkhondo. Anthu onyadawa anangokhala ‘pansalu zokwera mtengo’ chifukwa chokonda moyo wawofuwofu. Pomwe amene anadzipereka kuti apite ndi Baraki aja analolera ‘kuyenda mumsewu’ m’dera la mapiri la Tabori komanso m’chigwa chamatope cha Kisoni. M’pake kuti anthu okonda moyo wawofuwofuwo anauzidwa kuti ‘aganizire ntchito za Mulungu.’ Iwo ankafunika kuganizira za mwayi womwe anataya wothandiza kuti cholinga cha Yehova chikwaniritsidwe. Limeneli ndi chenjezo kwa aliyense amene sakudzipereka ndi mtima wonse potumikira Mulungu.

13. Kodi anthu a fuko la Rubeni, Dani ndi Aseri anali osiyana bwanji ndi a fuko la Zebuloni ndi Nafitali?

13 Anthu amene anadzipereka n’kupita kunkhondo anali ndi mwayi woona Yehova akusonyeza mphamvu zake monga Wolamulira wa chilengedwe chonse. Iwo akanatha kufotokozera ena “ntchito zolungama za Yehova” zimene anaona. (Ower. 5:11) Lemba la Oweruza 5:15-17 limati anthu a fuko la Rubeni, Dani ndi Aseri sankaganizira za ntchito ya Yehova koma ankangoganizira za zinthu zawo monga ziweto, sitima komanso madoko. Koma a fuko la Zebuloni ndi Nafitali ‘anaika miyoyo yawo pangozi’ n’cholinga choti athandize Debora ndi Baraki. (Ower. 5:18) Tingaphunzire zambiri pa nkhani imeneyi.

“TAMANDANI YEHOVA”

14. Kodi masiku ano tingasonyeze bwanji kuti tili kumbali ya ulamuliro wa Yehova?

14 Masiku ano sitimafunika kupita kunkhondo. Koma timagwira ntchito yolalikira ndipo timafunika kukhala akhama komanso olimba mtima. Panopa m’gulu la Yehova mukufunika anthu  ambiri odzipereka. Abale ndi alongo ambiri amadzipereka kuchita utumiki wa nthawi zonse. Ena akuchita upainiya, ena akutumikira ku Beteli, ena amamanga nawo Nyumba za Ufumu ndipo ena amadzipereka kugwira ntchito zosiyanasiyana pa misonkhano ikuluikulu. Ndiye palinso akulu amene ali m’Makomiti Olankhulana ndi Achipatala komanso Makomiti a Msonkhano Wachigawo. Yehova amayamikira kwambiri mtima wawo wodzipereka ndipo sadzaiwala zonse zimene amachita.​—Aheb. 6:10.

Musanasankhe zochita, muziganizira kaye mmene zingakhudzire banja lanu komanso mpingo (Onani ndime 15)

15. Kodi tingadziwe bwanji ngati tili ndi mtima wodzipereka kwa Yehova?

15 Tonsefe tingachite bwino kudzifufuza kuti tione ngati tili ndi mtima wodzipereka. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ineyo ndimangosiyira anthu ena kuti azigwira ntchito zambiri? Kodi ndimaganizira kwambiri zopeza chuma kuposa kutumikira Yehova? Kapena kodi ndimatsanzira Baraki, Debora, Yaeli ndi anthu 10,000 amene anadzipereka aja moti ndimagwiritsa ntchito zinthu zimene ndili nazo kuti nditumikire Yehova? Ngati ndikufuna kukasaka ndalama kudziko lina, kodi ndapemphera kwa Yehova n’kuganizira mmene kuchokako kungakhudzire banja langa komanso mpingo?’ *

16. Ngakhale kuti Yehova sasowa kanthu, kodi tingamupatse chiyani?

16 Yehova watilemekeza kwambiri potipatsa mwayi wosonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wake. Kuyambira nthawi ya Adamu ndi Hava, Satana wakhala akuyesetsa kuti anthu akhale kumbali yake potsutsana ndi Yehova. Choncho tikamatumikira Yehova modzipereka timasonyeza Satana kuti tili kumbali ya Yehovayo. Yehova amasangalala tikamachita zimenezi chifukwa choti tili ndi chikhulupiriro komanso mtima wosagawanika. (Miy. 23:15, 16) Tikamamvera Yehova timathandiza kuti ayankhe Satana amene amamunyoza. (Miy. 27:11) Mwachidule tingati tikamamvera Yehova timakhala kuti tikumupatsa zinthu zamtengo wapatali ndipo amasangalala kwambiri.

17. Kodi lemba la Oweruza 5:31 limasonyeza kuti chidzachitike n’chiyani m’tsogolomu?

17 Posachedwapa, padziko lonse padzakhala anthu amene asankha ulamuliro wa Yehova. Timalakalaka kwambiri nthawi imeneyi itafika. Timamva ngati Debora ndi Baraki amene anaimba kuti: “Inu Yehova, adani anu onse afafanizidwe chimodzimodzi, ndipo okukondani inu akhale amphamvu ngati mmene dzuwa limakhalira.” (Ower. 5:31) Pemphero limeneli lidzayankhidwa Yehova akadzawononga dziko la Satanali. Nkhondo ya Aramagedo ikadzayamba, sipadzafunika anthu oti adzipereke kuti amenye nawo nkhondoyo. M’malomwake, idzakhala nthawi yoti ‘tiime chilili ndi kuona Yehova akutipulumutsa.’ (2 Mbiri 20:17) Choncho nthawi yoti tithandize pokwaniritsa cholinga cha Yehova ndi inoyo ndipo tiyenera kuchita zimenezi mwakhama komanso molimba mtima.

18. Kodi chingachitike n’chiyani ngati tili ndi mtima wodzipereka?

18 Debora ndi Baraki anayamba nyimbo yawo ndi mawu otamanda Yehova osati anthu. Iwo anati: “Chifukwa cha kudzipereka mwaufulu kwa anthu, tamandani Yehova.” (Ower. 5:1, 2) Masiku anonso timafuna kuti anthu akaona mtima wathu wodzipereka, ‘azitamanda Yehova.’

^ ndime 6 Nthawi zina, zitsulo zimenezi zinkaoneka ngati zikwakwa. N’zodziwikiratu kuti palibe amene akanayesa kuyandikira magaleta oopsawa.

^ ndime 8 Kuti muimvetse bwino nkhaniyi, werengani Nsanja ya Olonda ya August 1, 2015, tsamba 12-15.

^ ndime 15 Onani nkhani yakuti, “Kuda Nkhawa Chifukwa cha Kusowa kwa Ndalama” mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2015.