Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Dokowe

Zimene Tingaphunzire kwa Mbalame

Zimene Tingaphunzire kwa Mbalame

“Funsa . . . zouluka zam’mlengalenga, ndipo zikuuza. Ndani pa zonsezi sadziwa bwino kuti dzanja la Yehova ndi limene lachita zimenezi?”—Yobu 12:7, 9.

ZAKA zoposa 3,000 zapitazo, Yobu anazindikira kuti pali zambiri zimene tingaphunzire kuchokera kwa mbalame. Zimene mbalame zimachita zakhala zikugwiritsidwanso ntchito monga zitsanzo kapena mafanizo. Baibulo limafotokoza zinthu zina zokhudza mbalame zimene zimatiphunzitsa mfundo zofunika zokhudza moyo komanso ubwenzi wathu ndi Mulungu. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.

MALO AMENE NAMZEZE AMAMANGA CHISA

Namzeze

Anthu okhala ku Yerusalemu ankadziwa bwino za anamzeze omwe amakonda kumanga zisa zawo kudenga la nyumba. Anamzeze ena ankamanga zisa kudenga la kachisi wa Solomo. Anamzezewa ayenera kuti ankaona kuti ndi malo amene anapiye awo angakhale motetezeka.

Mmodzi mwa ana a Kora, yemwe analemba Salimo 84, ankatumikira kukachisi mlungu umodzi pa miyezi 6 iliyonse ndipo ankaona zisa zimene anamzeze ankamanga kukachisiko. Iye ankafunitsitsa kuti akhale kunyumba ya Yehova nthawi zonse ngati mmene anamzezewa ankachitira. Iye anati: “Inu Yehova wa makamu, ine ndimakondadi chihema chanu chachikulu! Ndimalakalaka mabwalo a Yehova ndipo ndafookeratu chifukwa cholakalaka mabwalowo. Mtima wanga ndi thupi langa zikufuula mosangalala kwa Mulungu wamoyo. Inu Yehova wa makamu, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga, ngakhale mbalame zapeza malo okhala pafupi ndi guwa lanu lansembe lalikulu. Namzeze wadzimangira chisa chake pamenepo, ndi kuikamo ana ake!” (Salimo 84:1-3) Kodi nafenso limodzi ndi ana athu timasonyeza kuti ndife ofunitsitsa kukhala mumpingo wa anthu a Mulungu nthawi zonse?Salimo 26:8, 12.

DOKOWE AMADZIWA NTHAWI

Mneneri Yeremiya analemba kuti: “Dokowe, mbalame youluka m’mlengalenga, imadziwa bwino nthawi yake yoikidwiratu.” Mosakayikira Yeremiya ankadziwa kuti chaka chilichonse pa nthawi inayake, adokowe kapena kuti meza ankadutsa m’Dziko Lolonjezedwa posamukira kudziko lina. M’miyezi ya March ndi April adokowe amasamuka ku Africa kupita ku Europe ndipo amadutsa m’chigwa cha Yorodano. Mwachitsanzo, anthu ena aonapo adokowe oyera oposa 300,000 akusamuka. Adokowe amadziwa mwachibadwa nthawi yoti abwerere kumalo amene amakaikira mazira. Mofanana ndi mbalame zina zimene zimasamuka chaka chilichonse, adokowe ‘amadziwa nyengo yobwerera kumene achokera.’—Yeremiya 8:7.

Buku lina lofotokoza za mbalame limati: “Chochititsa chidwi kwambiri ndi nkhani ya kusamuka kwa mbalame n’chakuti zimangodziwa zokha mwachibadwa nthawi yake yoyenera kusamuka.” (Collins Atlas of Bird Migration) Yehova Mulungu analenga mbalame kuti zizidziwa mwachibadwa nthawi yoyenera kusamuka, pamene anthu anawalenga ndi luso lotha kuzindikira tanthauzo la zimene zikuchitika pa nthawi inayake. (Luka 12:54-56) Komabe kuti munthu azindikire tanthauzo la zinthu zimene zikuchitika m’nthawi yathuyi, ayenera kudziwa Mawu a Mulungu. Aisiraeli akale sankazindikira tanthauzo la zinthu zimene zinkachitika pa nthawiyo. Mulungu anafotokoza chifukwa chake sankazindikira  zimenezi. Iye anati: “Iwo akana mawu a Yehova. Kodi ali ndi nzeru yotani tsopano?”—Yeremiya 8:9.

Masiku ano pali umboni wokwanira wosonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza.’ (2 Timoteyo 3:1-5) Kodi inuyo mungatsatire chitsanzo cha dokowe n’kumachita zinthu zosonyeza kuti mukudziwa nthawi imene tikukhalayi?

CHIWOMBANKHANGA CHILI NDI MASO AKUTHWA

Chiwombankhanga

Baibulo limatchula chiwombankhanga maulendo ambiri ndipo mbalamezi zinkapezeka kwambiri m’Dziko Lolonjezedwa. Ziwombankhanga zimamanga zisa pamwamba kwambiri ndipo ‘zimafunafuna chakudya kuchokera pamenepo. Maso ake amaona kutali kwambiri.’ (Yobu 39:27-29) Maso a chiwombankhanga ndi akuthwa kwambiri moti chikhoza kuona kalulu ali kutali, ngakhale pa mtunda wa kilomita imodzi.

Mofanana ndi chiwombankhanga chimene ‘chimaona kutali kwambiri,’ Yehova amaona zam’tsogolo. N’chifukwa chake iye ananena kuti: “Ine ndi amene ndimanena za mapeto kuyambira pa chiyambi. Kuyambira kalekale, ndimanena za zinthu zimene sizinachitike.” (Yesaya 46:10) Tikamamvera malangizo a Yehova tikhoza kupindula ndi nzeru zake zopanda malire komanso luso lake looneratu zinthu zam’tsogolo.—Yesaya 48:17, 18.

Baibulo limayerekezera anthu amene amadalira Mulungu ndi chiwombankhanga. Limati: “Anthu odalira Yehova adzapezanso mphamvu. Iwo adzaulukira m’mwamba ngati ali ndi mapiko a chiwombankhanga.” (Yesaya 40:31) Ziwombankhanga zikamauluka, zimagwiritsa ntchito mpweya wotentha. Zikafika pamene pakuwomba mpweyawu zimafutukula mapiko ake n’kumauluka mozungulira pamwamba pa mpweyawo ndipo zimakankhidwa mpaka kupita m’mwamba kwambiri. Ziwombankhanga sizidalira mphamvu zake kuti ziuluke mtunda wautali koma zimadalira mpweya wotenthawu. Mofanana ndi zimenezi, anthu amene amadalira Yehova amadziwa kuti iye adzawapatsa “mphamvu yoposa yachibadwa.”—2 Akorinto 4:7, 8.

“MUJA NKHUKU YATHADZI IMASONKHANITSIRA ANAPIYE AKE”

Nkhuku yathadzi ndi anapiye

Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, anayang’anitsitsa mzinda wa Yerusalemu n’kunena kuti: “Yerusalemu, Yerusalemu, wakupha aneneri iwe ndi woponya miyala anthu otumizidwa kwa iwe. Mobwerezabwereza ndinafuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, muja nkhuku yathadzi imasonkhanitsira anapiye ake m’mapiko. Koma anthu inu simunafune zimenezo.”—Mateyu 23:37.

Chinthu china chochititsa chidwi ndi mbalame n’choti zinalengedwa ndi mtima wofuna kuteteza ana ake. Mbalame zomwe zimaikira mazira pansi monga nkhuku zimafunika kukhala tcheru nthawi zonse. Mwachitsanzo, nkhuku yathadzi ikaona mphamba imalira mokweza pochenjeza ana ake ndipo anawo amathawira m’mapiko ake. Mapikowa amathandizanso anapiye kuti atetezeke ku dzuwa lambiri ndiponso mvula yamphamvu. Nayenso Yesu ankafuna kuteteza anthu amumzinda wa Yerusalemu ku zinthu zimene zikanasokoneza ubwenzi wawo ndi Yehova. Masiku ano Yesu amatilimbikitsa kuti tizimutsatira n’cholinga choti tizitsitsimulidwa komanso kutetezedwa ku nkhawa zimene timakhala nazo tsiku ndi tsiku.—Mateyu 11:28, 29.

Monga taonera m’nkhaniyi, pali zinthu zambiri zomwe tingaphunzire kuchokera kwa mbalame. Mukamaona zimene zimachita muziyesetsa kukumbukira zimene Baibulo limanena zokhudza mbalamezi. Mwachitsanzo, zimene namzeze amachita zingakuthandizeni kukhala ofunitsitsa kumapezeka kunyumba yolambirira Yehova. Nkhani ya chiwombankhanga ingakuthandizeni kuti musamataye mtima koma muzidalira kwambiri Mulungu. Zimene nkhuku yathadzi imachita zingakuthandizeni kumatsatira Yesu n’kukhala otetezeka ku zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova. Komanso zimene dokowe amachita zingakukumbutseni kuti muyenera kumasonyeza kuti mukuzindikira tanthauzo la zimene zikuchitika m’nthawi yathu ino.