NSANJA YA OLONDA Na. 2 2019 | Kodi Mukuona Kuti Palibenso Chifukwa Chokhalira ndi Moyo?
Kodi mavuto aakulu amene mwakumana nawo akukuchititsani kuganiza kuti palibenso chifukwa chokhalira ndi moyo?
Mukamaona Kuti Simungathenso Kupirira
Ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto, pali chifukwa chokhalira ndi moyo.
Pakachitika Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi
M’Baibulo muli malangizo amene angakuthandizeni kupirira mukakumana ndi ngozi zogwa mwadzidzidzi.
Munthu Amene Mumamukonda Akamwalira
Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zinthu 5 zimene mungachite kuti muthe kupirira imfa ya munthu amene munkamukonda.
Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Akakhala Wosakhulupirika
Anthu ambiri amene mwamuna kapena mkazi wawo anachita zosakhulupirika anaona kuti Baibulo linawathandiza kupirira.
Ngati Mukudwala Matenda Aakulu
Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene zathandiza ena kupirira matenda aakulu.
Ngati Mukuona Kuti Bola Kungofa
Kodi munayamba mwavutikapo maganizo kwambiri mpaka kufika poganiza zongodzipha? Kodi n’chiyani chingakuthandizeni?
Musamaone Kuti Palibe Chifukwa Chokhalira ndi Moyo
Ngakhale kuti ena sangamvetse mmene mukuvutikira, musamakayikire kuti Mulungu amakuderani nkhawa ndipo akufuna kukuthandizani.
“Amakuderani Nkhawa”
Mavesi a m’Baibulo amenewa angakuthandizeni.