Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUDZIWA ZAMBIRI ZOKHUDZA ANGELO?

Kodi Angelo Angakuthandizeni?

Kodi Angelo Angakuthandizeni?

Lamlungu lina masana, a Kenneth ndi akazi awo a Filomena, omwe amakhala ku Curaçao, anapita kunyumba kwa banja lina lomwe ankaphunzira nalo Baibulo.

A Kenneth anati: “Titafika tinapeza kuti chitseko ndi chotseka ndipo panja panalibe galimoto. Koma chinachake chinangondiuza kuti ndiimbire foni amayi a kunyumbaku.”

Mayiwa anayankhadi foniyo ndipo anati amuna awo ali kuntchito. Koma atazindikira kuti awaimbirawo ndi a Kenneth, anatuluka n’kuwauza kuti alowe m’nyumba.

A Kenneth ndi akazi awo atalowa m’nyumbamo anazindikira kuti mayiwo amalira. A Kenneth atayamba kupemphera kuti phunziro liyambike, mayi aja anayambiranso kulira. Choncho iwo ndi akazi awo anawafunsa mokoma mtima kuti afotokoze vuto lawo.

Mayiwo anafotokoza kuti anali ndi matenda a nkhawa ndipo ankafuna kudzipha. Pa nthawi imene amawaimbira foniyo, n’kuti akulemba kalata yoti asiyire amuna awo. A Kenneth ndi akazi awo anakambirana ndi mayiwa mfundo zolimbikitsa za m’Baibulo. Zimene anakambiranazo zinathandiza kuti mayiwa asinthe maganizo.

A Kenneth anati: “Tinathokoza Yehova * potilola kuti tithandize mayiwa, amene anali atasokonezeka maganizo. Yehova ayenera kuti anagwiritsa ntchito angelo kapena mzimu woyera kutilimbikitsa kuti tiwaimbire foni.”

Monga taonera, a Kenneth ndi a Filomena amakhulupirira kuti Mulungu anagwiritsa ntchito angelo kapena mzimu woyera powathandiza kuti akumane ndi mayiyu. Kodi zimenezi ndi zoona? Kapena kodi zinangochitika mwamwayi kuti anaimba foni pa nthawi imene mayiyo ankafuna kudzipha?

Sitinganene motsimikiza. Koma zimene tikudziwa ndi zoti nthawi zina Mulungu amagwiritsa ntchito angelo kuti athandize anthu. Mwachitsanzo, Baibulo limati Mulungu anagwiritsa ntchito angelo pothandiza nduna ya ku Itiyopiya imene inkafuna munthu woti aithandize kumvetsa Malemba.​—Machitidwe 8:26-31.

Anthu a m’zipembedzo zambiri amakhulupirira kuti pali angelo amene amachitira anthu zinthu zina mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Amakhulupiriranso kuti munthu aliyense ali ndi mngelo amene amamuteteza komanso kumuthandiza. Komabe palinso anthu ena amene sakhulupirira n’komwe zoti kuli angelo.

Kodi angelo alipodi? Ngati alipo, kodi anachokera kuti? Kodi ndi zinthu ziti zimene muyenera kudziwa zokhudza angelo? Nanga kodi angelo angakuthandizeni? Nkhani zotsatira zikuyankha mafunso amenewa.

^ ndime 8 Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.​—Salimo 83:18.