NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) April 2017

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira May 29 mpaka July 2, 2017.

“Uzikwaniritsa Zinthu Zimene Walonjeza”

Kodi munthu angalonjeze kwa Mulungu zinthu ziti? Kodi Malemba amati chiyani pa nkhani ya zinthu zimene talonjeza kwa Mulungu?

Kodi Ufumu wa Mulungu Ukadzabwera Udzachotsa Zinthu Ziti?

Baibulo limanena kuti “dziko likupita.” Kodi mawu oti “dziko” akuimira chiyani?

MBIRI YA MOYO WANGA

Ndine Msilikali wa Khristu

Demetrius Psarras anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali. Komabe anapitiriza kuthandiza kuti Mulungu atamandike ngakhale atakumana ndi mayesero oopsa.

“Woweruza wa Dziko Lonse Lapansi” Amachita Zachilungamo

N’chifukwa chiyani tinganene kuti n’zosatheka kuti Yehova achite zopanda chilungamo? Kodi mfundo imeneyi ndi yolimbikitsa bwanji kwa Akhristu masiku ano?

Kodi Mumatsanzira Yehova pa Nkhani ya Chilungamo?

N’chifukwa chiyani tinganene kuti kudzichepetsa komanso kukhululuka n’zofunika ngati tikufuna kutsanzira Yehova pa nkhani ya chilungamo?

Kudzipereka Kwathu Kumachititsa Kuti Yehova Atamandidwe

Mulungu amayamikira chilichonse chimene atumiki ake amachita pothandiza kukwaniritsa cholinga chake.