Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mu Ufumu wa Mulungu, anthu “adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”​—Salimo 37:11

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Baibulo lingakuthandizeni mukakhala ndi nkhawa?

Kodi mungayankhe bwanji?

  • Inde

  • Ayi

  • Mwina

Zimene Baibulo limanena

‘Muzimutulira [Mulungu] nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’ (1 Petulo 5:7) Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu angatithandize tikakhala ndi nkhawa.

Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo

  • Mukapemphera, mungapeze “mtendere wa Mulungu” womwe ungakuthandizeni kuchepetsa nkhawa.​—Afilipi 4:6, 7.

  • Kuwerenga Mawu a Mulungu kungakuthandizeni kuti mudziwe zoyenera kuchita mukakhala ndi nkhawa.​—Mateyu 11:28-30.

Kodi zidzatheka anthufe kukhala opanda nkhawa?

Anthu ena amakhulupirira kuti . . . nkhawa ndi mbali imodzi ya moyo wa munthu, pomwe ena amakhulupirira kuti nkhawa zidzatha akadzamwalira n’kupita kumwamba. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Zimene Baibulo limanena

Mulungu analonjeza kuti adzachotsa zinthu zonse zomwe zimayambitsa nkhawa.​—Chivumbulutso 21:4.

Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo