Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsogolo Lanu Lili M’manja Mwanu

Tsogolo Lanu Lili M’manja Mwanu

KODI N’ZOTHEKA KUPANGA ZOSANKHA ZOKHUDZA TSOGOLO LATHU? Anthu ambiri amakhulupirira kuti Mulungu analemberatu tsogolo lawo moti palibe chimene angachite kuti alisinthe. Akalephera kukwaniritsa cholinga china chake amangogwa ulesi n’kumanena kuti, ‘Sikunalembedwe.’

Ena amataya mtima akaona kuti palibe zimene angachite m’dzikoli akamaponderezedwa komanso anthu ena akamawachitira zinthu zopanda chilungamo. Amayesetsa kuti akhale ndi moyo wabwino koma amalephera chifukwa cha zinthu monga nkhondo, kuphwanya malamulo, ngozi zadzidzidzi kapenanso matenda. Kenako amangoti, ‘Ndikudzivutitsiranji ine.’

N’zoona kuti mavuto ena angatilepheretse kukwaniritsa zolinga zathu. (Mlaliki 9:11) Komabe, n’zotheka kudzakwaniritsa cholinga chathu chachikulu chomwe ndi kudzakhala ndi moyo wosatha m’tsogolo. Baibulo limasonyeza kuti zimene tingasankhe panopo n’zimene zingachititse kuti tidzapeze moyo umenewu. Tiyeni tione zimene limanena.

Aisiraeli atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, Mose yemwe anali m’tsogoleri wawo anawauza mawu ochokera kwa Mulungu akuti: “Ndaika moyo ndi imfa, dalitso ndi temberero pamaso panu. . . . Choncho inuyo ndi mbadwa zanu musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo. Musankhe moyo mwa kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake ndi kum’mamatira.”​Deuteronomo 30:15, 19, 20.

‘Ndaika moyo ndi imfa, dalitso ndi temberero pamaso panu. . . . Choncho inuyo musankhe moyo.’​Deuteronomo 30:19

Mulungu anapulumutsa Aisiraeli ndi kuwachotsa kuukapolo ku Iguputo n’cholinga choti akakhale mwaufulu komanso mosangalala m’Dziko Lolonjezedwa. Komatu kuti alandire madalitso amenewa anayenera ‘kusankha moyo.’ Kodi akanachita bwanji zimenezi? ‘Mwa kukonda Yehova Mulungu, kumvera mawu ake ndi kum’mamatira.’

Nafenso masiku ano timafunika kusankha ndipo zimene tingasankhezo zingakhudze tsogolo lathu. Tikamakonda Mulungu, kumvera mawu ake ndi kum’mamatira, timakhala tikusankha kuti tidzakhale ndi moyo wosatha m’paradaiso. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

SANKHANI KUKONDA MULUNGU

Khalidwe lalikulu la Mulungu ndi chikondi. Mtumwi Yohane analemba kuti, “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) N’chifukwa chake munthu wina atafunsa Yesu kuti lamulo lalikulu kwambiri ndi liti, iye anayankha kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mateyu 22:37) Chimene chingathandize kuti munthu akhale paubwenzi ndi Yehova Mulungu ndi chikondi osati mantha kapena kumumvera m’chimbulimbuli. Komano n’chifukwa chiyani tiyenera kusankha kukonda Mulungu?

Yehova amakonda anthu mofanana ndi mmene makolo amakondera ana awo. Ngakhale kuti ndi ochimwa, makolo amalangiza, kulimbikitsa, kuthandiza komanso amapereka chilango kwa ana awo chifukwa choti amawafunira zabwino. Kodi makolo amayembekezera zotani kwa ana awo? Iwo amafuna kuti anawo aziwakonda. Amafunanso kuti azimvera malangizo amene amawapatsa kuti zinthu ziwayendere bwino. Kodi si zomveka kuti Atate wathu wakumwamba amafunanso kuti anthufe tizimukonda posonyeza kuyamikira zimene amatichitira?

 MUZIMVERA MAWU AKE

M’chinenero chimene anagwiritsa ntchito polemba Baibulo, mawu akuti “kumvera” amatanthauzanso “kutsatira.” Izi ndi zimenenso anthu amatanthauza akamauza mwana kuti, “Uzimvera makolo ako.” Choncho kuti tisonyeze kuti timamvera Mulungu tiyenera kuphunzira komanso kutsatira zimene amanena. Popeza kuti sitingamve Mulungu akutilankhula mwachindunji, tingamumvere tikamawerenga komanso kutsatira mfundo za m’Mawu ake Baibulo.​—1 Yohane 5:3.

Pofuna kusonyeza kufunika komvera Mulungu, Yesu anati: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mateyu 4:4) Mofanana ndi chakudya chomwe ndi chofunika m’thupi lathu, Mawu a Mulungu ndi ofunikanso kwambiri kwa anthufe. N’chifukwa chiyani tikutero? Mfumu yanzeru Solomo inafotokoza kuti: “Nzeru zimateteza monga mmene ndalama zimatetezera, koma ubwino wa kudziwa zinthu ndi wakuti nzeru zimasunga moyo wa eni nzeruzo.” (Mlaliki 7:12) Kudziwa zinthu komanso nzeru zochokera kwa Mulungu zingatiteteze ndiponso kutithandiza kuti tizisankha zinthu zoyenera zomwe zingachititse kuti tidzapeze moyo wosatha m’tsogolo.

MUZIM’MAMATIRA

Taganizirani fanizo la Yesu lomwe tinakambirana m’nkhani yapita ija. Iye anati: “Chipata cholowera ku moyo n’chopapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi owerengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Pamene tikuyenda pamsewu umenewu zinthu zingatiyendere bwino ngati titamayenda pafupi ndi munthu amene akuwadziwa bwino malowo n’cholinga choti tikafike kumene tikupita, komwe ndi kumoyo wosatha. Choncho pali zifukwa zomveka zom’mamatira Mulungu. (Salimo 16:8) Koma kodi tingachite bwanji zimenezi?

Pali zinthu zambiri zimene anthufe timachita tsiku lililonse ndipo zina mwa zinthu zimenezi zingachititse kuti tikhale otanganidwa kwambiri n’kulephera kuchita zimene Mulungu amafuna. N’chifukwa chake Baibulo limatikumbutsa kuti: “Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru. Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu chifukwa masikuwa ndi oipa.” (Aefeso 5:15, 16) Tingasonyeze kuti tikumamatira Mulungu ngati timaona kuti kukhala naye paubwenzi ndi chinthu chofunika kwambiri.​—Mateyu 6:33.

UFULU WOSANKHA ULI M’MANJA MWANU

Ngakhale kuti palibe zimene tingachite kuti tisinthe kale lathu, pali zambiri zomwe tingachite n’cholinga choti ifeyo komanso anthu amene timawakonda tikhale ndi tsogolo labwino. Baibulo limatitsimikizira kuti Atate wathu wakumwamba Yehova, amatikonda kwambiri ndipo amatiuza zimene amafuna kuti tizichita kuti zinthu zitiyendere bwino. Taonani zimene mneneri Mika analemba:

“Iwe munthu wochokera kufumbi, iye anakuuza zimene zili zabwino. Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo, ukhale wokoma mtima ndiponso uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.”​Mika 6:8.

Kodi ndinu wokonzeka kuyenda ndi Mulungu n’cholinga choti mudzalandire madalitso amene adzapereke kwa anthu omwe asankha kuyenda naye? Ufulu wosankha uli m’manja mwanu.