Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mukamaona Kuti Simungathenso Kupirira

Mukamaona Kuti Simungathenso Kupirira

MOYO umakoma zinthu zonse zikamayenda bwino. Koma bwanji ngati titakumana ndi mavuto amene tikuona kuti sitingathe kuwapirira?

Mwachitsanzo, ku United States kutawomba mphepo yamkuntho, katundu wambiri wa Sally * anawonongeka. Iye anati: “Ndinasowa mtengo wogwira, moti ndinkaona kuti sindingathenso kupirira.”

Vuto lina lingakhale imfa ya munthu amene timam’konda. Janice yemwe amakhala ku Australia anati: “Ana anga aamuna awiri atamwalira, ndinamva ululu woopsa mumtima mwanga. Ndinapemphera kwa Mulungu kuti: ‘Chonde, sindithanso kupirira. Ndiloleni ndingofa chifukwa sindikufunanso kukhala ndi moyo.’”

Nayenso Daniel anasokonezeka maganizo atazindikira kuti mkazi wake wachita chigololo. Iye anati: “Mkazi wanga atavomera kuti anachitadi zimenezi, zinangokhala ngati ndabayidwa ndi mpeni mumtimamu. Kwa miyezi ingapo ndinkamvabe ululu umenewu.”

Nsanja ya Olonda ino ifotokoza zimene zingatithandize kupirira

Choyamba, tiyeni tione zimene zingatithandize pakachitika ngozi zadzidzidzi.

^ ndime 3 Munkhanizi mayina ena asinthidwa.