Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Mudzakhale Ndi Moyo Wabwino Kuposa Umene Tili Nawo Panopa?

Kodi Mungatani Kuti Mudzakhale Ndi Moyo Wabwino Kuposa Umene Tili Nawo Panopa?

MOYO umene tikukhala panopa si womwe Mulungu ankafuna poyamba. Ankafuna kuti padzikoli pakhale anthu amene amafuna kuti iye aziwalamulira, azitsatira malangizo ake komanso azitsanzira makhalidwe ake. Ankafunanso kuti anthuwo azikhala mogwirizana komanso mosangalala akamabereka ana, kuphunzira zinthu zosiyanasiyana komanso kukonza dzikoli kuti likhale paradaiso.

MULUNGU AKULONJEZA KUTI ADZASINTHA ZINTHU PADZIKOLI KUTI ZIKHALE MMENE ANKAFUNIRA

  • “Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”​Salimo 46:9.

  • “Inafikanso nthawi . . . yowononga amene akuwononga dziko lapansi.”Chivumbulutso 11:18.

  • “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”Yesaya 33:24.

  • “Anthu anga osankhidwa mwapadera adzapindula mokwanira ndi ntchito ya manja awo.”​Yesaya 65:22.

Kodi malonjezo amenewa adzakwaniritsidwa bwanji? Mulungu anasankha Mwana wake, Yesu, kuti akhale wolamulira wa boma lakumwamba lomwe lidzalamulire padziko lapansi. Baibulo limanena kuti boma limeneli ndi Ufumu wa Mulungu. (Danieli 2:44) Ponena za Yesu, Baibulo limati: “Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu . . . Iye adzalamulira monga mfumu.”​—Luka 1:32, 33.

Yesu ali padzikoli, anachita zozizwitsa zambiri posonyeza kuti akamadzalamulira adzathandiza anthu kuti akhale ndi moyo wabwino, wosiyana kwambiri ndi wa masiku ano.

YESU ANASONYEZA MMENE ADZATHANDIZIRE ANTHU OMVERA

  • Ankachiritsa matenda alionse posonyeza kuti adzathetsa matenda onse.Mateyu 9:35.

  • Anakhalitsa bata nyanja posonyeza kuti ali ndi mphamvu zoletsa ngozi za m’chilengedwe.​Maliko 4:36-39.

  • Anadyetsa anthu masauzande ambiri posonyeza kuti azidzathandiza anthu kupeza zofunika pa moyo.Maliko 6:41-44.

  • Pa ukwati wina anasandutsa madzi kukhala vinyo, posonyeza kuti adzathandiza anthu kuti azisangalala ndi moyo.​Yohane 2:7-11.

Kodi mungatani kuti mudzakhale ndi moyo umene Mulungu wakonzera anthu amene amamukonda? Pali “msewu” umene muyenera kuyendamo. Baibulo limanena kuti umenewu ndi ‘msewu wopita kumoyo wosatha ndipo amene akuupeza ndi owerengeka.’​—Mateyu 7:14.

MMENE MUNGAPEZERE MSEWU WOPITA KU MOYO WOSATHA

Kodi msewu wopita ku moyo wosatha ndi chiyani? Mulungu amatiuza kuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakuchititsani  kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo.” (Yesaya 48:17) Kuyenda m’njira imene Mulungu akutiuza kungatithandize kuti tikhale ndi moyo wabwino kwambiri.

Nayenso Yesu ananena kuti: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo.” (Yohane 14:6) Kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu komanso kuti tikhale ndi moyo wabwino kwambiri, tiyenera kukhulupirira zimene Yesu anaphunzitsa komanso kumutsanzira.

Kodi mungapeze bwanji msewu wopita ku moyo wosatha? Padzikoli pali zipembedzo zambiri. Koma Yesu anachenjeza kuti: “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita chifuniro cha Atate wanga wakumwamba.” (Mateyu 7:21) Ananenanso kuti: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo.” (Mateyu 7:16) Baibulo lingakuthandizeni kuzindikira chipembedzo choona.​—Yohane 17:17.

Kodi mungatani kuti muyambe kuyenda pa msewu wopita ku moyo wosatha? Muyenera kudziwa zambiri zokhudza amene anatipatsa moyo. Muyenera kudziwa dzina lake, makhalidwe ake, zimene akutichitira panopa komanso zimene amafuna kuti tizichita. *

Sikuti Mulungu amafuna kuti anthu azingogwira ntchito, kudya, kuchita zosangalatsa kapenanso kubereka ana. Amafunanso kuti timudziwe ndiponso tikhale naye pa ubwenzi. Komanso tingasonyeze kuti timamukonda pomachita zimene amafuna. Yesu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona.”​—Yohane 17:3.

KUDZERA M’BAIBULO MULUNGU AMATIPHUNZITSA ‘KUTI ZINTHU ZITIYENDERE BWINO.’​—YESAYA 48:17

YAMBANI KUYENDA PA MSEWU WOPITA KU MOYO WOSATHA

Kuti tizisangalatsa Mulungu woona, tingafunike kusiya makhalidwe ena amene tinkachita poyamba. Mwina zimenezi zingaoneke zovuta. Koma zoona ndi zoti munthu akachita zimenezi amakhala ndi moyo wosangalala ndipo amasonyeza kuti wayamba kuyenda pa msewu wopita ku moyo. Pofuna kukuthandizani kupeza mayankho a mafunso okhudza Mulungu, a Mboni za Yehova akhoza kumaphunzira nanu Baibulo kwaulere pa nthawi ndi malo amene mungakonde. Tilembereni kudzera pa webusaiti yathu ya www.jw.org/ny.