Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Aramagedo n’chiyani?

Anthu ena amakhulupirira kuti . . .

ndi nthawi imene dziko lonseli lidzawonongedwe ndi zida za nyukiliya kapena chifukwa cha kuwonongeka kwa zinthu zachilengedwe. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Zimene Baibulo limanena

Aramagedo ndi “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” Pa nkhondoyi Mulungu adzawononga anthu onse ochita zoipa.​—Chivumbulutso 16:14, 16.

Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo

  • Mulungu adzamenya nkhondo ya Aramagedo osati ndi cholinga chofuna kuwononga dziko lapansili, koma pofuna kuliteteza kuti anthu asapitirize kuliwononga.​—Chivumbulutso 11:18.

  • Nkhondo ya Aramagedo idzathetsa nkhondo zonse.​—Salimo 46:8, 9.

Kodi n’zotheka kudzapulumuka pa nkhondo ya Aramagedo?

Kodi mungayankhe bwanji?

  • Inde

  • Ayi

  • Mwina

Zimene Baibulo limanena

“Khamu lalikulu la anthu” ochokera m’mitundu yonse lidzapulumuka “chisautso chachikulu” chomwe chidzathere pa nkhondo ya Aramagedo.​—Chivumbulutso 7:9, 14.

Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo

  • Mulungu akufuna kuti anthu ambiri adzapulumuke pa Aramagedo. Iye amachenjeza kaye anthu oipa ndipo amawawononga pokhapokha ngati sanasinthe.​—Ezekieli 18:32.

  • Baibulo limafotokoza zimene tingachite kuti tidzapulumuke pa Aramagedo.​—Zefaniya 2:3.