Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tikufunikira Dziko Labwino

Tikufunikira Dziko Labwino

A António Guterres omwe ndi mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations ananena kuti: “Tikukhala m’dziko lodzaza ndi mavuto.” Kodi inunso mukuona choncho?

Nkhani zimene timamvetsera, kuonera ndi kuwerenga, zimakhala ndi zinthu zambiri zodetsa nkhawa monga:

 • Matenda ndi miliri

 • Ngozi za m’chilengedwe

 • Umphawi ndi njala

 • Kuonongeka kwa mpweya ndi madzi komanso kutentha kwa dziko

 • Kuphwanya malamulo, zachiwawa ndiponso zachinyengo

 • Nkhondo

Mpake kuti tikufunikira dziko labwino. Dziko limene mudzakhale

 • Anthu athanzi labwino

 • Chitetezo

 • Chakudya chokwanira

 • Mpweya ndi madzi abwino

 • Chilungamo chenicheni

 • Mtendere wochuluka

Kodi tikamanena kuti dziko labwino tikutanthauza chiyani?

Kodi n’chiyani chimene chidzachitikire dziko limene tikukhalamoli?

Kodi tingatani kuti tidzakhale m’dziko labwino?

Magaziniyi ifotokoza mayankho otonthoza ochokera m’Baibulo a mafunso amenewa ndi enanso.