NSANJA YA OLONDA Na. 5 2016 | Kodi Ndi Ndani Angatithandize Tikakhala pa Mavuto?

Tonsefe timafunika kulimbikitsidwa makamaka tikakumana ndi mavuto. Nkhanizi zikufotokoza zimene Mulungu amachita potilimbikitsa.

NKHANI YAPACHIKUTO

Tonse Timafunika Kulimbikitsidwa

Kodi ndi ndani amene angatithandize tikaferedwa, tikadwala, tikakumana ndi mavuto a m’banja kapena tikasowa ntchito?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mulungu Amatilimbikitsa Bwanji?

Zinthu 4 zimene zingathandize anthu amene akukumana ndi mavuto.

NKHANI YAPACHIKUTO

Zimene Zingakuthandizeni Mukamakumana ndi Mavuto

Nkhaniyi ikusonyeza mmene anthu ena anathandizidwira atakumana ndi mavuto.

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO

“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”

N’chiyani chinathandiza Davide kuti aphe Goliyati? Kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhani ya Davide?

Nkhani ya Davide ndi Goliyati—Kodi Inachitikadi?

Anthu ena amakayikira zoti nkhani ya Davide ndi Goliyati inachitikadi. Kodi pali umboni wotithandiza kudziwa zoona zake?

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinali Mnyamata Wovuta Komanso Wokonda Ndewu

Kodi n’chiyani chinathandiza munthu wokonda ndewu wa ku Mexico kuti asinthe?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Yankho lake likhoza kukudabwitsani.

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Mulungu Angayankhe Mapemphero Anga?

Kuti Mulungu ayankhe mapemphero anu zimadalira kwambiri pa zimene inuyo mumachita.