Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Mulungu Amayankha Mapemphero Onse?

KODI MUNGAYANKHE KUTI . . .

  • Amayankha mapemphero onse

  • Amayankha mapemphero ena

  • Sayankha

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Yehova ali pafupi ndi onse . . . amene amamuitana m’choonadi.”—Salimo 145:18.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO

  • Mulungu samvetsera mapemphero a anthu amene samumvera. (Yesaya 1:15) Komabe anthu oterewa akhoza kusintha zochita zawo n’kukhala “pa ubwenzi wabwino” ndi Mulungu.—Yesaya 1:18.

  • Kuti Mulungu aziyankha mapemphero athu, tiyenera kupemphera mogwirizana ndi mfundo zimene amatiuza m’Baibulo.—1 Yohane 5:14.

Kodi tiyenera kukhala mwanjira inayake popemphera?

ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA kuti ayenera kupemphera atagwada, atazyolika kapena ataika manja awo pamodzi. Nanga inuyo mukuganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mulungu anamvetserapo mapemphero a anthu omwe ankapemphera ‘atakhala pansi,’ ‘ataimirira’, ‘atagona’ kapenanso ‘atagwada.’ (1 Mbiri 17:16; 2 Mbiri 30:27; Ezara 10:1; Machitidwe 9:40) Choncho Mulungu safuna kuti anthu azichita kukhala mwanjira inayake akamapemphera.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO