Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Anthu Ofatsa Adzalandira Dziko Lapansi”

“Anthu Ofatsa Adzalandira Dziko Lapansi”

Ambirife taonapo anthu akupotoza chilungamo komanso osalakwa akuponderezedwa ndi anthu oipa. Kodi idzafika nthawi pamene sikudzakhalanso zoipa ndiponso zinthu zopanda chilungamo?

Baibulo pa Salimo 37 limapereka yankho la funsoli komanso malangizo omwe angatithandize. Taonaninso mmene Salimoli limayankhira mafunso ofunika kwambiri awa:

  • Kodi tizitani anthu ena akamatizunza?​Vesi 1, 2.

  • Kodi n’chiyani chidzachitikire anthu oipa?​Vesi 10.

  • Kodi anthu amene amachita zabwino ali ndi tsogolo lotani?​Vesi 1129.

  • Kodi tiyenera kuchita chiyani panopa?​Vesi 34.

Mfundo zimene zimapezeka mu Salimo 37 zimafotokoza momveka bwino zokhudza tsogolo labwino la anthu omwe ‘amayembekezera Yehova, ndi kusunga njira zake.’ A Mboni za Yehova angasangalale kwambiri kukuthandizani kuti muphunzire Baibulo komanso kuti mudziwe zimene mungachite kuti inuyo komanso anthu amene mumawakonda, mudzalandire madalitso amene Mulungu walonjeza.