Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pamene Mulungu ankalamulira, zolengedwa zonse zinkakhala mogwirizana komanso mwamtendere

N’chifukwa Chiyani Tikufunikira Ufumu wa Mulungu?

N’chifukwa Chiyani Tikufunikira Ufumu wa Mulungu?

Anthu oyambirira atalengedwa, Yehova yekha, yemwe ndi Mlengi wathu, ndi amene anali Wolamulira. Iye ankalamulira mwachikondi. Anakonza munda wokongola kwambiri ku Edeni kuti anthu azikhalamo ndipo anawapatsa chakudya chochuluka. Kuwonjezera pamenepa, anawapatsanso ntchito yoti azisangalala nayo. (Genesis 1:28, 29; 2:8, 15) Zikanakhala kuti Mulungu ndi amene akulamulirabe, anthu akanapitiriza kukhala mwamtendere.

Anthu oyambirira anakana kuti Mulungu akhale Wolamulira wawo

Baibulo limanena kuti mngelo wina wopanduka, yemwe anadzapatsidwa dzina loti Satana Mdyerekezi, ananena kuti Mulungu alibe ufulu wolamulira anthu. Apa anasonyeza kuti anthu akhoza kumakhala osangalala popanda kulamuliridwa ndi Mulungu. N’zomvetsa chisoni kuti mofanana ndi Satana, nawonso makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava, anapandukira Mulungu.​—Genesis 3:1-6; Chivumbulutso 12:9.

Popeza kuti Adamu ndi Hava anakana kuti Mulungu aziwalamulira, anataya mwayi wokhala m’munda wokongola uja komanso chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha ndiponso wangwiro. (Genesis 3:17-19) Zimene anasankhazi zinakhudzanso ana omwe anadzabereka. Baibulo limanena kuti popeza Adamu anachimwa, ‘uchimo unalowa m’dziko ndipo imfa kudzera mwa uchimo.’ (Aroma 5:12) Uchimo unabweretsanso vuto lina ili: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) Mfundo yake ndi yakuti anthu akamadzilamulira okha, pamakhala mavuto ambirimbiri.

MMENE ULAMULIRO WA ANTHU UNAYAMBIRA

Nimurodi anapandukira Yehova

Baibulo limanena kuti Nimurodi ndi amene anali woyamba kukhala wolamulira padzikoli. Iye anapandukira ulamuliro wa Yehova. Kuchokera nthawi imeneyo, olamulira amphamvu akhala akugwiritsa ntchito udindo wawo molakwika. Zaka pafupifupi 3,000 zapitazo, Mfumu Solomo analemba kuti: “Ndinaona misozi ya anthu amene akuponderezedwa, koma panalibe wowatonthoza. M’manja mwa oponderezawo munali mphamvu.”​—Mlaliki 4:1.

Zinthu sizinasinthebe mpaka pano. Mu 2009, bungwe la United Nations linatulutsa chikalata chomwe chinanena kuti ulamuliro wopondereza ndi “chimodzi mwa zinthu zomwe zikubweretsa mavuto ambirimbiri padzikoli.”

NTHAWI YOTI MULUNGU AKONZE ZINTHU

Dzikoli likufunikira olamulira abwino komanso boma labwino. Zimenezi n’zomwe Mlengi wathu watilonjeza.

Ngakhale maboma amene amaoneka kuti ndi abwino kwambiri alephera kuthetsa mavuto a anthu

Mulungu wakhazikitsa Ufumu kapena kuti boma. Ufumuwo udzalowa m’malo mwa maulamuliro onse a anthu “ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.” (Danieli 2:44) Ufumu umenewu ndi womwe anthu ambiri akhala akuupempherera. (Mateyu 6:9, 10) Mulungu si amene adzalamulire bomali koma wasankha wina, amene pa nthawi ina anakhalako munthu, kuti adzakhale Wolamulira. Ndiye kodi wasankha ndani?