Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE OWERENGA AMAFUNSA

Kodi Akhristu Ayenera Kukondwerera Khirisimasi?

Kodi Akhristu Ayenera Kukondwerera Khirisimasi?

Anthu ambiri padziko lonse amakhulupirira kuti Khirisimasi ndi chikondwerero chokumbukira kubadwa kwa Yesu Khristu. Koma kodi Akhristu oyambirira, omwe ankadziwana bwino ndi Yesu monga atumwi komanso ophunzira ake, ankakondwerera Khirisimasi? Nanga kodi mukudziwa zimene Baibulo limanena pa nkhani yokondwerera tsiku lobadwa? Mayankho a mafunso amenewa angatithandize kudziwa ngati zili zoyenera kuti Akhristu azikondwerera Khirisimasi kapena ayi.

Choyamba, Baibulo silinena chilichonse chokhudza tsiku lokondwerera kubadwa kwa Yesu kapena kwa mtumiki aliyense wokhulupirika wa Mulungu. M’Baibulo muli nkhani za anthu awiri okha omwe anakondwerera tsiku limene anabadwa. Anthu awiri onsewa sanali atumiki a Yehova ndipo pa tsiku lokumbukira kubadwa kwawoko, panachitika zinthu zoipa. (Genesis 40:20; Maliko 6:21) Malinga ndi zimene buku lina linanena, Akhristu ankatsutsa “mwambo wachikunja wokumbukira tsiku lobadwa.”​—Encyclopædia Britannica.

Kodi Yesu anabadwa liti?

Baibulo silitchula tsiku lenileni limene Yesu anabadwa. Buku lina linati: “Chipangano Chatsopano sichitchula tsiku limene Yesu anabadwa komanso tsikuli silipezeka m’buku lililonse.” (McClintock and Strong’s Cyclopedia) Kunena zoona, ngati Yesu akanafuna kuti otsatira ake azikondwerera tsiku lake lobadwa, akanaonetsetsa kuti iwo akudziwa bwino tsikulo.

Chachiwiri, Baibulo silinena kuti Yesu kapena wophunzira wake aliyense ankakondwerera Khirisimasi. Buku lina limanena kuti nkhani yokhudza kukondwerera Khirisimasi inatchulidwa koyamba m’buku lina la Aroma ndipo zomwe zili m’bukuli zinalembedwa m’chaka cha 336 C.E. (New Catholic Encyclopedia) Apa n’kuti Baibulo litatha kale kulembedwa komanso n’kuti patatha zaka zambiri kuchokera pamene Yesu anali padzikoli. N’chifukwa chake buku lomwe tinatchula m’ndime yachitatu lija linanenanso kuti, “Zoti anthu azichita chikondwerero cha Khirisimasi sizinachokere kwa Mulungu ndipo sizipezeka m’Chipangano Chatsopano.” *​—McClintock and Strong’s Cyclopedia.

Kodi ndi mwambo uti umene Yesu anauza ophunzira ake kuti azichita?

Monga Mphunzitsi Wamkulu, Yesu anapereka malangizo omveka bwino okhudza zimene amafuna kuti otsatira ake azichita ndipo malangizo amenewa analembedwa m’Baibulo. Koma pa malangizowa, palibe amene amanena kuti otsatira ake azikondwerera Khirisimasi. Palibe mphunzitsi amene amafuna kuti ana a m’kalasi mwake azichita zosiyana ndi zimene anawaphunzitsa. Nayenso Yesu safuna kuti ophunzira ake ‘azipitirira zinthu zolembedwa’ m’Baibulo.​—1 Akorinto 4:6.

Koma pali mwambo umodzi wofunika kwambiri umene Akhristu oyambirira ankachita. Umenewu ndi mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Yesu anauza ophunzira ake tsiku loyenera kuchita mwambowu ndiponso mmene angauchitire. Komanso m’Baibulo muli malangizo okhudza mmene mwambo umenewu uyenera kuchitikira komanso tsiku lenileni limene Yesu anafa.​—Luka 22:7, 19; 1 Akorinto 11:25.

Mu nkhaniyi taona kuti Khirisimasi ndi chikondwerero chokumbukira tsiku lobadwa, ndipo Akhristu oyambirira sankachita nawo chikondwerero cha anthu osalambira Yehova chimenechi. Taonanso kuti Baibulo silitchula kuti Yesu kapena munthu wina aliyense ankakondwerera Khirisimasi. Akhristu ambiri akaganizira mfundo zimenezi amaona kuti n’zosayenera kuti azichita Khirisimasi.

^ ndime 6 Ngati mukufuna kudziwa zambiri zokhudza mmene miyambo yomwe imachitika pa Khirisimasi inayambira, werengani nkhani yakuti, “Zimene Owerenga Amafunsa . . . Kodi ndi Zinthu Ziti Zomwe Tiyenera Kudziwa pa Nkhani ya Khirisimasi?” mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 2014. Magaziniyi ikupezekanso pawebusaiti yathu ya www.jw.org/ny.