Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUDZIWA ZAMBIRI ZOKHUDZA ANGELO?

Kodi Aliyense Ali Ndi Mngelo Amene Amamuyang’anira?

Kodi Aliyense Ali Ndi Mngelo Amene Amamuyang’anira?

Baibulo silinena kuti munthu aliyense ali ndi mngelo wake amene amamuyang’anira. N’zoona kuti Yesu anati: “Samalani anthu inu kuti musanyoze mmodzi wa tianati, [ophunzira a Yesu] chifukwa ndikukutsimikizirani kuti angelo awo kumwamba amaona nkhope ya Atate wanga wakumwamba nthawi zonse.” (Mateyu 18:10) Koma sikuti apa Yesu ankatanthauza kuti aliyense ali ndi mngelo amene amamuyang’anira. M’malomwake ankatanthauza kuti angelo amachita chidwi ndi wophunzira wa Yesu aliyense ndipo amafuna kuti zinthu zizimuyendera bwino. Choncho atumiki a Mulungu sachita dala zinthu zoika moyo pangozi poganiza kuti angelo a Mulungu awateteza.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti angelo sathandiza anthu? Ayi. (Salimo 91:11) Anthu ena amakhulupirira ndi mtima wonse kuti Mulungu amawateteza komanso amawatsogolera pogwiritsa ntchito angelo. Mmodzi wa anthu amenewa ndi a Kenneth amene tawatchula m’nkhani yoyamba ija. N’kuthekadi kuti Mulungu ndi amene anathandiza a Kenneth. Nthawi zambiri a Mboni za Yehova amaona umboni wosonyeza kuti angelo amawathandiza pa ntchito yawo yolalikira. Komabe popeza angelo saoneka, sitingafotokoze mwatsatanetsatane zonse zimene amachita pothandiza anthu m’njira zosiyanasiyana. Koma sikulakwa ngati munthu akuthokoza Yehova chifukwa choti akuona kuti wamuthandiza pogwiritsa ntchito angelo.​—Akolose 3:15; Yakobo 1:17, 18.