Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NSANJA YA OLONDA Na. 5 2017 | N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kudziwa Zambiri Zokhudza Angelo?

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

Kodi angelo alipodi? Baibulo limati:

“Tamandani Yehova, inu angelo ake amphamvu, ochita zimene wanena, mwa kumvera malamulo ake.”​Salimo 103:20.

Magaziniyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani ya angelo komanso mmene angatithandizire.

 

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Angelo Angakuthandizeni?

Zimene zinachitikira anthu ena zimachititsa anthu ambiri kukhulupirira kuti angelo amathandiza anthu.

NKHANI YAPACHIKUTO

Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Angelo

Palibe kwina komwe tingapeze mayankho olondola a mafunso okhudza angelo kuposa m’Baibulo.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Aliyense Ali Ndi Mngelo Amene Amamuyang’anira?

Kodi ndi bwino kuganiza kuti pali mngelo kapena angelo amene angakutetezeni?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Pali Angelo Ena Oipa?

Baibulo limayankha funso limeneli momveka bwino.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Angelo Angakuthandizeni Bwanji?

Maulendo angapo, Mulungu ankatumiza angelo ake kuti adzathandize atumiki ake padziko lapansi.

Kodi Mukudziwa?

Kodi zimene Yesu ananena zokhudza “tiagalu” zinali zonyoza?

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinkaona Kuti Kulibe Mulungu

Kodi zinatheka bwanji kuti munthu amene kuyambira ali mwana ankatsatira mfundo zachikomyunizimu komanso mfundo yoti kulibe Mulungu, asinthe n’kuyamba kuphunzira Baibulo?

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO

Yehova Anamutchula Kuti “Mfumukazi”

N’chifukwa chiyani dzina latsopanoli linali lomuyenera?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Masiku ano zimaoneka ngati n’zosatheka kukhala ndi mtendere padzikoli komanso kukhala ndi mtendere wamumtima chifukwa zinthu zoipa komanso zopanda chilungamo zikuchitika paliponse. Kodi n’zotheka padzikoli kudzakhala mtendere?

Zina zimene zili pawebusaiti