Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUDZIWA ZAMBIRI ZOKHUDZA ANGELO?

Kodi Pali Angelo Ena Oipa?

Kodi Pali Angelo Ena Oipa?

Inde alipo. Koma kodi anachokera kuti? Paja Mulungu anapatsa angelo ufulu wosankha zochita. Komabe pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Adamu ndi Hava analengedwa, mngelo wina anagwiritsa ntchito molakwika ufulu wake wosankha ndipo anachititsa Adamu ndi Hava kuti asamvere Mulungu. (Genesis 3:1-7; Chivumbulutso 12:9) Baibulo silifotokoza udindo umene mngelo ameneyu anali nawo komanso dzina limene ankadziwika nalo asanachimwe. Koma atasiya kumvera Mulungu, Baibulo linayamba kumutchula kuti Satana, kutanthauza “Wotsutsa” komanso Mdyerekezi, kutanthauza “Woneneza.”​—Mateyu 4:8-11.

N’zomvetsa chisoni kuti patapita nthawi angelo enanso sanamvere Mulungu. M’nthawi ya Nowa angelo ena “anasiya malo awo okhala” kumwamba. Angelowa anabwera padziko lapansi n’kuvala matupi a anthu ndipo anayamba kuchita zinthu zoipa kwambiri zosagwirizana ndi mmene Mulungu anawalengera.​—Yuda 6; Genesis 6:1-4; 1 Petulo 3:19, 20.

Kenako Mulungu anabweretsa Chigumula padziko lonse lapansi. Ndiyeno angelo oipawa anavula matupi a anthu aja n’kubwereranso kumwamba. Koma Mulungu sanawalole kuti abwererenso ‘kumalo awo oyambirira.’ M’malomwake anawaika “mu mdima [wauzimu] wandiweyani” womwe umatchedwa Tatalasi. (Yuda 6; 2 Petulo 2:4) Angelo amenewa amatchedwa ziwanda ndipo tingati analola kuti azitsogoleredwa ndi Satana Mdyerekezi yemwe “amadzisandutsa mngelo wa kuwala” komanso ndi ‘wolamulira wa ziwanda.’​—Mateyu 12:24; 2 Akorinto 11:14.

Baibulo limaphunzitsa kuti Ufumu wa Mulungu, womwe wolamulira wake ndi Mesiya, ndi boma lakumwamba ndipo unakhazikitsidwa mu 1914. * Ufumu umenewu utangokhazikitsidwa, Satana ndi ziwanda zake anathamangitsidwa kumwamba n’kuwaponyera padziko lapansi. Chifukwa choti iwo ndi okwiya, akuchititsa kuti anthu azichita makhalidwe oipa kwambiri komanso kuti padzikoli pazichitika mavuto osiyanasiyana.​—Chivumbulutso 12:9-12.

Mavuto komanso zinthu zoipa kwambiri zimene zikuchitika padzikoli, ndi umboni wakuti posachedwapa Satana ndi ziwanda zake sakhalanso ndi mphamvu zoyambitsa mavuto. Ufumu wa Mulungu ukadzalamulira kwa zaka 1,000 padzikoli, angelo oipawa adzapatsidwanso mwayi woti ayese anthu komaliza. Kenako Satana ndi ziwanda zake adzawonongedwa ndipo sadzakhalakonso mpaka kalekale.​—Mateyu 25:41; Chivumbulutso 20:1-3, 7-10.

^ ndime 6 Kuti mudziwe zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu, werengani mutu 8 m’buku lakuti, Zimene Baibulo Limaphunzitsa. Bukuli limafalitsidwa ndi a Mboni za Yehova ndipo likupezekanso pawebusaiti ya www.jw.org/ny.